Kodi Mapeto a Dziko Oloseredwa Ali Pafupi?
DETROIT Free Press Magazine ya February 6, 1994, inati: “Malingaliro a chiwonongeko chotheratu anakhala nkhaŵa yaikulu pamene nyengo ya nyukiliya inayamba. Pambuyo pa kuphulitsidwa kwa Hiroshima pa Aug. 6, 1945, kunali kwachionekere kwa aliyense kuti: Dziko likhozadi kutha tsopano!”
M’December wapita, Charles B. Strozier, katswiri wa psychoanalysis wa ku New York ndi profesa wa mbiri yakale, anati: “Sitifunikiranso andakatulo kutiuza kuti anthu onse akhoza kuzimiririka kamodzinkamodzi, kapena mwakachetechete, kapena ndi nsautso ya AIDS.” Ndiponso, iye anawonjezera kuti: “Tsopano kusaganiza kuti anthu akhoza kutha kungakhale kulota kwambiri.”
Popeza kuti Yesu Kristu anaphunzitsa kuti dziko lidzatha, kodi tingapeze umboni wakuti mapeto alidi pafupi m’ziphunzitso zake?
Mapeto—Liti?
Ophunzira a Yesu anamfunsa za “chizindikiro” chosonyeza pamene dzikoli, kapena dongosolo la zinthu, lidzatha. “Zija zidzaoneka liti?” iwo anafunsa motero, “ndipo chizindikiro cha [kukhalapo, NW ] kwanu nchiyani, ndi cha mathedwe a nthaŵi ya pansi pano?” (Mateyu 24:3) Mungapende “chizindikiro” chimene Yesu anapereka poyankha funsoli. Chalembedwa m’Baibulo mu Mateyu chaputala 24, Marko chaputala 13, ndi Luka chaputala 21. Zochitika zina zazikulu zopanga chizindikirocho nzotere:
NKHONDO ZAZIKULU: “Mtundu umodzi wa anthu udzaukirana ndi mtundu wina, ndi ufumu ndi ufumu wina.” (Mateyu 24:7) Ife taonadi mbali imeneyi ya chizindikiro ikukwaniritsidwa. “Nkhondo Yadziko Yoyamba [yoyamba mu 1914] inali nkhondo yoyamba ‘yomenyedwa ndi onse,’” anatero wolemba mbiri wina. Komabe, Nkhondo Yadziko II inali yoipirapo kwambiri, ikumapha anthu pafupifupi 50 miliyoni. Ndipo nkhondo zikusakazabe dziko lapansi.
NJALA: “Kudzakhala njala.” (Mateyu 24:7) Pambuyo pa Nkhondo Yadziko I panatsatira njala yowopsa, ndipo chiyambire pamenepo njala yapitiriza kufalikira kumadera ambiri a dziko lapansi. Ngakhale m’maiko olemera, njala ndi matenda a njala zili zofala.
ZIVOMEZI ZAZIKULU: “Kudzakhala zivomezi zazikulu.” (Luka 21:11) Tangolingalirani zingapo zokha zazikulu: mu 1920, China, 200,000 anaphedwa; mu 1923, Japan, miyoyo 143,000 inatayika; mu 1970, Peru, 66,800 anaphedwa; ndipo mu 1976, China, 240,000 (ena amati 800,000) anafa. Katswiri wa uinjiniya wopanga njira zoletsera kuwononga kwa chivomezi anatcha chivomezi cha mu 1976 cha ku China “tsoka la chivomezi lalikulu koposa m’mbiri ya anthu.”
MATENDA: “Miliri m’malo akutiakuti.” (Luka 21:11) Nkhondo Yadziko I itangotha, anthu pafupifupi 21 miliyoni anafa ndi fuluwenza ya Spanya. Science Digest inasimba kuti: “Imfa sinafalikirepo mwamsanga ndi mosalekeza chotero m’mbiri yonse ya anthu.” Chiyambire pamenepo, nthenda ya mtima, kansa, AIDS, ndi matenda ena apha anthu miyandamiyanda.
UPANDU: “Kuchuluka kwa kusayeruzika.” (Mateyu 24:12) M’maiko ambiri upandu uli wosalamulirika. Mbanda, kulanda, kugwirira chigololo, uchigaŵenga, ziphuphu—masiku onse timamva za maupandu otero kapena amatichitikira ife enife.
Maulosi ena a Baibulo analoseranso za mikhalidwe imene inali kudzakhalako m’masiku otsiriza. Mwachitsanzo, m’buku la Chivumbulutso, muli masomphenya a okwera pa akavalo anayi. (Chivumbulutso 6:1-8) Wapakavalo woyamba amaimira Yesu mwiniyo monga Mfumu yolakika. Apakavalo enawo ndi akavalo awo aimira zochitika pa dziko lapansi zosonyeza chiyambi cha ulamuliro wa Yesu: nkhondo, njala, ndi imfa yosayembekezera yobwera m’njira zosiyanasiyana.
Ndiponso maulosi ena a Baibulo amafotokoza za mzimu ndi mikhalidwe imene inali kudzafala mkati mwa “nyengo yomaliza ya dziko ili.” Talingalirani zimene mtumwi wina wa Yesu analemba. Pamene mukuŵerenga ulosi umenewu, dzifunseni kuti: Kodi zimenezi sizikufotokozadi nthaŵi zovuta za lero?
“Nyengo yomaliza ya dziko ili,” analemba motero mtumwiyo, “idzakhala nthaŵi ya mavuto. Anthu sadzakonda china chilichonse koma ndalama ndi iwo eni; adzakhala odzikuza, onyada, ndi amwano; opanda ulemu kwa makolo, osayamika, osakhulupirika, opanda chikondi chachibadwa; adzakhala osakhoza kusintha pa maudani awo, akazitape, aukali ndi owopsa, alendo pa zabwino zonse, amdyera kuŵiri, akandifere, otupa nako kudzikweza. Adzakhala anthu oika zokondweretsa m’malo mwa Mulungu, anthu odzionetsera kunja ngati a chipembedzo, koma okana choonadi chake nthaŵi zonse.”—2 Timoteo 3:1-5, The New English Bible.
Ulosi wina wofunika wa mapeto a dzikoli ndi uja wolonjeza kuti Mulungu ‘adzawononga iwo akuwononga dziko.’ (Chivumbulutso 11:18) Anthu a mibadwo yapita analibe mphamvu ya sayansi yopanga zinthu yowonongera dziko lapansi, koma tsopano ali nayo. Ndipo lerolino zinthu zatsopano zopangidwa ndi sayansi zikuthandizira kwambiri kuipitsa malo. Mu November 1992, manyuzipepala anali ndi mitu ya nkhani yonga uwu: “Asayansi Apamwamba Achenjeza za Kuwonongeka kwa Dziko Lapansi.”
Zindikirani Ulosi Woona
Palibe kukayikira kulikonse. Zinthu zonse zimene Baibulo linalosera kuti zidzachitika mu “nyengo yomaliza,” kapena “mathedwe a nthaŵi ya pansi pano,” zikuchitika pakali pano. Tikuuona ulosi woona ukukwaniritsidwa, ndipo nkofunika kwambiri kuti tiulabadire. Yesu anasonyeza zimenezi pofotokoza mkhalidwe wa masiku a Nowa, “mlaliki wa chilungamo,” dziko la panthaŵiyo litangotsala pang’ono kutha.—2 Petro 2:5.
Yesu analongosola kuti: “Monga m’masiku aja, chisanafike chigumula, anthu analinkudya ndi kumwa, analikukwatira ndi kukwatiwa, kufikira tsiku limene Nowa analoŵa m’chingalaŵa, ndipo iwo sanadziŵa kanthu, kufikira kumene chigumula chinadza, chinapululutsa iwo onse, kotero kudzakhala [kukhalapo, NW ] kwake kwa Mwana wa munthu.” (Mateyu 24:38, 39) Pamene ulosi woona unyalanyazidwa, pamakhala zotsatirapo zoipa.
Mwinamwake mukunena kuti, ‘Inde, ndikukhulupirira maulosi a Baibulo ameneŵa; mapeto adzadza tsiku lina, koma akali kutali.’ Komabe, kodi ndinu wotsimikiza? Kodi simuyenera kulabadira chenjezolo tsopano lino?
Machenjezo Oyenera Kulabadira
Mwachionekere, machenjezo ena alibe maziko, ndipo kungakhale kupusa kuwalabadira. Koma ena ali nawo. Chabe chifukwa chakuti ambiri, kuphatikizapo anthu otchuka kumaloko, amachepsa chenjezo, sindicho chifukwa cholinyalanyazira. Talingalirani chitsanzochi.
Munali m’March 1902, ndipo pachilumba chokongola cha ku Caribbean cha Martinique, Phiri la Pelée la volokano linayamba kutukusira. Pofika mu April, utsi, phulusa, ndi timiyala zinatuluka limodzi ndi mpweya woŵaŵa. Nzika za mzinda wa St. Pierre, wokhala pa mtunda wa makilomita asanu ndi atatu, zinada nkhaŵa. “Mzinda wadzala phulusa,” nzika ina inalemba motero. “Anthu ambiri akukakamizika kuphimba mphuno zawo ndi nsalu zominira zonyoŵa kudzitetezera ku mpweya wopuyitsawo.”
Kuchiyambi kwa May kutukusira kwa volokano imeneyo kunawonjezereka. Nyuzipepala yakumaloko inati: “Mvula yaphulusa siikutha . . . Kuyenda kwa ngolo sikukumvekanso m’makwalala. Magudumu ake sakumvekanso.” Kutentha kwake kunali kopuyitsa.
Ndiyeno, pa May 5, volokanoyo inatulutsa matope otentha amene anapha anthu ambiri okhala m’njira mwake. Koma kodi akuluakulu a mzindawo anati bwanji?
Nthaŵi yakudula nzimbe inali kuyandikira, ndipo eni mabizinesi anauza anthu kuti panalibe chowopsa kwenikweni. Ngakhale andale, pofuna chisankho chomwe chinali kudzachitika pa May 10, sanafune anthuwo kuthaŵa. Chotero nawonso anayesa kuchotsa mantha mwa anthuwo. Ndiponso, atsogoleri achipembedzo anamvana ndi amabizinesi ndi andale nanyengerera anthu awo kusachoka.
Ndiyeno panachitika zowopsa. Pa May 8, itangotsala pang’ono kukwana 8:00 a.m., Phiri la Pelée linaphulika ndi kulilima kogonthetsa m’kutu. Mitambo yaikulu yakuda bii, yotentha kwadzaoneni inayenda ndi liŵiro losaneneka kulinga ku St. Pierre. Posapita nthaŵi mpweya wotenthawo unapha miyoyo ya anthu zikwizikwi. Tingonena kuti onse mu St. Pierre anafa—anthu 30,000 kapena kuposapo. Munthu yekha yemwe anapulumuka anali mkaidi wachichepere yemwe anali m’lumande yapansi pa ndende.
Mkhalidwewo Lerolino
Momwemonso lerolino, pali ambiri amene amachepsa umboni wakuti maulosi a Baibulo akukwaniritsidwa. Iwo amakana kulabadira umboni umene uyenera kukhutiritsa munthu aliyense wanzeru wakuti mapeto a dongosolo ili ali pafupi. Komabe, Baibulo linaloseradi za mzimu wawo, likumati: “Masiku otsiriza adzafika onyoza ndi kuchita zonyoza, oyenda monga mwa zilakolako za iwo eni, ndi kunena, Lili kuti lonjezano la [kukhalapo, NW ] kwake? Pakuti kuyambira kuja makolo adamwalira zonse zikhala monga chiyambire chilengedwe.”—2 Petro 3:3, 4.
Koma onyoza alerolino ngolakwa. Choonadi nchakuti, zinthu zasintha. Maulosi a Baibulo ali kukwaniritsidwa. Umboni wakuti mapeto ali pafupi ngwochuluka.
Mwanzeru, musazengereze kuchitapo kanthu kupulumutsa moyo wanu. Koma kodi mufunikira kuchitanji?
[Mawu a Chithunzi patsamba 26]
Chithunzithunzi cha U.S. National Archives
[Mawu a Chithunzi patsamba 26]
WHO/E. Hooper
[Mawu a Chithunzi patsamba 27]
Chithunzithunzi cha WHO chojambulidwa ndi W. Cutting