Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb20 September tsamba 3
  • Musamafalitse Nkhani Zabodza

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Musamafalitse Nkhani Zabodza
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2020
  • Nkhani Yofanana
  • ‘Munthu Wosadziwa Zinthu Amakhulupirira Mawu Alionse’
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Kuchuluka kwa Chidziŵitso
    Galamukani!—1998
  • Pitirizani Kuchita Zimene Mwaphunzira
    Nsanja ya Olonda—2002
  • Kodi Mukudziwa Nkhani Yonse?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2018
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2020
mwb20 September tsamba 3

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Musamafalitse Nkhani Zabodza

Mzimayi akugula chakudya ndipo wadabwa ndi zimene waona pafoni yake.

Masiku ano, nkhani zimafalitsidwa mwamsanga komanso kwa anthu ambiri pogwiritsa ntchito zinthu monga nyuzipepala, wailesi, TV kapena intaneti. Atumiki a “Mulungu wachoonadi” safuna kufalitsa nkhani zabodza, ngakhale mosadziwa. (Sl 31:5; Eks 23:1) Nkhani zabodza zikanenedwa kwa anthu ena zingabweretse mavuto ambiri. Mukamafuna kudziwa ngati nkhani inayake ndi yoona kapena ayi, muzidzifunsa kuti:

  • ‘Kodi nkhaniyi ndi yochokera kwa munthu kapena gulu lodalirika?’ N’kutheka kuti munthu amene wakuuzani nkhaniyo sakudziwa nkhani yonse. Nthawi zambiri nkhani zimasinthidwa zikamafalitsidwa ndi anthu. Choncho muzichita zinthu mosamala ngati simukudziwa kumene nkhaniyo yachokera. Anthu amene ali ndi udindo mumpingo ayenera kusamala kwambiri kuti asamafalitse nkhani zopanda umboni. Zili choncho chifukwa abale ndi alongo amakhulupirira zimene iwo amanena.

  • ‘Kodi nkhaniyi ikhoza kuipitsa mbiri ya munthu wina kapena gulu lina?’ Ngati zimenezi zingachitike, si bwino kuuza anthu ena nkhaniyo.​—Miy 18:8; Afi 4:8.

  • ‘Kodi nkhaniyi ingachitikedi?’ Muzisamala kwambiri mukamva nkhani zokhudza zinthu zodabwitsa.

ONERANI VIDIYO YAKUTI, KODI NDINGATANI KUTI NDITHETSE MISECHE? KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Mnyamata wamangiriridwa pabodi ndipo mipeni ikumuzungulira.

    Malinga ndi Miyambo 12:18, kodi mawu angapweteke bwanji anthu?

  • Gulu la anthu omwe akulankhulana zamiseche.

    Kodi lemba la Afilipi 2:4 limatithandiza bwanji kuona moyenera nkhani yolankhula za anthu ena?

  • Munthu akufulatira munthu wina amene akunena miseche.

    Kodi tizichita chiyani anthu akayamba kunena zinthu zoipa zokhudza anthu ena?

  • Munthu akunena miseche ndipo munthu wina yemwe wavala ngati mtolankhani akulemba notsi.

    Tisanayambe kulankhula za ena, kodi tiyenera kudzifunsa mafunso ati?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena