Kulabadira Chenjezo Kungapulumutse Moyo Wanu
CHENJEZO lingakhale chizindikiro cha pa msewu chonena kuti “Slow,” “Caution,” kapena “Yield”; kapena ingakhale nyali yowalima yachikasu. Lingapezeke pa choikamo mankhwala kapena ululu. Kulabadira machenjezo oterowo sikuli kusokoneza kwakukulu ndipo kungapulumutse moyo wanu.
Komabe, m’nkhani zina kungatanthauze kuwononga kwa makonzedwe kapena kutaya zinthu zakuthupi. Machenjezo a namondwe ndi mphepo yaikulu angafune asodzi a nsomba kubwerera kumtunda kapena kukhala pa doko ndipo osagwira ntchito tsiku limenelo. Machenjezo samangotanthauza kokha kuwononga kwa makonzedwe koma kusiya nyumba ndi zinthu zakuthupi, kapena kupirira kukhala kosayenera mu misasa yapakanthaŵi. Nthaŵi zina machenjezo oterowo samalabadiridwa, ndi chotulukapo chotaya moyo.
Mwachitsanzo, m’ngululu ya chaka cha 1902, zinthu zonse zinali kuyenda bwino pachisumbu chokongola cha Caribbean cha Martinique. Kenaka machenjezo a tsoka anayamba kuwoneka pa Phiri la Pelée, phiri la tanthwe lotentha lokhala chifupifupi pa mtunda wa mamailosi asanu (8 km) kuchokera ku St. Pierre, Mzinda waukulu wa chisumbucho, linayamba kugwira ntchito. Kenaka, pamene utsi, phulusa, ndi miyala yaing’ono inawulutsidwa limodzi ndi utsi wonunkha, anthu a mtauni anakhala ozindikira. Mkhalidwe unapitiriza kuipiraipirabe, ndipo chinayenera kukhala chodziwikiratu kuti tsoka lenileni linali nkudza.
Machenjezo Osalabadiridwa
Chifukwa chakuti kukolola kwa nzimbe kunali kuyandikira, anthu amalonda a ku St. Pierre anatsimikizira anthu kuti kunalibe tsoka. A ndale zadziko, odera nkhaŵa ndi chisankho chomwe chinali nkudza, sanafune kuti anthuwo adzithawa, chotero analankhula m’njira imodzimodziyo. Atsogoleri achipembedzo anagwirizana mwa kuuza ansembe awo kuti zonse zinali bwino. Kenaka, pa May 8, Phiri la Pelée linaphulika ndi phokoso lalikulu. Mitambo yotentha kwambiri yakuda inathamanga kulinga ku St. Pierre, ndipo anthu 30,000 anafa.
Kwa mibadwo yambiri Phiri la St. Helens, lokhala mu boma la Washington, U.S.A., linali chithunzi cha bata ndi mtendere. Malowo anali odzazidwa ndi mitundu yosiyanasiyana ya nyama za mthengo ndipo anali malo abwino a kuchezera ndi kusodza nsomba. Koma kenaka mu March 1980, zizindikiro za tsoka zinabwera mu mkhalidwe wa zivomezi zambiri ndi kuphulika kwakung’ono kwa nthunzi. Pofika kumayambiriro kwa May phirilo linali kugwira ntchito ndi mphamvu yaikulu. Nduna zakumaloko ndi za m’dziko zinayamba kupereka machenjezo a tsoka kwa awo omwe anali m’malo a matanthwe otentha a pansi pa nthaka.
Komabe, anthu ambiri anatsala m’malowo, pamene ena ananyalanyaza zizindikiro za chenjezo zotsutsa kuoloka kupita ku malo a tsoka. Mwadzidzidzi, pa Sande m’mawa, May 18, kunali kuphulika kwakukulu kumene kunachotsa mapazi 1,300 (400 m) a pamwamba pa phiri ndi kubweretsa chiwonongeko pa zomera ndi nyama, limodzinso ndi anthu 60 omwe analephera kulabadira machenjezo opatsidwa.
Mosiyanako, mu November 1986, Phiri la Mihara pa chisumbu cha Izu-Oshima, mu Japan, linaphulika mwadzidzidzi, kuopsyeza chisumbu chonse limodzi ndi unyinji wa anthu akewo zikwi khumi okhala pa chisumbu ndi alendo ochezera dziko. Pamene chilengezo chakuti, “Chokani tsopano!” chinabwera, analabadira chenjezolo. Nkhani zotsatirazi zochokera kwa mlembi wa Galamukani! mu Japan zikukamba nkhaniyo.