AUGUST 18-24
MIYAMBO 27
Nyimbo Na. 102 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)
1. Anzathu Abwino Amatithandiza
(10 min.)
Anzathu abwino amatipatsa malangizo molimba mtima (Miy 27:5, 6; w19.09 5 ¶12)
Anzathu abwino akhoza kutithandiza bwino kwambiri kuposa achibale athu (Miy 27:10; it-2 491 ¶3)
Anzathu abwino amatithandiza kukhala anthu abwino (Miy 27:17; w23.09 9 ¶7)
2. Mfundo Zothandiza
(10 min.)
Miy 27:21—Kodi kutamandidwa kumayesa munthu m’njira yotani? (w06 9/15 19 ¶12)
Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
3. Kuwerenga Baibulo
(4 min.) Miy 27:1-17 (th phunziro 5)
4. Ulendo Woyamba
(3 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Lalikirani munthu amene si Mkhristu. (lmd phunziro 6 mfundo 5)
5. Ulendo Wobwereza
(4 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Gwiritsani ntchito vidiyo yopezeka pa Zinthu Zophunzitsira. (lmd phunziro 8 mfundo 3)
6. Nkhani
(5 min.) ijwyp nkhani na. 75—Mutu: Ndingatani Ngati Mnzanga Atandikhumudwitsa? (th phunziro 14)
Nyimbo Na. 109
7. “M’bale Amene Anabadwa Kuti Akuthandize Pakagwa Mavuto”
(15 min.) Nkhani yokambirana.
Yehova anatipatsa abale ndi alongo padziko lonse, ndipo pakati pa anthu amenewa tikhoza kupeza anzathu amene amatikonda. N’zoona kuti tikhoza kumacheza ndi anthu onse mumpingo, koma kodi anzathu apamtima ndi angati? Anthu amakhala mabwenzi apamtima ngati amamvetsetsana, amakhulupirirana, amalankhulana momasuka, amachitira zinthu limodzi komanso amathandizana kuchokera pansi pa mtima. Choncho pamafunika nthawi komanso khama kuti anthu ayambe kugwirizana n’kukhala mabwenzi apamtima.
Werengani Miyambo 17:17. Kenako funsani funso ili:
N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala ndi mabwenzi apamtima panopa chisautso chachikulu chisanayambe?
Werengani 2 Akorinto 6:12, 13. Kenako funsani funso ili:
Kodi kugwiritsa ntchito mfundo za m’mavesiwa kungatithandize bwanji kupeza anzathu?
Onerani VIDIYO yakuti “Chilichonse Chili ndi Nthawi Yake”—Kulimbitsa Ubwenzi ndi Anzathu Kumatenga Nthawi. Kenako funsani funso ili:
Kodi mwaphunzira chiyani zokhudza anzanu kuchokera muvidiyoyi?
Kuti mupeze anzanu, mungayambe ndi kuwamwetulira kapena kuwapatsa moni wansangala, kenako n’kumawasonyeza chidwi. Kuti ubwenziwo ulimbe zimatenga nthawi, choncho muzikhala oleza mtima. Mukamachita zinthu zomwe zingalimbitse ubwenzi wanu ndi anzanu, mukhoza kukhala mabwenzi mpaka kalekale.
8. Phunziro la Baibulo la Mpingo
(30 min.) lfb mutu 10-11