MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Khalani Ngati Yosefe—Thawani Dama
Yosefe ndi chitsanzo chabwino kwa ife pamene tikuyesedwa kuti tichite dama. Nthawi zonse mkazi wa mbuye wake akamunyengerera kuti agone naye, Yosefe ankakana. (Gen. 39:7-10) Yankho lake lakuti: “Ndingachitirenji choipa chachikulu chonchi n’kuchimwira Mulungu?” likusonyeza kuti iye ankadziwa kuti Yehova amafuna kuti anthu okhawo omwe ndi okwatirana ndi amene ayenera kugonana. Ndiye zinthu zitafika poipa, sanazengereze komanso sanamupatse mkaziyo mpata womulepheretsa kuchita zoyenera, koma anathawa.—Gen. 39:12; 1 Akor. 6:18.
ONERANI VIDIYO YAKUTI THAWANI DAMA, NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
Kodi Jin anakumana ndi vuto lotani?
Kodi Jin anadzifunsa funso lanzeru liti Mee-Kyong atamupempha kuti amuthandize homuweki ya masamu?
Kodi zimene Mee-Kyong anapempha zinamukhudza bwanji Jin?
Kodi Jin anathandizidwa bwanji?
Kodi Jin anatani kuti athawe dama?
Kodi mwaphunzira zotani mu vidiyoyi?