May 18-24
GENESIS 40-41
Nyimbo Na. 8 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (1 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Yehova Anapulumutsa Yosefe”: (10 min.)
Gen. 41:9-13—Farao anamva kuti Yosefe akhoza kumasulira maloto (w15 2/1 14 ¶4-5)
Gen. 41:16, 29-32—Yehova anathandiza Yosefe kumasulira maloto a Farao (w15 2/1 14-15)
Gen. 41:38-40—Yosefe anakhala wachiwiri kwa Farao monga wolamulira ku Iguputo (w15 2/1 15 ¶3)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (10 min.)
Gen. 41:14—N’chifukwa chiyani Yosefe anameta asanakakumane ndi Farao? (w15 11/1 9 ¶1-3)
Gen. 41:33—Kodi tingaphunzire chiyani tikaona mmene Yosefe analankhulira ndi Farao? (w09 11/15 28 ¶14)
Pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno, kodi mwapeza mfundo ziti zokhudza Yehova, utumiki kapena zinthu zina?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Gen. 40:1-23 (th phunziro 2)
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Vidiyo ya Ulendo Wobwereza Woyamba: (5 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyoyi, ndipo kenako funsani omvera mafunso otsatirawa: N’chiyani chikusonyeza kuti banjali linakonzekera limodzi ulendo wobwerezawu? Kodi m’bale uja anatani pofuna kuthandiza mwininyumba kumvetsa bwino mfundo ya palemba lomwe anawerenga?
Ulendo Wobwereza Woyamba: (Osapitirira 4 min.) Gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulendo wobwereza woyamba. (th phunziro 11)
Ulendo Wobwereza Woyamba: (Osapitirira 5 min.) Yambani ndi chitsanzo cha ulendo wobwereza woyamba. Kenako mugawireni buku kapena magazini yopezeka pa Zinthu Zophunzitsira. (th phunziro 13)
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Khalani Ngati Yosefe—Uzipilira Ngakhale Ena Akukuchitira Nkhanza: (6 min.) Yambani ndi kuonera vidiyo yakuti Khalani Bwenzi la Yehova—Uzipilira Ngakhale Ena Akukuchitira Nkhanza. Kenako uzani ana omwe munawasankhiratu kuti abwere kupulatifomu ndipo afunseni mafunso awa: Kodi Kalebe ndi Sofiya anakumana ndi nkhanza zotani? Kodi mukuganiza kuti anaphunzira chiyani pa zimene zinachitikira Yosefe?
Zofunika Pampingo: (9 min.)
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 85
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 74 ndi Pemphero