JULY 14-20
MIYAMBO 22
Nyimbo Na. 79 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)
1. Mfundo Zothandiza Polera Ana
(10 min.)
Muzithandiza ana anu kukonzekera mavuto amene angadzakumane nawo m’tsogolo (Miy 22:3; w20.10 27 ¶7)
Muziyamba kuwaphunzitsa akangobadwa (Miy 22:6; w19.12 26 ¶17-19)
Muziwalangiza mwachikondi (Miy 22:15; w06 4/1 9 ¶4)
2. Mfundo Zothandiza
(10 min.)
Miy 22:29—Kodi tingagwiritse ntchito bwanji vesili pa zochitika za mpingo, nanga zimenezi zili ndi ubwino wotani? (w21.08 23 ¶11)
Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
3. Kuwerenga Baibulo
(4 min.) Miy 22:1-19 (th phunziro 10)
4. Ulendo Woyamba
(3 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. (lmd phunziro 5 mfundo 4)
5. Ulendo Woyamba
(4 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Muonetseni mmene angapezere malangizo othandiza makolo pa jw.org. (lmd phunziro 1 mfundo 4)
6. Nkhani
(5 min.) ijwyp nkhani na. 100—Mutu: Kodi Ndingatani Ngati Sindinamvere Lamulo la Makolo Anga? (th phunziro 20)
Nyimbo Na. 134
7. Muzikhala Oleza Mtima Koma Osati Olekerera
(15 min.) Nkhani yokambirana.
Kulera ana kumafuna kuleza mtima kwambiri. Makolo amafunika kumachita chidwi ndi ana awo nthawi zonse komanso kumakhala ndi nthawi yokwanira yochita nawo zinthu. (De 6:6, 7) Kuti adziwe zimene zili mumtima mwa ana awo, makolo amayenera kuwafunsa mafunso kenako n’kumawamvetsera akamafotokoza. (Miy 20:5) Makolo ayenera kumabwereza malangizo amene amapereka kwa ana awo n’cholinga choti anawo amvetse malangizowo n’kumawagwiritsa ntchito.
Komabe, sikuti makolo oleza mtima amakhala olekerera. Yehova anapereka udindo kwa makolo ouza ana awo zimene akuyenera kuchita ndi zimene sakuyenera kuchita komanso kuti aziwapatsa chilango ngati sanamvere.—Miy 6:20; 23:13.
Werengani Aefeso 4:31. Kenako funsani funso ili:
N’chifukwa chiyani makolo sayenera kupereka chilango kwa ana awo atapsa mtima?
Werengani Agalatiya 6:7. Kenako funsani funso ili:
N’chifukwa chiyani makolo amayenera kuphunzitsa ana awo kuti zochita zawo zimakhala ndi zotsatirapo zake, kaya zoipa kapena zabwino?
Onerani VIDIYO yakuti ‘Moleza Mtima, Muzilolerana M’chikondi’—Ana Anu. Kenako funsani funso ili:
Kodi mwaphunzira chiyani muvidiyoyi?
8. Phunziro la Baibulo la Mpingo
(30 min.) lfb “Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira,” mawu ofotokoza chigawo 1 komanso mutu 1