May 11-17
GENESIS 38-39
Nyimbo Na. 33 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (1 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Yehova Sanasiye Yosefe”: (10 min.)
Gen. 39:1—Yosefe anakhala kapolo ku Iguputo (w14 11/1 12 ¶4-5)
Gen. 39:12-14, 20—Yosefe anamunamizira ndipo anamutsekera m’ndende (w14 11/1 14-15)
Gen. 39:21-23—Yehova anakhalabe ndi Yosefe (w14 11/1 15 ¶2)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (10 min.)
Gen. 38:9, 10—N’chifukwa chiyani Yehova anapha Onani? (it-2 555)
Gen. 38:15-18—Kodi tinganene chiyani pa zimene Yuda ndi Tamara anachita? (w04 1/15 30 ¶4-5)
Pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno, kodi mwapeza mfundo ziti zokhudza Yehova, utumiki kapena zinthu zina?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Gen. 38:1-19 (th phunziro 5)
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Vidiyo ya Ulendo Woyamba: (4 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyoyi, ndipo kenako funsani omvera mafunso otsatirawa: Kodi mlongoyu anachita chiyani kuti uthenga wake ukhale womveka kwa mwininyumba? (th phunziro 17) Kodi wofalitsayu akanatani kuti agawire buku kapena magazini yopezeka pa Zinthu Zophunzitsira?
Ulendo Woyamba: (Osapitirira 2 min.) Gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulendo woyamba. (th phunziro 1)
Ulendo Woyamba: (Osapitirira 3 min.) Yambani ndi chitsanzo cha ulendo woyamba. Sonyezani mmene mungayankhire munthu amene wanena zinthu zina zomwe anthu amakonda kunena ngati sakufuna kuti tikambirane nawo. (th phunziro 11)
Ulendo Woyamba: (Osapitirira 3 min.) Yambani ndi chitsanzo cha ulendo woyamba. Kenako musiyireni khadi lodziwitsa anthu za jw.org. (th phunziro 6)
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
“Khalani Ngati Yosefe—Thawani Dama”: (15 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyo yakuti Thawani Dama.
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 84
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 54 ndi Pemphero