May 25-31
GENESIS 42-43
Nyimbo Na. 120 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (1 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Yosefe Anasonyeza Kudziletsa Kwambiri”: (10 min.)
Gen. 42:5-7—Yosefe anakhala wodekha ataona azichimwene ake (w15 5/1 13 ¶5; 14 ¶1)
Gen. 42:14-17—Yosefe anayesa azichimwene ake (w15 5/1 14 ¶2)
Gen. 42:21, 22—Azichimwene ake a Yosefe anasonyeza mtima wolapa (it-2 108 ¶4)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (10 min.)
Gen. 42:22, 37—Kodi ndi makhalidwe abwino ati amene Rubeni anasonyeza? (it-2 795)
Gen. 43:32—N’chifukwa chiyani Aiguputo ankaona kuti kudya pamodzi ndi Aheberi kunali konyansa? (w04 1/15 29 ¶1)
Pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno, kodi mwapeza mfundo ziti zokhudza Yehova, utumiki kapena zinthu zina?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Gen. 42:1-20 (th phunziro 2)
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Vidiyo ya Ulendo Wobwereza Wachiwiri: (5 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyoyi, ndipo kenako funsani omvera mafunso otsatirawa: Kodi m’bale uja ananena zotani zomwe zinali zogwirizana ndi lemba lomwe amafuna kuwerenga? Kodi m’bale uja anatani kuti agawire buku la Zimene Baibulo Limaphunzitsa ndipo n’chifukwa chiyani?
Ulendo Wobwereza Wachiwiri: (Osapitirira 3 min.) Gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulendo wobwereza wachiwiri. (th phunziro 15)
Phunziro la Baibulo: (Osapitirira 5 min.) lvs 38-39 ¶18 (th phunziro 8)
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
“Muziyesetsa Kumvetsa Nkhani Yonse”: (15 min.) Nkhani yokambirana. Onerani mbali ina ya vidiyo yakuti Muziyesetsa Kumvetsa Zimene Mumawerenga M’Baibulo. Limbikitsani onse kuti akaonere vidiyo yonse kunyumba kwawo.
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 86 ndime 1-7
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 130 ndi Pemphero