OCTOBER 6-12
MLALIKI 5-6
Nyimbo Na. 42 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)
Aisiraeli akumvetsera mwatcheru pamene wansembe akufotokoza Chilamulo
1. Kodi Timasonyeza Bwanji Kuti Timalemekeza Mulungu Wathu Wamkulu?
(10 min.)
Tingasonyeze ulemu pamisonkhano tikamamvetsera komanso tikamavala ndi kudzikongoletsa moyenera (Mla 5:1; w08 8/15 15-16 ¶17-18)
Tikamapereka mapemphero a pagulu omwe si aatali komanso omwe ndi aulemu (Mla 5:2; w09 11/15 11 ¶21)
Tikamasungabe lonjezo lathu loti tidzatumikira Yehova (Mla 5:4-6; w17.04 6 ¶12)
2. Mfundo Zothandiza
(10 min.)
Mla 5:8—Kodi lembali lingatilimbikitse bwanji ngati tachitiridwa zinthu zopanda chilungamo? (w20.09 31 ¶3-5)
Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
3. Kuwerenga Baibulo
(4 min.) Mla 5:1-17 (th phunziro 12)
4. Ulendo Woyamba
(1 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Munthuyo akufuna kukangana nanu. (lmd phunziro 4 mfundo 5)
5. Ulendo Woyamba
(2 min.) KULALIKIRA M’MALO OPEZEKA ANTHU AMBIRI. Kambiranani nkhani imodzi yopezeka pagawo lakuti “Choonadi Chomwe Timakonda Kuphunzitsa Anthu” mu zakumapeto A, m’kabuku kakuti Muzikonda Anthu—Muziwaphunzitsa. (lmd phunziro 1 mfundo 3)
6. Ulendo Wobwereza
(3 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Gwiritsani ntchito vidiyo yopezeka pa Zinthu Zophunzitsira. (lmd phunziro 7 mfundo 3)
7. Kuphunzitsa Anthu
Nyimbo Na. 160
8. Kodi Mumagwiritsa Ntchito Gawo Lakuti “Choonadi Chomwe Timakonda Kuphunzitsa Anthu”?
(15 min.) Nkhani yokambirana.
Kungoyambira nthawi imene kabuku kakuti Muzikonda Anthu—Muziwaphunzitsa kanatuluka, kakhala kakutithandiza kuti tiwonjezere maluso athu pokambirana ndi anthu. Zakumapeto A m’kabukuka, zinakonzedwa kuti zizitithandiza kuyamba kukambirana ndi anthu mfundo zosavuta kumva za choonadi cha m’Baibulo. (Ahe 4:12) Kodi mumadziwa bwino nkhani zonse 9 zomwe zimapezeka pagawo lakuti “Choonadi Chomwe Timakonda Kuphunzitsa Anthu”?
Kodi tingayambe bwanji kukambirana ndi anthu mfundo yosavuta kumva ya choonadi cha m’Baibulo pamene tikucheza?—lmd zakumapeto A
Kodi ndi nkhani ziti zimene mwaona kuti ndi zothandiza kwambiri m’gawo lanu?
Kodi mungatani kuti mudziwe bwino malemba omwe ali mu zakumapeto A?
Tikamagwiritsa ntchito malembawa kawirikawiri mu utumiki, m’pamenenso tingawadziwe bwino kwambiri. Koma kuti tizitha kuwagwiritsa ntchito, choyamba tiyenera kuzolowera kulankhulana ndi anthu a m’dera lathu.
Onerani VIDIYO yakuti “Chitsulo Chimanola Chitsulo Chinzake”—Kulalikira Anthu Ambiri. Kenako funsani funso ili:
Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tizilankhula ndi anthu ambiri m’gawo lathu?
9. Phunziro la Baibulo la Mpingo
(30 min.) lfb mutu 24-25