Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwbr20 November tsamba 1-4
  • Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu ya November 2020

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu ya November 2020
  • Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2020
  • Timitu
  • NOVEMBER 2-8
  • NOVEMBER 9-15
  • NOVEMBER 16-22
  • NOVEMBER 23-29
  • NOVEMBER 30–​DECEMBER 6
Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2020
mwbr20 November tsamba 1-4

Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu

NOVEMBER 2-8

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EKISODO 39-40

Kufufuza Mfundo Zothandiza

it-2 884 ¶3

Chikopa cha Akatumbu

Mmene Aisiraeli Ankachipezera. Ngati mawu a Chiheberi oti taʹchash opezeka m’Baibulo ankatanthauza mtundu wina wa akatumbu, pangakhale funso lakuti kodi Aisiraeli ankapeza bwanji chikopa cha akatumbu. Nthawi zambiri akatumbu amapezeka kumpoto kwenikweni komanso kum’mwera kwenikweni kwa dziko lapansi. Koma akatumbu ena amakhala kumayiko otentherapo. Mwachitsanzo, masiku ano kunyanja ya Mediterranean komanso kunyanja zina zotentherapo kumapezeka akatumbu ena ochepa. Pa zaka zapitazi, anthu akhala akupha akatumbu ambiri moti atsala ochepa, koma kale n’kutheka kuti nyamazi zinkapezeka zambiri m’nyanja ya Mediterranean komanso m’Nyanja Yofiira. Ngakhale m’chaka cha 1832 buku lina la Chingelezi lotanthauzira mawu a m’Baibulo (Calmet’s Dictionary of the Holy Bible tsa. 139) linati: “Patizilumba tambiri ta m’Nyanja Yofiira, pafupi ndi peninsula ya ku Sinai, pamapezeka akatumbu.”—Onaninso buku lakuti The Tabernacle’s Typical Teaching, lolembedwa ndi A. J. Pollock, tsa. 47.

NOVEMBER 9-15

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | LEVITIKO 1-3

“Chifukwa Chake Nsembe Zinkaperekedwa”

it-2 525

Nsembe

Nsembe zopsereza. Nsembe zopsereza zinkaperekedwa zathunthu kwa Mulungu ndipo palibe mbali iliyonse ya nyama imene wopereka ankatenga. (Yerekezerani ndi Owe 11:30, 31, 39, 40.) Izi zinkasonyeza kuchonderera Yehova kuti alandire, kapena kuti kusonyeza kuti walandira, nsembe yamachimo yomwe nthawi zina ankapereka limodzi ndi nsembe yopsereza. Yesu Khristu anapereka moyo wake wonse ngati “nsembe yopsereza.”

it-2 528 ¶4

Nsembe

Nsembe zambewu. Nsembe zambewu zinkaperekedwa limodzi ndi nsembe zachiyanjano, nsembe zopsereza, nsembe zamachimo komanso ngati zipatso zoyambirira. Zinkaperekedwanso nthawi zina pazokha. (Eks 29:40-42; Le 23:10-13, 15-18; Nu 15:8, 9, 22-24; 28:9, 10, 20, 26-28; chaputala 29) Nsembezi zinkasonyeza kuti Mulungu amapereka madalitso ambiri. Nthawi zambiri zinkaperekedwa limodzi ndi mafuta komanso lubani. Nsembe zambewu zinkaperekedwa monga ufa wosalala kapena mbewu zokazinga. Zinkaperekedwanso monga mkate wozungulira woboola pakati kapena timitanda ta mkate topyapyala ndipo mikateyi inkaphikidwa mu uvuni, m’chiwaya kapena mumphika wa mafuta ambiri. Mbali ina ya nsembe yambewu inkaikidwa paguwa lansembe zopsereza, ina ansembe ankaidya ndipo ngati inaperekedwa monga nsembe yachiyanjano woperekayo ankadya nawo. (Le 6:14-23; 7:11-13; Nu 18:8-11) Nsembe zambewuzi zinkayenera kukhala zopanda chofufumitsa komanso uchi (zikuoneka kuti uchiwu unali madzi a nkhuyu kapena a zipatso zina) zomwe zikhoza kusasa.—Le 2:1-16.

it-2 526 ¶1

Nsembe

Nsembe zachiyanjano (kapena kuti nsembe zamtendere). Nsembe zachiyanjano zovomerezeka ndi Yehova zinkasonyeza kukhala naye pa mtendere. Wopereka nsembeyi limodzi ndi banja lake ankadya nawo (m’bwalo la chihema. Ena amati misasa inkaikidwa mozungulira mkati mwa nsalu yotchingira bwalolo, pomwe m’kachisi munali zipinda zodyeramo). Wansembe wopereka nsembe ankalandira mbali ya nsembeyo ndipo ansembe ena amene ankatumikira pa nthawiyo ankalandira mbali ina. Ndipo zinali ngati Yehova ankalandira utsi wosangalatsa wa mafuta amene ankatenthedwa paguwa lansembe. Magazi, omwe ankaimira moyo wa nyamayo, ankaperekedwa kwa Mulungu. Choncho zinali ngati ansembe, eniake a nsembeyo komanso Yehova ankadyera limodzi, zomwe zinkasonyeza kuti anali pa mtendere. Munthu aliyense amene ankadya nsembe ali wodetsedwa (m’njira iliyonse yotchulidwa m’Chilamulo) kapena amene anadya nyamayo nthawi yoyenera kuidya itadutsa (m’nyengo yotentha ya kumeneko nyamayo inkakhala itayamba kuola) ankayenera kuphedwa. Munthuyo ankadetsa chakudyacho chifukwa choti iye anali wodetsedwa kapena anadya nyamayo itaola zomwe zinali zonyansa kwa Yehova Mulungu. Pochita zimenezi anasonyeza kunyoza zinthu zopatulika.—Le 7:16-21; 19:5-8.

Kufufuza Mfundo Zothandiza

it-1 813

Mafuta

Chifukwa chake lamuloli linaperekedwa. M’pangano la Chilamulo, magazi komanso mafuta ankaonedwa kuti anali a Yehova yekha. M’magazi muli moyo, womwe Yehova yekha ndi amene angapereke, choncho magaziwo ndi ake. (Le 17:11, 14) Mafuta ankaonedwa kuti anali mbali yonona kwambiri ya nyama. Choncho zikuoneka kuti kupereka mafuta a nyama kwa Yehova, yemwe amapereka mowolowa manja, kunkasonyeza kuti mbali zabwino kwambiri ndi zake. Kunkasonyezanso kuti mwini nsembeyo ankafunitsitsa kupatsa Mulungu zinthu zonse zabwino zimene angathe. Popeza mafutawo ankaimira mtima wa Aisiraeli wofuna kupatsa Yehova zinthu zabwino kwambiri, Baibulo limanena kuti ankatenthedwa paguwa lansembe monga “chakudya” komanso “fungo lokhazika mtima pansi” kwa Yehova. (Le 3:11, 16) Choncho munthu akadya mafuta ankakhala kuti wagwiritsa ntchito molakwika zinthu zopatulidwa kwa Mulungu komanso kuphwanya ufulu wa Yehova. Ndiye munthu akadya mafuta ankaphedwa. Koma mosiyana ndi magazi, mafuta ankatha kugwiritsidwa ntchito pa zinthu zina, makamaka ngati nyamayo inafa yokha kapena kuphedwa ndi nyama ina.—Le 7:23-25.

NOVEMBER 16-22

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | LEVITIKO 4-5

“Muzipereka kwa Yehova Zonse Zimene Mungathe”

it-2 527 ¶9

Nsembe

Nsembe za kupalamula. Nsembe za kupalamula zinkaperekedwa chifukwa cha machimo popeza munthu akapalamula amakhala kuti wachimwa. Nsembezi zinkaperekedwa chifukwa cha machimo apadera koma zinkasiyana pang’ono ndi nsembe zamachimo chifukwa zikuoneka kuti zinkaperekedwa chifukwa choti munthuyo anachimwira Yehova kapena munthu wina. Nsembezi zinkathandiza kuti chilungamo cha Yehova chionekere kapena kuthandiza kuti wolakwayo asamavutikebe ndi zotsatira za tchimo lake.—Yerekezerani ndi Yes 53:10.

Kufufuza Mfundo Zothandiza

it-1 1130 ¶2

Kuyera

Zinyama ndi Zokolola. Ng’ombe zamphongo, nkhosa zamphongo ndi mbuzi zamphongo zoyamba kubadwa zinali zopatulika kwa Yehova ndipo zinkayenera kuperekedwa nsembe. Komanso mbali ina ya nsembeyo inkaperekedwa kwa ansembe. (Nu 18:17-19) Zokolola zoyambirira kucha komanso chakhumi zinali zopatulika mofanana ndi mmene zinalili nsembe ndiponso mphatso zonse zopatulidwa kuti zizigwiritsidwa ntchito m’malo opatulika. (Eks 28:38) Zinthu zonse zopatulidwa kwa Yehova sizinkayenera kugwiritsidwa ntchito pa zinthu wamba kapena zosayenera. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi lamulo lokhudza chakhumi. Munthu akaika padera chakhumi cha zinthu ngati tirigu kenako iye kapena munthu wa m’banja lake mosadziwa n’kuphika, munthuyo ankakhala ataphwanya lamulo la Mulungu lokhudza zinthu zopatulika. Lamuloli linanena kuti munthuyo ankayenera kupereka kumalo opatulika chakhumicho n’kuwonjezerapo magawo awiri pa magawo 10 a chakhumicho. Ankayeneranso kupereka nsembe nkhosa yamphongo yopanda chilema. Lamuloli linkathandiza anthu kuti azilemekeza zinthu zopatulidwa kwa Yehova.—Le 5:14-16.

NOVEMBER 23-29

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | LEVITIKO 6-7

“Nsembe Yosonyeza Kuyamikira”

Kufufuza Mfundo Zothandiza

it-1 833 ¶1

Moto

Wa chihema komanso kachisi. Moto unkagwiritsidwa ntchito polambira kuchihema ndipo kenako kukachisi. Tsiku lililonse m’mawa komanso madzulo, mkulu wa ansembe ankafukiza zofukiza paguwa lansembe zofukiza. (Eks 30:7, 8) Lamulo la Mulungu linkanena kuti moto wapaguwa lansembe zopsereza uzikhala woyaka nthawi zonse. (Le 6:12, 13) Ayuda amanena kuti moto wapaguwa lansembe unayatsidwa poyamba ndi Mulungu mozizwitsa ndipo anthu ambiri amakhulupirira zimenezi. Koma si zimene Malemba amaphunzitsa. Malinga ndi malangizo amene Yehova anapatsa Mose, ana a Aroni ankayenera ‘kuika moto paguwa lansembelo ndi kuyalapo nkhuni’ asanaike nsembe paguwalo. (Le 1:7, 8) Moto wochokera kwa Yehova, mwina wochokera kumtambo pamwamba pa chihema, unanyeketsa nsembe imene inali paguwa pambuyo poti unsembe wa Aroni wakhazikitsidwa komanso nsembe za mwambowu zaperekedwa. Izi zikusonyeza kuti moto wochokera kwa Yehovawu sunayatse nkhuni zapaguwa koma ‘unanyeketsa nsembe yopsereza ndiponso mafuta zimene zinali paguwa lansembe.’ Ndiye moto umene unapitiriza kuyaka paguwalo uyenera kuti unkaphatikiza moto wochokera kwa Mulungu komanso moto umene unalipo kale paguwapo. (Le 8:14–9:24) Mofanana ndi zimenezi, moto wochokera kwa Yehova unanyeketsa nsembe, Solomo atangopereka pemphero pa mwambo wopereka kachisi.—2Mb 7:1; onaninso Owe 6:21; 1Mf 18:21-39; 1Mb 21:26 kuti muone nthawi zina pamene Yehova anagwiritsa ntchito moto posonyeza kuti walandira nsembe zimene atumiki ake anapereka.

si 27 ¶15

Buku la Baibulo Nambala 3—Levitiko

15 (3) Munthu ankayenera kupereka nsembe yamachimo chifukwa cha machimo amene sankadziwa kuti wachita kapena wachita mwangozi. Nyama imene inkayenera kuperekedwa inkadalira amene anachita machimo, kaya ndi wansembe, mtundu wonse, mtsogoleri kapena munthu wamba. Mosiyana ndi nsembe zopsereza komanso zachiyanjano zimene anthu ankapereka mwa kufuna kwawo, nsembe zamachimo anthu ankalamulidwa kupereka.—4:1-35; 6:24-30.

NOVEMBER 30–​DECEMBER 6

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | LEVITIKO 8-9

“Umboni Wakuti Yehova Ankawadalitsa”

it-1 1207

Kulonga Munthu Unsembe

Mose anasambitsa Aroni komanso ana ake, Nadabu, Abihu, Eleazara ndi Itamara (kapena kuti anawauza kuti asambe) m’beseni losambira lamkuwa pabwalo n’kuveka Aroni zovala zaulemerero za mkulu wa ansembe. (Nu 3:2, 3) Aroni anavala zovala zokongolazi ndipo zinali ngati wapatsidwa chizindikiro cha makhalidwe komanso udindo wa ntchito yake. Kenako Mose anadzoza chihema, zinthu zonse zam’chihemacho, guwa lansembe zopsereza, beseni komanso ziwiya. Zimenezi zinkachititsa kuti zinthuzi zikhale zopatulika kuti zizingogwiritsidwa ntchito potumikira Mulungu basi. Pomaliza Mose anadzoza Aroni pothira mafuta pamutu pake.—Le 8:6-12; Eks 30:22-33; Sl 133:2.

it-1 1208 ¶8

Kulonga Munthu Unsembe

Pa tsiku la 8, ansembe anali atalongedwa ndipo anayamba kugwira ntchito yawo (popanda Mose kuwathandiza) pochita mwambo wophimba machimo a Aisiraeli. Aisiraeli ankafunika kuyeretsedwa chifukwa choti anali ochimwa komanso chifukwa cha zoipa zimene anachita ndi mwana wa ng’ombe wagolide, zomwe zinakwiyitsa Yehova. (Le 9:1-7; Eks 32:1-10) Pambuyo poti ansembe atsopano achita mwambowu, Yehova anasonyeza kuti anavomereza mwambowu komanso ansembewo potumiza moto, mosakayikira wochokera kumtambo pamwamba pa chihema, n’kunyeketsa zotsala paguwa la nsembe.—Le 9:23, 24.

Kufufuza Mfundo Zothandiza

it-2 437 ¶3

Mose

Mulungu anasankha Mose kuti akhale mkhalapakati wa pangano la chilamulo ndi Aisiraeli. Udindowu unali wapadera kwambiri moti panalibe munthu wina amene anali ndi udindo ngati umenewu kupatulapo Yesu Khristu, yemwe ndi Mkhalapakati wa pangano latsopano. Mose anatenga magazi a nsembe za nyama n’kuwaza buku la pangano, limene linkaimira Yehova, komanso anawaza Aisiraeli (mosakayikira akulu). Izi zinali ngati wawaza magulu awiri a panganoli. Iye anawerengera Aisiraeli buku la pangano ndipo iwo anayankha kuti, “Mawu onse amene Yehova wanena tidzachita.” (Eks 24:3-8; Ahe 9:19) Monga mkhalapakati, Mose anali ndi mwayi woyang’anira kupangidwa kwa chihema ndi ziwiya zake potsatira malangizo amene Yehova anamupatsa. Anayang’aniranso kulonga anthu unsembe ndipo anadzoza chihema komanso Aroni monga mkulu wa ansembe ndi mafuta opangidwa mwapadera. Kenako anatsogolera pa nthawi yoyamba imene ansembe atsopano anayamba utumiki wawo.—Eks chaputala 25-29; Le chaputala 8, 9.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena