Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ijwfq nkhani 48
  • Kodi Munthu Atafuna Angasiye Kukhala wa Mboni za Yehova?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Munthu Atafuna Angasiye Kukhala wa Mboni za Yehova?
  • Mafunso Ofunsidwa Kawirikawiri
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Nanga bwanji ngati munthu wasiya kulalikira kapena kupita kumisonkhano yanu? Kodi mumamuona kuti wasiya kukhala wa Mboni?
  • Padzatsala Chipembedzo Chimodzi
    Galamukani!—1996
  • Kodi Mpingo wa Chikhristu Umayendetsedwa bwanji?
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Mverani Atsogoleri
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Kulondola Chipembedzo Choyera Kaamba ka Chipulumutso
    Nsanja ya Olonda—1991
Onani Zambiri
Mafunso Ofunsidwa Kawirikawiri
ijwfq nkhani 48
A man walks out of a Kingdom Hall

Kodi Munthu Atafuna Angasiye Kukhala wa Mboni za Yehova?

Ee. Munthu akhoza kusiya kukhala wa Mboni pogwiritsa ntchito njira ziwiri izi:

  • Kupempha. Munthu akhoza kulemba kalata kapena kungonena kuti sakufunanso kukhala wa Mboni za Yehova.

  • Zochita zake. Munthu angachite zinazake zomwe zingachititse kuti asakhalenso m’gulu lathu. (1 Petulo 5:9) Mwachitsanzo, munthuyo angalowe m’chipembedzo china n’kusonyeza kuti akufuna kupitiriza kukhala m’chipembedzocho.—1 Yohane 2:19.

Nanga bwanji ngati munthu wasiya kulalikira kapena kupita kumisonkhano yanu? Kodi mumamuona kuti wasiya kukhala wa Mboni?

Ayi, si choncho. Kusankha kusiya kukhala wa Mboni za Yehova n’kosiyana kwambiri ndi kungofooka. Nthawi zambiri, anthu amene asiya kupita kumisonkhano kapena kulalikira sikuti amakhala kuti akufuna kusiya kukhala a Mboni. Amakhala kuti angofooka chifukwa chokhumudwa ndi zinazake. Choncho timayesetsa kulimbikitsa ndiponso kuthandiza anthu oterewa. (1 Atesalonika 5:14; Yuda 22) Ngati munthu wotereyu akufuna kuthandizidwa, akulu amumpingo amamuthandiza mwauzimu.—Agalatiya 6:1; 1 Petulo 5:1-3.

Komabe udindo wa akulu si kukakamiza munthu kuti akhalebe wa Mboni za Yehova. Aliyense amasankha yekha pa nkhani ya chipembedzo. (Yoswa 24:15) Timakhulupirira kuti anthu ayenera kulambira Mulungu mwa kufuna kwawo komanso kuchokera mumtima.—Salimo 110:3; Mateyu 22:37.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena