JULY 7-13
MIYAMBO 21
Nyimbo Na. 98 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)
1. Mfundo Zothandiza Kuti Banja Lizikhala Losangalala
(10 min.)
Musathamangire kulowa m’banja (Miy 21:5; w03 10/15 4 ¶5)
Muzisonyeza kuti ndinu wodzichepetsa pakakhala kusamvana (Miy 21:2, 4; g 7/08 7 ¶2)
Muzichitirana zinthu moleza mtima komanso mokoma mtima (Miy 21:19; w06 9/15 28 ¶13)
2. Mfundo Zothandiza
(10 min.)
Miy 21:31—Kodi kufotokoza zokhudza hatchi palembali, kukutithandiza bwanji kumvetsa bwino udindo wa Yesu mu ulosi wopezeka pa Chivumbulutso 6:2? (w05 1/15 17 ¶9)
Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
3. Kuwerenga Baibulo
(4 min.) Miy 21:1-18 (th phunziro 5)
4. Ulendo Woyamba
(3 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. (lmd phunziro 3 mfundo 3)
5. Ulendo Wobwereza
(4 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. (lmd phunziro 7 mfundo 3)
6. Kufotokoza Zimene Mumakhulupirira
(5 min.) Chitsanzo. Ijwfq nkhani na. 54—Mutu: Kodi a Mboni za Yehova Amaiona Bwanji Nkhani Yothetsa Banja? (lmd phunziro 4 mfundo 3)
Nyimbo Na. 132
7. Muzilemekezana M’banja
(15 min.) Nkhani yokambirana.
Mukakwatirana, mumalonjeza pamaso pa Yehova kuti muzikondana komanso kulemekezana. Choncho mmene mumachitira zinthu ndi mwamuna kapena mkazi wanu zimakhudza ubwenzi wanu ndi Yehova.—Miy 20:25; 1Pe 3:7.
Onerani VIDIYO yakuti Mungatani Kuti Banja Lanu Lizisangalala: Muzisonyezana Ulemu. Kenako funsani mafunso awa:
Kodi kusonyeza ulemu kwa mwamuna kapena mkazi wanu n’kofunika bwanji?
Kodi ndi zinthu ziti zimene tingafunike kusintha n’cholinga choti tizichita zinthu mwaulemu kwambiri?
Kodi ndi mfundo zina ziti za m’Baibulo zimene zingatithandize?
Kodi tingasonyeze ulemu kwa mwamuna kapena mkazi wathu m’njira ziti?
Kodi tiyenera kumaganizira zinthu ziti zokhudza mwamuna kapena mkazi wathu, nanga n’chifukwa chiyani?
8. Phunziro la Baibulo la Mpingo
(30 min.) bt mutu 28 ¶16-22