Ziri Ponseponse Potizungulira!
“Mawu akuti ‘chipembedzo’ ndi ‘ndale zadziko’ anafalikira m’mbiri za nkhani kupyola 1984 yonse m’mbali zonse zadziko. . . . Bishopo wa Chianglican Desmond Tutu [anali] chizindikiro cha kuwombana pakati pa tchalitchi ndi ulamuliro pa nkhani ya tsankho la khungu . . . Pa kupereka madalitso pa msonkhano wa [ndale zadziko], Jerry Falwell, mtsogoleri wa ulamuliro wa Kukhala Bwino Kokomera Unyinji, anasonya kwa Reagan ndi wachiŵiri kwa Prezidenti George Bush monga ‘ziwiya za Mulungu za kumangiranso Amerika.’”—1985 Britannica Book of the Year.
“Kuchokera ku Poland kufika ku Philippines . . . Kuli abishopo ndi ansembe omwe akulankhula molimbana ndi Boma mu limene iwo amakhalamo. Tchalitchi sichiri kokha malo kumene Mulungu amalambiridwako, koma kumene kusamvana kumayambitsidwa.”—Glasgow Herald, January 3, 1985.
KODI mwakhala mukuŵerenga maripoti a nkhani zoterozo? Mwachidziŵikire mwatero, popeza kuti ambiri a ife tawona kuti chipembedzo ndi ndale zadziko ziri kaŵirikaŵiri zogwirizanitsidwa ndi nkhani. Kodi mumadzimva kuti chiri choyenera kaamba ka chipembedzo ndi ndale zadziko kusanganizana?
Ena anganene kuti, ‘Chipembedzo ndi ndale zadziko ziri nkhani zimene sindimakambapo.’ Ngakhale kuti mumadzimva tero, chiri kaamba ka chikondwerero chanu chabwino kuti mudziwitsidwe ponena za chimene chikuchitika kulinga ku chipembedzo ndi ndale zadziko ndi mmene ichi chingadzayambukirire moyo wanu weniweniwo. Ndiponso, mwakusonya ku Baibulo pa nkhaniyi, mudzapeza kuti Mulungu ali ndi zinthu zonena ponena za kulowerera kwa chipembedzo mu ndale zadziko ndi ponena za kumene icho chikutsogolera.
Kusanganizana kwa Dziko Lonse
Poyamba chidzakhala chothandiza kuwona kokha mmene kusanganizana kumeneku kwafalikira. Yang’anitsitsani maripoti ena a posachedwapa.
◼ April 21, 1986: “Mu Philippines Tchalitchi cha Chikatolika chasangalala ndi kumveka kwakukulu kaamba ka kuthandiza prezidenti wakale womveka kwambiri Ferdinand Marcos. Zipembedzo za Anglican, Methodist ndi Chikatolika mu South Africa zatsutsana kwa zaka zingapo molimbana ndi malamulo a boma a tsankho la khungu. Atsogoleri achipembedzo a Chikatolika mu Latin America, pansi pa kumveka kwa ‘nthanthi zaufulu,’ ali ophatikizidwa kwakukulu mu kuyesa kuchotsa ulamuliro womwe ukudidikiza osauka.”
◼ Seoul, Boma la Korea, March 9, 1986: “Mkulu wa Chipembedzo cha Chikatolika cha ku South Korea, Stephen Cardinal Kim Sou Hwan, wapereka chichirikizo chake lerolino ku zifuno za chipani chotsutsa kaamba ka kusintha kwa mwamsanga kwa malamulo.”
◼ August 18, 1986: ‘Wophunzira ali wokhazikitsidwa ndi minisitala msilikari wa Chiprotestanti, womenyera kutulutsa chipani chake kuchokera ku kudidikizidwa kochepa komwe iye amada. Kodi ndani uyu amene ali magwero odzidzimutsa ndi ogwedeza mu ndale zadziko za uprezidenti wa mu U.S.? Mophiphiritsira, kulongosolako kumagwira ntchito bwino lomwe kwa akulu achipembedzo aŵiri: Pat Robertson ku Republiki la ku lamanja ndi Jesse Jackson ku Demokratiki wa kumanzere.’ ‘Kalata yosonkhetsa ndalama kuloza ku kupambana [kwa Robertson] kwa wophunzira wopezekapo kunali kutayambidwa “Akristu apambana! . . . Ndi kupambana kotani nanga kwa Ufumu!”’
◼ Brasília, Brazil, July 3, 1986: “Chipembedzo chatuluka kale monga chotsutsa champhamvu cha Boma latsopano la anthu wamba . . . Monga chotulukapo, unansi wa chipembedzo ndi boma uli kachiŵirinso pa ngozi, wokhala ndi nduna zikupatsa mlandu ansembe kaamba ka kusintha mkhalidwe m’mbali za dziko ndipo mabishopo ena akutsutsa boma kaamba ka kusinthira ku nzeru za ‘kuzunza ndi kufooketsa.’”
◼ September 25, 1984: “Khomeini wa ku Iran aimirako magwero a ziphunzitso za Shia za Chisilamu ndipo aphunzitsa kuti Chisilamu chifunikira kulamulira ndale zadziko, ndalama ndi kuwunikira kwa gulu la nkhondo.”
◼ April 7, 1985: “Ochuluka a Chianglican akulingalira kuti tchalitchi cha ku England chifunikira kusatengamo mbali mu ndale zadziko, kulingana ndi Kuvota kwa Chisawawa kochitidwa konse kwa The Sunday Telegraph.”
◼ October 4, 1986: “Tchalitchi cha Chikatolika cha ku Mexico chikundandama kumbuyo kwa kutsutsa komakulakula kwa [chipani] cholamulira cha dziko. Tchalitchi chinapanga malonda ake a akulu mu ndale zadziko mu July . . . Mabishopo anafuna kuchotsapo misa ya pa Sande monga njira ya kutsutsira pa mzere wokavota; koma Papa analowereramo.”
◼ Washington, D.C., U.S.A., July 6, 1986: “Atsogoleri Achikristu a chievangeli akugwiritsira ntchito ndalama zawo, chikhulupiriro chawo chauzimu ndi mamiliyoni a ziwalo kaamba ka kumenyana kwapoyera—ndipo akuchita mbali yosonkhezera mowonjezereka mu ndale zadziko za ku Amerika.”
Nchifukwa Ninji Ziri Tero?
Inde, palibe kukana ponena zakuti chipembedzo chiri chophatikizidwa kwenikweni mu ndale zadziko. Koma kodi nchiyani chimene chimapangitsa atsogoleri a zipembedzo kusanganizana mu nkhani za ndale zadziko? Kodi Mulungu wapereka chiweruzo chirichonse pa kusanganizana kumeneku? Kodi zonsezi zikutsogolera kuti, ndipo kodi inu mudzayambukiridwa motani?
[Bokosi patsamba 3]
“Kulowerera kwa ndale zadziko kuli kowonekera mu Uthenga Wachikristu, watero [Peter-Hans Kolvenbach,] mtsogoleri wa Society of Jesus, . . . yemwe papitapo wakhala pansi pa moto kuchokera ku Vatican kaamba ka kusanganizana kwambiri mu nkhani za ndale zadziko.”—The Toronto Star, May 31, 1986.