February 17-23
GENESIS 18-19
Nyimbo Na. 1 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (Osapitirira 1 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“‘Woweruza wa Dziko Lonse Lapansi’ Anawononga Sodomu ndi Gomora”: (10 min.)
Gen. 18:23-25—Abulahamu ankakhulupirira kuti Yehova amapereka chiweruzo cholungama nthawi zonse (w17.04 18 ¶1)
Gen. 18:32—Yehova anatsimikiza kuti sawononga Sodomu ngati mutapezeka anthu 10 olungama (w18.08 30 ¶4)
Gen. 19:24, 25—Yehova anawononga Sodomu ndi Gomora chifukwa anthu ake anali oipa (w10 11/15 26 ¶12)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (10 min.)
Ge 18:1, 22—Kodi Yehova “anaonekera kwa Abulahamu” komanso “anatsala ataima” nayebe m’njira yotani? (w88 5/15 23 ¶4-5)
Gen. 19:26—N’chifukwa chiyani mkazi wa Loti anasanduka “chipilala chamchere”? (w19.06 20 ¶3)
Kodi mwapeza mfundo ziti zokhudza Yehova, utumiki kapena zinthu zina pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Gen. 18:1-19 (th phunziro 12)
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Vidiyo ya Ulendo Wobwereza Woyamba: (5 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyoyi ndipo kenako funsani omvera mafunso otsatirawa: Kodi n’chiyani chakusangalatsani ndi zimene wofalitsayu ananena asanawerenge lemba? Kodi anathandiza bwanji womvetsera wake kuona mmene angagwiritsire ntchito mfundo ya lembalo?
Ulendo Wobwereza Woyamba: (Osapitirira 3 min.) Gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulendo wobwereza woyamba. (th phunziro 6)
Ulendo Wobwereza Woyamba: (Osapitirira 5 min.) Gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulendo wobwereza woyamba. Kenako m’patseni buku lakuti Zimene Baibulo Limaphunzitsa, ndipo kambiranani chithunzi chomwe chili patsamba 98. (th phunziro 9)
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
“Kodi Mumapindula ndi Kabuku ka Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku?”: (15 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyo yakuti, Musamakonde Dziko (1 Yoh. 2:15).
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 73
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 102 ndi Pemphero