CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 18-19
“Woweruza wa Dziko Lonse Lapansi” Anawononga Sodomu ndi Gomora
Kodi tikuphunzirapo chiyani pa zimene Yehova anachita ndi Sodomu komanso Gomora?
Yehova sadzalekerera zoipa ngakhale pang’ono
Anthu amene amamvera komanso kuchita zimene Mulungu amafuna ndi amene adzapulumuke chiweruzo chikubweracho.—Luka 17:28-30
DZIFUNSENI KUTI: ‘Kodi ndimavutika mtima chifukwa cha khalidwe lotayirira la anthu a m’dzikoli?’ (2 Pet. 2:7) ‘Kodi zimene ndimachita tsiku lililonse zimasonyeza kuti ndimaona kuti kuchita chifuniro cha Yehova n’kofunika?’