Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb22 November tsamba 3
  • “Khalani Opatsa”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Khalani Opatsa”
  • Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2022
  • Nkhani Yofanana
  • Timathokoza Yehova Chifukwa cha Chikondi Chanu
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
  • ‘Muziika Kenakake Pambali’
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
  • ‘Timakobidi Tiwiri Tating’ono’ Tamtengo Wapatali
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2020
  • “Muzipereka Mphatso kwa Yehova”
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2018
Onani Zambiri
Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2022
mwb22 November tsamba 3
Mlongo wachikulire akupereka ndalama kudzera pa intaneti. Zithunzi zosonyeza mmene zopereka zathu zimagwirira ntchito. 1. Kusindikiza mabuku ku Beteli. 2. Masukulu ophunzitsa Baibulo. 3. Ulaliki wa m’malo opezeka anthu ambiri. 4. Ntchito zomangamanga.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

“Khalani Opatsa”

Yesu ananena kuti munthu wopatsa amachititsanso ena kukhala opatsa. (Lu 6:38) Mukakhala ndi chizolowezi chopatsa ena zinthu, mumalimbikitsa abale ndi alongo anu kukhala okoma mtima komanso opatsa.

Yehova amayembekezera kuti anthu amene amamulambira azipereka mokondwera. Iye amaona anthu amene ali ndi mtima wopatsa komanso omwe amathandiza Akhristu anzawo amene akuvutika ndipo adzawapatsa mphoto.​—Miy 19:17.

ONERANI VIDIYO YAKUTI TIKUKUTHOKOZANI CHIFUKWA CHA MTIMA WANU WOPATSA, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi zopereka zanu zimagwiritsidwa ntchito bwanji pothandiza abale ndi alongo anu?

  • N’chifukwa chiyani tiyenera kupitiriza kukhala ndi mtima wopatsa posatengera kukula kwa mphatso zathu?​—Onaninso nkhani ya pa jw.org yakuti “Zimene Ena Ali Nazo Zimathandizira pa Zimene Ena Akusowa.”

DZIWANI ZAMBIRI PAWEBUSAITI YATHU

Kodi mungapereke bwanji ndalama zothandizira ntchito ya Mboni za Yehova? Dinani pa mawu akuti “Donations” m’munsi mwa tsamba loyamba la JW Library®. M’mayiko ambiri, pangakhale linki ina yopita ku nkhani yonena za Mafunso Ofunsidwa Kawirikawiri ya mutu wakuti Zopereka Zopita ku Gulu la Mboni za Yehova​—Mafunso Ofunsidwa Kawirikawiri.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena