Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wp22 No. 1 tsamba 8-9
  • 2 | Musamabwezere

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • 2 | Musamabwezere
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2022
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Baibulo Limati:
  • Zimene Lembali Limatanthauza:
  • Mmene Lembali Lingakuthandizireni:
  • Kodi Baibulo Limati Chiyani pa Nkhani ya Kubwezera?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Kodi Muyenera Kuchita Chiyani Mukakhumudwitsidwa?
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Ndinali Mnyamata Wovuta Komanso Wokonda Ndewu
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2016
  • Kodi Kubwezera Nkolakwa?
    Nsanja ya Olonda—1991
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2022
wp22 No. 1 tsamba 8-9
Azibambo awiri okwiya akhala moyang’anizana pa nthambi za mtengo. Aliyense akudula nthambi yomwe wakhalira.

KODI TINGATHETSE BWANJI CHIDANI?

2 | Musamabwezere

Baibulo Limati:

“Musabwezere choipa pa choipa. . . . Ngati ndi kotheka, khalani mwamtendere ndi anthu onse, monga mmene mungathere. Musabwezere, . . . pakuti Malemba amati: ‘“Kubwezera ndi kwanga, ndidzawabwezera ndine, watero Yehova.’”​—AROMA 12:17-19.

Zimene Lembali Limatanthauza:

Ngakhale kuti mwachibadwa anthufe timakwiya munthu wina akatilakwira, Mulungu safuna kuti tizibwezera. M’malomwake, iye amafuna kuti tizimuyembekezera moleza mtima chifukwa posachedwapa adzathetsa zinthu zonse zopanda chilungamo.​—Salimo 37:7, 10.

Mmene Lembali Lingakuthandizireni:

Popeza kuti anthufe tinabadwa ndi uchimo, tikamabwezera zoipa zimene anthu ena atichitira, zimangochititsa kuti chidani chizipitirira. Choncho, musamabwezere munthu wina akakulakwirani kapena akakuchitirani zoipa. Muziyesetsa kuugwira mtima komanso kuyankha modekha. Nthawi zinanso ndi bwino kungoisiya nkhaniyo. (Miyambo 19:11) Komabe, ngati pali zifukwa zomveka, nthawi zina mungachite bwino kuuza ena zomwe zakuchitikirani. Mwachitsanzo, ngati munthu wina wakuchitirani nkhanza zoopsa, mungasankhe kukanena nkhaniyo kupolisi kapena kwa akuluakulu ena m’dera lanu.

Anthu amene amakonda kubwezera amangodziika m’mavuto

Mungatani ngati zikukuvutani kuthetsa nkhaniyo mwamtendere? Nanga mungatani ngati mwayesapo kale kuthetsa nkhaniyo mwamtendere koma zikuvutabe? Musamabwezere. Zili choncho chifukwa kubwezera kungangokulitsa vutolo. Koma mukasankha kusabwezera mungathandize kuti chidani chisapitirire. Muzidalira Mulungu ndipo muzikhulupirira kuti iye ali ndi njira yabwino yothetsera mavuto. Baibulo limati: “Umudalire ndipo iye adzachitapo kanthu.”​—Salimo 37:3-5.

Zimene Zinachitikira Munthu Wina​—ADRIÁN

Anasiya Kubwezera

Adrián.

Adrián ali wachinyamata ankakonda kumenyana ndi anzake mumsewu pobwezera amene amulakwira. Iye anati: “Nthawi zambiri tinkawomberana ndi anthu moti maulendo angapo anthuwo ankaganiza kuti ndafa, ankandisiya mumsewu ndili thapsa nditasamba magazi.”

Adrián anayamba kuphunzira Baibulo ali ndi zaka 16. Iye ananena kuti: “Ndinapitiriza kuphunzira Baibulo ndipo ndinayamba kuona kuti ndikufunika kusintha khalidwe langa.” Iye ankafunikira kuthetsa chidani mumtima mwake komanso kusiya kuchita zachiwawa. Lemba limene linamuthandiza kwambiri ndi la Aroma 12:17-19 lomwe limatilimbikitsa kuti tisamabwezere. Adrián akufotokoza kuti: “Zimenezi zinandithandiza kuzindikira kuti Yehova adzathetsa zinthu zopanda chilungamo pa nthawi yake ndiponso m’njira yabwino. Patapita nthawi ndinasiya kukonda ndewu.”

Tsiku lina madzulo gulu la achinyamata lomwe linkakonda kumenyana ndi gulu la Adrián linayamba kumumenya. Mtsogoleri wawo ananena kuti: “Bwanji sukubwezera?” Adrián akunena kuti: “Ndinkafunitsitsa kubwezera.” Koma m’malo mobwezera iye anapemphera kwa Yehova mwachidule n’kuchokapo.

Adrián akufotokozanso kuti: “Tsiku lotsatira ndinakumana ndi mtsogoleri wawo uja ali yekha. Nditamuona ndinkafuna kuti ndibwezere zimene anandichita koma ndinapempheranso chamumtima kuti Yehova andithandize kuugwira mtima. Koma ndinadabwa kuona kuti anabwera pafupi n’kundiuza kuti: ‘Undikhululukire chifukwa cha zimene zinachitika dzulo zija. Inenso ndikufuna nditakhala ngati iweyo. Ndikufuna kuphunzira Baibulo.’ Ndinasangalala kwambiri kuti ndinakwanitsa kuugwira mtima chifukwa zinathandiza kuti nayenso ayambe kuphunzira Baibulo.”

Kuti mumve zambiri zokhudza mbiri ya moyo wa Adrián werengani magazini ya Nsanja ya Olonda Na. 5 2016, tsamba 14 ndi 15

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena