AUGUST 11-17
MIYAMBO 26
Nyimbo Na. 88 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)
1. Muzipewa “Munthu Wopusa”
(10 min.)
“Munthu wopusa” sayenera kulemekezedwa (Miy 26:1; it-2 729 ¶6)
“Anthu opusa” nthawi zambiri amafunikira chilango champhamvu (Miy 26:3; w87 10/1 19 ¶12)
“Munthu wopusa” amakhala wosadalirika (Miy 26:6; it-2 191 ¶4)
TANTHAUZO: M’Baibulo, mawu akuti “munthu wopusa” amatanthauza munthu amene saganiza bwino ndipo satsatira mfundo zolungama za Mulungu.
2. Mfundo Zothandiza
(10 min.)
Miy 26:4, 5—N’chifukwa chiyani tinganene kuti mavesi awiriwa satsutsana? (it-1 846)
Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
3. Kuwerenga Baibulo
(4 min.) Miy 26:1-20 (th phunziro 5)
4. Ulendo Woyamba
(3 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Yambani kukambirana pogwiritsa ntchito kapepala. (lmd phunziro 1 mfundo 5)
5. Ulendo Wobwereza
(4 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Pitirizani kukambirana za kapepala komwe munasiya pa ulendo wapita. (lmd phunziro 7 mfundo 4)
6. Kuphunzitsa Anthu
(5 min.) Thandizani wophunzira wanu kukonzekera kudzalalikira wachibale wake. (lmd phunziro 11 mfundo 5)
Nyimbo Na. 94
7. Kuphunzira Baibulo Panokha Kumakupatsani ‘Nzeru Zothandiza kuti Mudzapulumuke’
(15 min.) Nkhani yokambirana.
Mtumwi Paulo anakumbutsa Timoteyo kuti aziona kuti malemba oyera omwe anaphunzira kuyambira ali mwana ndi ofunika kwambiri. Malemba amenewa anathandiza Timoteyo kupeza ‘nzeru zomuthandiza kuti adzapulumuke.’ (2Ti 3:15) Chifukwa choti choonadi cha m’Baibulo ndi chamtengo wapatali, Mkhristu aliyense ayenera kumapeza nthawi yowerenga komanso kuphunzira Baibulo. Koma bwanji ngati sitisangalala ndi kuphunzira?
Werengani 1 Petulo 2:2. Kenako funsani mafunso awa:
Kodi n’zotheka kuti tizisangalala pophunzira Baibulo?
Kodi tingatani kuti ‘tizilakalaka’ Mawu a Mulungu?—w18.03 29 ¶6
Kodi mapulogalamu a pa zipangizo zamakono amene gulu la Yehova limatipatsa, angatithandize bwanji pophunzira Baibulo?
Onerani VIDIYO yakuti Zimene Gulu Lathu Lachita—Zimene Zingakuthandizeni Mukamagwiritsa Ntchito JW Library. Kenako funsani mafunso awa:
Kodi pulogalamu ya JW Library® yakuthandizani bwanji?
Kodi ndi zinthu ziti mu pulogalamu ya JW Library® zimene zimakusangalatsani?
Kodi ndi zinthu ziti mu pulogalamuyi zimene mukufuna kuphunzira n’kuyamba kuzigwiritsa ntchito?
8. Phunziro la Baibulo la Mpingo
(30 min.) lfb mutu 8-9