SEPTEMBER 29–OCTOBER 5
MLALIKI 3-4
Nyimbo Na. 93 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)
Muzichitira zinthu limodzi ndi mkazi kapena mwamuna wanu komanso ndi Yehova
1. Muzilimbitsa Chingwe Chanu Chopotedwa ndi Zingwe Zitatu
(10 min.)
Muzipeza nthawi kuti muzikambirana zinthu zolimbikitsa komanso zofunika ndi mkazi kapena mwamuna wanu (Mla 3:1; ijwhf nkhani na. 10 ¶2-8)
Muzichitira zinthu limodzi (Mla 4:9; w23.05 23-24 ¶12-14)
Muzilimbitsa ubwenzi wanu ndi Yehova (Mla 4:12; w23.05 21 ¶3)
DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi kukhala popanda mkazi kapena mwamuna wanga kwa nthawi yaitali, kupita ku holide ndekha, kapena kupita kwina kukagwira ntchito kungakhudze bwanji banja langa?’
2. Mfundo Zothandiza
(10 min.)
Mla 3:8—Kodi ndi nthawi iti imene si “nthawi yachikondi”? (it “Chikondi” ¶39)
Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
3. Kuwerenga Baibulo
(4 min.) Mla 4:1-16 (th phunziro 2)
4. Ulendo Woyamba
(3 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Gwiritsani ntchito Nsanja ya Olonda Na. 1 2025 kuti muyambe kukambirana. Sinthani nkhani yomwe mukukambirana kuti igwirizane ndi nkhani yomwe munthuyo ali nayo chidwi. (lmd phunziro 2 mfundo 5)
5. Ulendo Wobwereza
(4 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Pemphani kuti muziphunzira Baibulo ndi munthu amene walandira Nsanja ya Olonda Na. 1 2025. (lmd phunziro 9 mfundo 4)
6. Nkhani
(5 min.) lmd zakumapeto A mfundo 12—Mutu: Mulungu Alibe Tsankho Ndipo Sakondera. (th phunziro 19)
Nyimbo Na. 131
7. Mukakumana ndi Mavuto M’banja Lanu, Muzidalira Yehova Kuti Akuthandizeni
(15 min.) Nkhani yokambirana.
Yehova anapereka kwa mabanja zinthu zonse zimene angafunikire kuti azisangalala komanso kuti banjalo liziyenda bwino. Komabe, nthawi ndi nthawi banja likhoza kumakumana ndi mavuto. (1Ak 7:28) Ngati sangapeze njira yothetsera mavutowo, sangamasangalale komanso angayambe kuona kuti zinthu sizingasinthe. Kodi mungatani ngati mukukumana ndi mavuto m’banja lanu?
Vidiyo yakuti Chikondi Chenicheni inasonyeza banja lachinyamata lomwe linkakumana ndi mavuto aakulu kwambiri. Kodi mukukumbukira malangizo amene bambo wa muvidiyoyi anapereka kwa mwana wake pamene ankafuna kusankha zinthu zimene sizikanasangalatsa Yehova?
Onerani VIDIYO yakuti Chikondi Chenicheni—Kachigawo Kake. Kenako funsani funso ili:
N’chifukwa chiyani tiyenera kudalira malangizo a Yehova tikamakumana ndi mavuto a m’banja?—Yes 48:17; Mt 19:6
Mukamakumana ndi mavuto aakulu m’banja lanu, muzionetsetsa kuti ubwenzi wanu ndi Yehova uli bwino pochitabe zinthu zokhudza kulambira. Muziyesetsa kuthetsa mavuto anu pogwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo komanso muzifufuza m’mabuku athu mfundo zomwe zingakuthandizeni kuona mavutowo mmene Yehova amawaonera. Mukamachita zimenezi, mumakhala mukusonyeza Yehova kuti mukufuna kuti akuthandizeni komanso akudalitseni.—Miy 10:22; Yes 41:10.
Onerani VIDIYO yakuti Tisamapusitsidwe ndi Mtendere Wosakhalitsa—Darrel ndi Deborah Freisinger. Kenako funsani funso ili:
Kodi mwaphunzira chiyani kuchokera kwa M’bale ndi Mlongo Freisinger pa nkhani yothetsa mavuto aakulu m’banja?
8. Phunziro la Baibulo la Mpingo
(30 min.) lfb mutu 22, mawu oyamba gawo 5 komanso mutu 23