MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Mmene Utumiki Wothandiza Anthu pa Nthawi ya Mavuto Wathandizira Akhristu a ku Caribbean
Monga mmene zinalili ndi Akhristu oyambirira, ifenso masiku ano tili ndi mwayi wosonyeza chikondi kwa Akhristu anzathu omwe akumana ndi ngozi zachilengedwe. (Yoh. 13:34, 35) Onerani vidiyo yakuti Chikondi Chimaonekera ndi Zochita—Ntchito Yothandiza Anthu pa Zilumba za Caribbean kuti muone mmene Akhristu anathandizira abale ndi alongo awo. Kenako kambiranani mafunso otsatirawa:
Kodi abale a ku Caribbean anakumana ndi mavuto otani kutachitika mphepo yamkuntho?
Kodi Yehova anathandiza bwanji abale a ku Caribbean pogwiritsa ntchito Akhristu anzawo?
Kodi Akhristu a ku Caribbean anamva bwanji ataona chikondi chachikulu chomwe Akhristu anzawo anawasonyeza?
Kodi ndi abale ndi alongo ochuluka bwanji omwe anagwira ntchito yothandiza anthu ku Caribbean kutachitika mphepo yamkuntho?
Kodi ena tonse tingachite zotani pothandiza Akhristu anzathu omwe agweredwa tsoka?
Mogwirizana ndi zomwe mwaona m’vidiyoyi, mukumva bwanji mukaganizira kuti muli m’gulu lomwe limachita zinthu mwachikondi?