Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu
OCTOBER 2-8
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | DANIELI 7-9
it-2 902 ¶2
Milungu 70
Kuphwanya malamulo komanso machimo zinathetsedwa. Yesu anaphedwa n’kuukitsidwa ndipo kenako anapita kumwamba. Izi zinachititsa kuti ‘athetse kuphwanya malamulo, machimo komanso aphimbe cholakwa.’ (Dan. 9:24) Pangano la Chilamulo linkasonyeza kuti Ayuda anali ochimwa ndiponso otembereredwa chifukwa choti anaphwanya pangano. Chilamulocho chinavumbula kuti pamene uchimo “unawonjezeka,” chifundo cha Mulungu chinawonjezerekanso kudzera mwa Mesiya. (Aroma 5:20) Popeza kuti Mesiya anapereka nsembe, anthu amene alapa amakhululukidwa machimo awo ndipo sadzalangidwa chifukwa cha machimowo.
it-2 900 ¶7
Milungu 70
Mesiya Anafika Patadutsa ‘Milungu 69.’ “Milungu 62” (Dan. 9:25) imene ndi mbali ya milungu 70, inayamba patadutsa “milungu 7.” Choncho ‘kuchokera pamene mawu anamveka’ akuti Yerusalemu akonzedwenso kudzafika pamene “Mesiya Mtsogoleri” anaonekera, panadutsa “milungu” 7 komanso “milungu” 62 kapena kuti “milungu” 69. Zimenezi ndi zaka 483 zoyambira mu 455 B.C.E. mpaka mu 29 C.E. M’chaka cha 29 C.E., Yesu anabatizidwa ndipo anadzozedwa ndi mzimu woyera n’kuyamba utumiki wake monga “Mesiya Mtsogoleri.”—Luka 3:1, 2, 21, 22.
it-2 901 ¶2
Milungu 70
‘Anaphedwa’ pakatikati pa mlungu. Mngelo Gabirieli anauuza Danieli kuti: “Pambuyo pa milungu 62 imeneyi, Mesiya adzaphedwa ndipo sadzasiya kalikonse.” (Dan. 9:26) Kumapeto kwa ‘milungu 7 komanso milungu 62’ zomwe ndi zaka zitatu ndi hafu, Khristu anaphedwa pamtengo wozunzikirapo ndipo anapereka moyo wake monga dipo lowombola anthu onse. (Yes. 53:8) Ndipotu pali umboni wosonyeza kuti hafu ya “mlungu” woyambirira, Yesu anali akulalikira. Pa nthawi ina cha m’ma 32 C.E., Yesu anapereka fanizo lonena za mtundu wa Ayuda kuti unali ngati mtengo wa mkuyu (yerekezerani ndi Mat. 17:15-20; 21:18, 19, 43) womwe sunabereke zipatso kwa “zaka zitatu.” Wosamalira munda anauza mwini munda kuti: “Mbuyanga, bwanji muusiye chaka chino chokha. Ine ndikumba mouzungulira n’kuthirapo manyowa. Ukadzabala zipatso m’tsogolo, zidzakhala bwino, koma ngati sudzabala mudzaudule.” (Luka 13:6-9) N’kutheka kuti pamenepa Yesu ankanena za ntchito imene ankagwira yolalikira mtundu wosamverawo. Pofika nthawi imeneyi iye anali atachita utumiki wake kwa zaka zosachepera zitatu.
it-2 901 ¶5
Milungu 70
“Pakatikati pa mlungu” panali pakatikati pa zaka 7 kapena kuti zaka zitatu ndi hafu za “mlungu” woimira zaka. Popeza kuti “mlungu” wa 70 unayamba mu 29 C.E., pamene Yesu anabatizidwa komanso kudzozedwa kuti akhale Khristu, ndiye kuti hafu ya mlunguwu (zaka zitatu ndi hafu) inali mu 33 C.E., m’nyengo ya Pasika (Nisani 14) m’chakacho. Kalendala ya Gregory imasonyeza kuti tsiku la Pasikali liyenera kuti linali pa 1 April, 33 C.E. Mtumwi Paulo anafotokoza kuti Yesu anabwera ‘kudzachita chifuniro cha Mulungu’ chomwe chinali ‘kuchotsa dongosolo loyambalo [nsembe zimene zinkaperekedwa malinga ndi Chilamulo] kuti akhazikitse lachiwiri.’—Heb. 10:1-10.