October 5-11
EKISODO 31-32
Nyimbo Na. 45 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (1 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Thawani Kulambira Mafano”: (10 min.)
Eks 32:1—Kulambira milungu yonyenga ndi kolakwika ngakhale pa nthawi yovuta (w09 5/15 11 ¶11)
Eks 32:4-6—Aisiraeli anasakaniza kulambira Yehova ndi kulambira milungu yonyenga (w12 10/15 25 ¶12)
Eks 32:9, 10—Yehova anakwiyira kwambiri Aisiraeli (w18.07 20 ¶14)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (10 min.)
Eks 31:17—Kodi Yehova wakhala akupuma pa tsiku la 7 lolenga zinthu m’njira iti? (w19.12 3 ¶4)
Eks 32:32, 33—Kodi tikudziwa bwanji kuti si zoona kuti munthu akangolandira Yesu kukhala mpulumutsi wake ndiye kuti basi wapulumuka? (w87 9/1 29)
Pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno, kodi mwapeza mfundo ziti zokhudza Yehova, utumiki kapena zinthu zina?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Eks 32:15-35 (th phunziro 10)
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Vidiyo ya Ulendo Woyamba: (4 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyoyi kenako funsani omvera mafunso otsatirawa: N’chifukwa chiyani tinganene kuti Brenda anagwiritsa ntchito bwino mafunso? Kodi anachita zotani pokonza zoti adzakambiranenso ndi munthuyo ulendo wotsatira?
Ulendo Woyamba: (Osapitirira 4 min.) Yambani ndi chitsanzo cha ulendo woyamba. Kenako musonyezeni ndi kukambirana naye mfundo za m’vidiyo yakuti N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuphunzira Baibulo? (koma musaonetse vidiyoyi). (th phunziro 9)
Nkhani: (Osapitirira 5 min.) w10 5/15 21—Mutu: N’chifukwa Chiyani Yehova Sanalange Aroni Atapanga Fano la Mwana wa Ng’ombe? (th phunziro 7)
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
“Muziona Kuti Ubwenzi Wanu Ndi Yehova Ndi Wamtengo Wapatali”: (15 min.) Nkhani Yokambirana. Onerani vidiyo yakuti Muziteteza Ubwenzi Wanu ndi Yehova (Akl 3:5).
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (Osapitirira 30 min.) jy mutu 103
Mawu Omaliza (Osapitirira 3 min.)
Nyimbo Na. 92 ndi Pemphero