May 27–June 2
AGALATIYA 1-3
Nyimbo Na. 106 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Ndinamutsutsa Pamasom’pamaso”: (10 min.)
[Onerani vidiyo yakuti Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Agalatiya.]
Agal. 2:11-13—Akhristu achiyuda atamuchezera, Petulo anasiya kugwirizana ndi abale a mitundu ina chifukwa choopa anthu (w17.04 27 ¶16)
Agal. 2:14—Paulo anadzudzula Petulo (w13 3/15 5 ¶12)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)
Agal. 2:20—Kodi dipo tiziliona bwanji ndipo n’chifukwa chiyani? (w14 9/15 16 ¶20-21)
Agal. 3:1—N’chifukwa chiyani Paulo ananena kuti Agalatiya anali “opusa”? (it-1 880)
Kodi mwaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kodi ndi mfundo zina ziti zothandiza zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Agal. 2:11-21 (th phunziro 10)
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Vidiyo ya Ulendo Wobwereza Wachiwiri: (5 min.) Onerani ndi kukambirana mfundo za m’vidiyoyi.
Ulendo Wobwereza Wachiwiri: (Osapitirira 3 min.) Gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulendo wobwereza wachiwiri. (th phunziro 2)
Phunziro la Baibulo: (Osapitirira 5 min.) bhs 202-203 ¶18-19 (th phunziro 6)
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
“Zomwe Tonse Tingachite Posamalira Malo Athu Olambirira”: (15 min.) Nkhani yokambirana yokambidwa ndi mkulu. Mukaonera vidiyo yakuti Kusamalira Malo Athu Olambirira ndi kukambirana mafunso a patsamba 7, kambiranani mwachidule ndi m’bale woimira komiti yoyang’anira Nyumba ya Ufumu pogwiritsa ntchito mafunso ali mmunsiwa. (Ngati mpingo wanu ulibe m’bale woimira komiti yoyang’anira Nyumba ya Ufumu, kambiranani ndi wogwirizanitsa ntchito za akulu. Koma ngati mpingo wanu ndi wokhawo umene umagwiritsa ntchito Nyumba ya Ufumuyo, mukambirane ndi woyang’anira Nyumba ya Ufumu.) Kodi ndandanda yosamalira Nyumba ya Ufumu ikutsatiridwa? Kodi timayesetsa kupewa ngozi pogwira ntchitoyi? Takonzapo zinthu ziti chaposachedwa, nanga tikufunika kukonza zinthu ziti m’tsogolomu? Ngati winawake ali ndi luso kapena akufuna ataphunzira ntchitoyo inayake kuchokera kwa amene akuidziwa bwino angatani? Kodi tonsefe, mosatengera kuti zinthu zili bwanji pamoyo wathu, tingatani kuti tizigwira nawo ntchito yosamalira Nyumba ya Ufumu?
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 37
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 3 ndi Pemphero