MARCH 24-30
MIYAMBO 6
Nyimbo Na. 11 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)
1. Kodi Tingaphunzire Chiyani kwa Nyerere?
(10 min.)
Tingaphunzire zambiri kuchokera kwa nyerere (Miy 6:6)
Ngakhale kuti zilibe wozilamulira, mwachibadwa nyerere zimagwira ntchito mwakhama, zimachita zinthu mogwirizana komanso zimakonzekereratu zam’tsogolo (Miy 6:7, 8; it-1 115 ¶1-2)
Muzitengera chitsanzo cha nyerere (Miy 6:9-11; w00 9/15 26 ¶3-4)
© Aerial Media Pro/Shutterstock
2. Mfundo Zothandiza
(10 min.)
Miy 6:16-19—Kodi machimo amene atchulidwa m’mavesi amenewa akutchula zinthu zonse zimene Yehova amadana nazo? (w00 9/15 27 ¶3)
Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
3. Kuwerenga Baibulo
(4 min.) Miy 6:1-26 (th phunziro 10)
4. Ulendo Woyamba
(4 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Itanirani wachibale amene anasiya kusonkhana kuti adzamvetsere nawo nkhani yapadera komanso kuti adzabwere ku Chikumbutso. (lmd phunziro 4 mfundo 3)
5. Ulendo Woyamba
(4 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Pemphani abwana anu kuti akuloleni kuti musadzapite kuntchito n’cholinga choti mudzapezeke pa Chikumbutso. (lmd phunziro 3 mfundo 3)
6. Ulendo Woyamba
(4 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Muitanireni ku nkhani yapadera komanso ku Chikumbutso. (lmd phunziro 5 mfundo 3)
Nyimbo Na. 2
7. Chilengedwe Chimasonyeza Kuti Yehova Amafuna Tizisangalala—Nyama Zochititsa Chidwi
(5 min.) Nkhani yokambirana.
Onerani VIDIYO. Kenako funsani funso lotsatirali:
Kodi zinyama zimatiphunzitsa chiyani zokhudza Yehova?
8. Zofunika Pampingo
(10 min.)
9. Phunziro la Baibulo la Mpingo
(30 min.) bt mutu 24 ¶7-12, bokosi patsamba 193