MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Mukhoza Kumasangalalabe Ngakhale Muli ndi “Munga M’thupi”
M’masiku otsiriza ano atumiki onse a Mulungu akukumana ndi mavuto aakulu okhala ngati munga. (2 Tim. 3:1) Kodi tingasonyeze bwanji kuti timadalira Yehova kuti atithandize kupilira mavutowa? Onerani vidiyo yakuti “Maso a Anthu Akhungu Adzatsegulidwa” kuti mudziwe zimene Talita Alnashi ndi makolo ake anachita. Mukaonera vidiyoyi yankhani mafunso awa:
Kodi Talita akulimbana ndi vuto lanji?
Ndi malonjezo ati a m’Baibulo omwe athandiza Talita ndi makolo ake kuti asamakhale ndi nkhawa kwambiri?
Kodi Makolo a Talita anasonyeza bwanji kuti amadalira Yehova mwana wawo atangochitidwa kumene opaleshoni?
Kodi makolo a Talita amagwiritsa ntchito bwanji zinthu zomwe gulu lathu limatipatsa pothandiza mwana wawo kuti azikonda kwambiri Mulungu?
N’chiyani chikusonyeza kuti Talita akukula mwauzimu ngakhale kuti ali ndi “munga m’thupi”?
Kodi nkhani ya Talita yakulimbikitsani bwanji?