Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb25 January tsamba 2-3
  • January 6-12

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • January 6-12
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Kabuku ka Msonkhano—2025
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Kabuku ka Msonkhano—2025
mwb25 January tsamba 2-3

JANUARY 6-12

MASALIMO 127-134

Nyimbo Na. 134 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. Makolo, Pitirizani Kusamalira Cholowa Chanu Chamtengo Wapatali

(10 min.)

Makolo akhoza kudalira Yehova kuti awathandiza kupezera banja lawo zofunika pa moyo (Sl 127:1, 2)

Ana ndi mphatso yamtengo wapatali yochokera kwa Yehova (Sl 127:3; w21.08 5 ¶9)

Muziphunzitsa mwana aliyense mogwirizana ndi zimene amafunikira (Sl 127:4; w19.12 27 ¶20)

Bambo akugwiritsa ntchito kabuku kamutu wakuti “Zimene Ndikuphunzira M’Baibulo” pophunzitsa ana ake awiri. Anawo akuganizira akusewera ndi njovu komanso nyani m’Paradaiso.

Yehova amasangalala ngati makolo amamudalira komanso amayesetsa kuchita zonse zomwe angathe posamalira ana awo

2. Mfundo Zothandiza

(10 min.)

  • Sl 128:3—N’chifukwa chiyani wolemba masalimo anayerekezera ana ndi mphukira za mtengo wa maolivi? (it-1 543)

  • Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

3. Kuwerenga Baibulo

(4 min.) Sl 132:1-18 (th phunziro 2)

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

4. Ulendo Woyamba

(3 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. (lmd phunziro 1 mfundo 3)

5. Ulendo Woyamba

(4 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Munthuyo watchula zimene amakhulupirira koma ndi zotsutsana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa. (lmd phunziro 5 mfundo 4)

6. Kuphunzitsa Anthu

(5 min.) lff phunziro 16 mfundo 4-5. Konzani zoti wophunzira wanuyo adzaphunzire Baibulo ngakhale kuti inu mukuchokapo. (lmd phunziro 10 mfundo 4)

MOYO WATHU WA CHIKHRISTU

Nyimbo Na. 13

7. Makolo, Kodi Ndinu Chitsanzo Chabwino kwa Ana Anu?

(15 min.) Nkhani yokambirana.

Gulu la Yehova latulutsa zinthu zambiri pofuna kuthandiza makolo kuti aziphunzitsa ana awo zokhudza Yehova. Komabe, njira yabwino kwambiri imene makolo angagwiritse ntchito ndi chitsanzo chawo chabwino.—De 6:5-9.

Yesu ankagwiritsa ntchito njira imeneyi pophunzitsa ophunzira ake.

Werengani Yohane 13:13-15. Kenako funsani omvera funso ili:

  • N’chifukwa chiyani mukuganiza kuti njira imene Yesu ankagwiritsira ntchitoyi inali yothandiza kwambiri?

Monga makolo, zimene mumachita zingathandize ana anu kumvetsa kuti zimene mumawaphunzitsa ndi zoona. Chitsanzo chanu chabwino chikhozanso kuwathandiza kuti azilemekeza zimene mumawaphunzitsa komanso azikumverani mosavuta.

Zithunzi za muvidiyo yakuti “Ana Athu Anatengera Chitsanzo Chathu.” 1. Banja la a Garcia lili m’galimoto pamene akupita kumisonkhano. 2. Banjalo lakhala mozungulira tebulo kunyumba kwawo pambuyo pa misonkhano. Akudya komanso akucheza. 3. M’bale Garcia wasiya kaye kuphunzira payekha kuti alankhule ndi mwana wake. 4. M’bale ndi Mlongo Garcia akugwiritsa ntchito Baibulo pokambirana ndi mwana wawo.

Onerani VIDIYO yakuti Ana Athu Anatengera Chitsanzo Chathu. Kenako funsani omvera mafunso otsatirawa:

  • Kodi M’bale ndi Mlongo Garcia anaphunzitsa ana awo zinthu zofunika ziti?

  • Kodi vidiyoyi yakulimbikitsani bwanji kuti mupitirizebe kukhala chitsanzo chabwino kwa ana anu?

Chitsanzo chanu chabwino chingathandize ana anu kuti . . .

  • azisankha zinthu mwanzeru pa nkhani ya zosangalatsa, kumwa mowa komanso kugwiritsa ntchito malo ochezera a pa intaneti

  • aziona kuti zinthu zokhudza kulambira ndi zofunika kwambiri pa moyo wawo

  • azilemekeza komanso kukonda mkazi kapena mwamuna wawo

8. Phunziro la Baibulo la Mpingo

(30 min.) bt mutu 20 ¶13-20

Mawu Omaliza (3 min.) | Nyimbo Na. 73 ndi Pemphero

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena