November 12-18
MACHITIDWE 1-3
Nyimbo Na. 104 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Mpingo Wachikhristu Unalandira Mzimu Woyera”: (10 min.)
[Onerani vidiyo yakuti Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Machitidwe.]
Mac. 2:1-8, 14, 37, 38, 41—Atalandira mzimu woyera, ophunzira a Yesu anayamba kulalikira ndipo izi zinachititsa kuti anthu pafupifupi 3,000 abatizidwe
Mac. 2:42-47—Ophunzira a Yesu anasonyeza mtima wowolowa manja komanso wochereza ndipo izi zinathandiza kuti anthu amene anangobatizidwa kumene akhalebe kwa kanthawi ku Yerusalemu kuti alimbitse chikhulupiriro chawo (w86 12/1 29 ¶4-5, 7)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)
Mac. 3:15—N’chifukwa chiyani Yesu amatchedwa “Mtumiki Wamkulu wa moyo”? (it-2 61 ¶1)
Mac. 3:19—Kodi vesili likusonyeza bwanji mmene Yehova amachitira akamakhululukira munthu amene walapa? (cl 265 ¶14)
Kodi mwaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kodi ndi mfundo zina ziti zothandiza zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Mac. 2:1-21
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Ulendo Woyamba: (Osapitirira 2 min.) Gwiritsirani ntchito chitsanzo cha ulendo woyamba.
Vidiyo ya Ulendo Wobwereza Woyamba: (5 min.) Onerani ndi kukambirana mfundo za m’vidiyoyi.
Nkhani: (Osapitirira 6 min.) it-1 129 ¶2-3—Mutu: N’chifukwa Chiyani Panasankhidwa Mtumwi Wolowa M’malo Mwa Yudasi Pamene Atumwi Ena Okhulupirika Akamwalira Sankalowedwa M’malo ndi Ena?
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
“Tizichita Zinthu Mogwirizana Tikamalalikira M’gawo la Zinenero Zambiri”: (15 min.) Nkhani yokambirana yokambidwa ndi woyang’anira utumiki. Onerani ndi kukambirana mfundo za m’vidiyoyi. Fotokozani dongosolo lomwe mpingo wanu wakonza lokhudza kulalikira m’gawo la zinenero zambiri.
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 13
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 97 ndi Pemphero