CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 38-39
Yehova Sanasiye Yosefe
Pa nthawi imene Yosefe ankakumana ndi mayesero osiyanasiyana, Yehova ankadalitsa “chilichonse chimene anali kuchita” ndipo “anachititsa mkulu wa ndende kum’konda Yosefe.” (Gen. 39:2, 3, 21-23) Kodi nkhaniyi ikutiphunzitsa chiyani?
Tikakumana ndi mayesero tisamaganize kuti Yehova sakusangalala nafe.—Sal. 34:19
Tiyenera kuyesetsa kuzindikira mmene Yehova akutidalitsira, n’kumamuyamikira.—Afil. 4:6, 7
Tizidalira Yehova kuti azitithandiza.—Sal. 55:22