Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb25 March tsamba 2-16
  • March 3-9

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • March 3-9
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Kabuku ka Msonkhano—2025
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Kabuku ka Msonkhano—2025
mwb25 March tsamba 2-16

MARCH 3-9

MIYAMBO 3

Nyimbo Na. 8 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. Muzisonyeza Kuti Mumakhulupirira Yehova

(10 min.)

Musamadzidalire koma muzikhulupirira Yehova (Miy 3:5; ijwbv nkhani na. 14 ¶4-5)

Muzisonyeza kuti mumakhulupirira Yehova pofunafuna malangizo ake komanso kuwatsatira (Miy 3:6; ijwbv nkhani na. 14 ¶6-7)

Muzipewa kudzidalira kwambiri (Miy 3:7; be 76 ¶4)

Mlongo wachitsikana akufufuza pa tabuleti zolinga zomwe angakhale nazo. Kumanzere kwake kuli timabuku tokhudzana ndi maphunziro am’dzikoli. Kumanja kwake kuli fomu yofunsira utumiki komanso timabuku tofotokoza utumiki wa pa Beteli.

DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi ndimafunafuna malangizo a Yehova pa zonse zomwe ndimachita pa moyo wanga?’

2. Mfundo Zothandiza

(10 min.)

  • Miy 3:3—Kodi chikondi chokhulupirika komanso kukhulupirika tingazimange bwanji m’khosi mwathu ndiponso kuzilemba pamtima pathu? (w06 9/15 17 ¶7)

  • Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

3. Kuwerenga Baibulo

(4 min.) Miy 3:1-18 (th phunziro 12)

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

4. Ulendo Woyamba

(3 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Sonyezani mmene mungayankhire munthu amene wanena zinthu zomwe anthu amakonda kunena ngati sakufuna kuti tikambirane nawo. (lmd phunziro 1 mfundo 5)

5. Ulendo Woyamba

(4 min.) KULALIKIRA M’MALO OPEZEKA ANTHU AMBIRI. Mufotokozereni za webusaiti yathu ya jw.org ndipo m’patseni khadi lodziwitsa anthu za webusaitiyi. (lmd phunziro 3 mfundo 3)

6. Nkhani

(5 min.) w11 3/15 14 ¶7-10—Mutu: Muzisonyeza Kuti Mumadalira Mulungu Mukakumana ndi Anthu Opanda Chidwi mu Utumiki. (th phunziro 20)

MOYO WATHU WA CHIKHRISTU

Nyimbo Na. 124

7. Muzisonyeza Kuti Mumakhulupirira Gulu la Yehova

(15 min.) Nkhani yokambirana.

Zikhoza kukhala zosavuta kukhulupirira malangizo opezeka m’Mawu achoonadi ouziridwa, Baibulo. Koma zikhoza kukhala zovuta kukhulupirira malangizo ochokera kwa anthu opanda ungwiro omwe amatsogolera gulu la Yehova, makamaka ngati sitikumvetsa kapena kugwirizana ndi malangizowo.

Werengani Malaki 2:7. Kenako funsani funso lotsatirali:

  • N’chifukwa chiyani sitiyenera kudabwa kuti Yehova amagwiritsa ntchito anthu opanda ungwiro kuti azitsogolera anthu ake?

Werengani Mateyu 24:45. Kenako funsani funso lotsatirali:

  • N’chifukwa chiyani tiyenera kukhulupirira malangizo ochokera ku gulu la Yehova?

Werengani Aheberi 13:17. Kenako funsani funso lotsatirali:

  • N’chifukwa chiyani tiyenera kugwirizana ndi zosankha za abale amene Yehova amawakhulupirira kuti azitsogolera mu gulu lake?

M’bale wakapereka chakudya kwa banja lina. Onse avala masiki ndipo akubayibitsana ali chapatali.
Mlongo akupereka ndemanga pamisonkhano. M’bale wamupatsira maikolofoni kuti ayankhirepo. Onse m’Nyumba ya Ufumuyo avala masiki.

Onerani VIDIYO yakuti Lipoti la Bungwe Lolamulira la Nambala 9 la 2021—Kachigawo Kake. Kenako funsani funso lotsatirali:

  • Kodi malangizo amene tinalandira pa nthawi ya COVID-19, anakuthandizani bwanji kuti muzikhulupirira kwambiri gulu la Yehova?

8. Phunziro la Baibulo la Mpingo

(30 min.) bt mutu 23 ¶9-15, bokosi patsamba 184, 186

Mawu Omaliza (3 min.) | Nyimbo Na. 57 ndi Pemphero

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena