“Chokani Tsopano!”
Ndi mlembi wa “Galamukani!” mu Japani
Kutuluka kwa Anthu Zikwi Khumi Usiku Wonse
“CHOKANI tsopano! Tsopano lino!” Amuna ndi akazi okalamba a mu Nyumba ya Nzika Zachikulire mu Oshima anauzidwa kuthaŵira ku sukulu yapafupi chifukwa cha kuphulika kwa Phiri la Mihara pa November 21, 1986. Ngakhale kuti ogwira ntchito mu nyumbayo anakonzekeretsedwa kuchoka pamene matanthwe otentha a pansi pa nthaka anayamba kugwira ntchito masiku ochepa oyambirirawo, kuphulika kwa mwadzidzidzi masana amenewo sikunapangitse icho kukhala chopepuka kwa iwo kuthawa.
“Sitinaganizire nkomwe za machira omwe tinakonza,” akulongosola Kazuko, chiwalo cha ogwira ntchito pa nyumbayo. “Tinatenga okalamba m’manja athu kapena kuwabereka kumsana kwathu ndi kuwapereka ku mabasi aŵiri omwe ofesi ya mzinda inatumiza kunyumbayo. Awa anadzazidwa mwamsanga, ndipo anthu ena ananyamulidwa ndi magalimoto akulu kupita ku msasa.”
Pa nthaŵi yabwino achikulirewo anafika pa doko ndipo anaikidwa m’bwato la Maritime Safety Agency kuti achoke pa chisumbucho. Anali pakati pa oyambirira kuchoka. Kuchoka kwa anthu oposa zikwi khumi za anthu okhala pa chisumbu ndi anthu odzacheza mmalowo kunatsatira.
Zivomezi ndi Kuphulika
Phiri la Mihara pa chisumbu cha Izu-Oshima, kaŵirikaŵiri lotchedwa Oshima, liri limodzi la matanthwe otentha a pansi pa nthaka anayi achangu omwe ali pansi pa chiyang’aniro chosamalitsa mu Japani. Ilo lakhala lodziŵika chifukwa cha machitidwe ake odekha. Pa November 15, 1986, ngakhale kuli tero, phirilo linaphulika kokha milungu iŵiri pambuyo pakuti msonkhano wa kulosera kwa Kuphulika kwa Matanthwe otentha a Pansi pa Nthaka unalengeza kuti phirilo linali lachisungiko. Kuphulika kuchokera ku chiboo choyambirira cha pakati pa matanthwe otentha a pansi pa nthaka (crater) kunapitiriza kuwonjezeka. (Onani mapu pa tsamba 6.) Matope anayenda mu mkombero wamkati mwachiboo chimenechi ndikudzafika pa chiboo chachikulu (caldera) cha tanthwe lotentha la pansi pa nthaka. Kenaka, pa 21, kuphulika kosayembekezereka kunadzidzimutsa anthu okhala pa chisumbu. Chiboo chatsopano pakati pa mwala wotentha wa pansi pa nthaka chinapangika. Ichi chinatsatiridwa ndi kuphulika kochokera m’ming’ankha ya pansi ikutulutsa akasupe a moto opambana pa mapazi 330 (100 m). Akasupe a moto atsopano anatuluka pamene ming’ankha inapitiriza kutseguka mu mphepete mwa phirilo.
Zivomezi zinagwedeza anthu amene anali owopsyedwa kale ndi kuphulika. Mkati mwa ora limodzi, zivomezi 80 zinagwedeza chisumbucho. Matope osefukira kuchokera mu mkombero wakunja kwa chiboo cha tanthwe lotentha la pansi pa nthaka anatsetserekera pansi pa phiri ndikuyenda kumalo komwe kunali anthu ambiri ku dera la Oshima, Motomachi. Matope oyenda kulinga ku Motomachi anasonkhezera Hidemasa Uemura, nduna ya mzinda kulamulira kuchoka kwa anthu okhala pa chisumbu kuchokera ku Motomachi. Panthaŵi imeneyi, mbali ya kummwera kwa chisumbucho, gawo la Habu, linalingaliridwa kukhala lachisungiko.
‘Kuphimba kwa Mtambo Konga Bowa Konga Kuja kwa Kuphulika kwa Bomba la Atomu’
“Tinali kumwa tii,” akukumbukira Jiro Nishimura, Mkulu yekha mu mpingo wa Mboni za Yehova wa Izu-Oshima. “Kenaka, kuphulika kwakukulu kunagwedeza mphepo. Pamene ndinapita panja, panali mtambo wonga bowa pamwamba pa Phiri la Mihara wonga uja wa kuphulika kwa bomba la atomu. Ndinazindikira kuti iko sikunali kuphulika kwamaseŵera. Ndinamva chinachake pa chokuzira mawu cha ofesi ya mzinda, koma chifukwa sindinali kumva bwino chilengezocho, ndinatumiza lamya ku ofesi ya mzinda. Iwo ananena kuti nzika za mdera la Motomachi sizinali kulangizidwa kuchoka. Ndinazindikira kuti tinafunikira chinachake chakudya, chotero ndinafunsa mkazi wanga kuphika mpunga ndikupanga nthongo za mpunga. Koma ndisanamalize nkomwe kudya nthongo yanga yoyamba ya mpunga, lamulo la kuchoka linaperekedwa.
“Asanu a ife, kuphatikizapo amayi a mkazi wanga, amene ali ndi zaka 90, tinathaŵira ku Doko la Motomachi. Anthu anapanga mzera kuti akwere bwato kuchoka pa chisumbu. Mzera unali wautali, koma popeza amayi a mkazi wanga anali okalamba ndipo sankatha kuyenda okha, tinaloledwa kukwera bwato loyambirira kupita ku Atami.”
Kwa ena, sichinali chopepuka kusiya chisumbu chimene anali anazoloŵerana nacho kwambiri. Kichijiro Okamura, wa zaka 84, sing’anga wa pa Nyumba ya Nzika Zachikulire ya mu Oshima, wakhala pa Oshima kwa zaka 40. Okamura akulongosola malingaliro ake: “Zivomezi zinali zoipitsitsa, koma ndinalingalira kuti zinali bwino ndipo ndinafuna kuwona mmene zinthu zikayendera kwa masiku ochepa. Ndiri wozoloŵerana ndi kuphulika ndi zivomezi. Sindinadere nkhaŵa kwakukulu chifukwa ndinadziwa kuti zidzazimiririka. Koma amuna ozima moto ananditenga ine mokakamiza ndi kundipangitsa ine kuchoka. Ndinayenera kugonjera.” Anachoka limodzi ndi mkazi wake Yoshie, ana awo a akazi aŵiri, ndi adzukulu anayi.
Lamulo la Kuchoka kwa Chisumbu Chonse
Pachiyambi, kuyenda kwa matope kunawopsyeza kokha mbali ya kumpoto ya chisumbucho. Ena omwe amakhala ku dera la Motomachi anaperekedwa kudera la Habu. Nzika za mbali yakum’mwera kwa chisumbucho zinangouzidwa kusonkhana pa malo ochitirapo maseŵera olimbitsa thupi kapena masukulu.
“Koma ndinali ndi mabulangeti aŵiri ndi chola ichi,” akunena tero Kaoko Hirakawa, amene anathaŵira ku malo ochitirapo maseŵera olimbitsa thupi ku Nomashi pa 5:00 p.m. “Ndinaganizira kuti tidzakhala kokha usiku wonse.” Mwamuna wake Rinzo anaganizira za makolo ake odwala omwe amakhala pafupi ndi chiboo chatsopano pa matanthwe otentha a pansi pa nthaka. Modera nkhaŵa, anakwera m’galimoto kukatenga makolo ake. “Zivomezi zinali zazikulu,” akunena tero Rinzo. “Chinali monga ngati takwera bwato. Mwamsanga pamene tinaika makolo anga m’galimoto, kokha makilomita ochepera kuchoka panyumba ya makolo anga nthaka inaphulika.” Anakhoza kufika pa malo ochitirapo maseŵera olimbitsa thupi ku Nomashi, koma kenaka anauzidwa kupita ku Habu.
Pa 10:50 p.m. nduna yamzinda inalamula kuti chisumbu chonse chichokedwe. “Tinathaŵira ku Third Junior High School mu Habu,” Mrs. Tamaoki akutero. “Kenaka tinauzidwa kuyenda kupita ku doko. Koma Doko la Habu linali losazama kwambiri kaamba ka mabwato akulu, ndiyeno pomalizira tinakwera basi kupita ku Motomachi komwe tinakwera bwato kupita ku Tokyo.”
Ulendo wa anthu oposa zikwi khumi okhala pazisumbu ndi anthu odzachezera dziko unamalizidwa pa 5:55 a.m., November 22, ndi nduna ya mzinda ndi akuluakulu akukwera bwato lomaliza la anthu ochotsedwa kaamba ka mavuto. Kuchoka kwa Izu-Oshima kunamalizidwa m’maora asanu pambuyo pakuphulika kwakukulu. Chinachitika bwino mwamya ndipo mwadongosolo ku mbali yaikulu, kuchiyamikiro cha nduna za mu mzinda, kampani yotumiza katundu yomwe inatumiza masitima ku Oshima kaamba ka ochoka, ndi kugwirizana kodzipereka kwa anthu okhala pa chisumbuwo. Kokha ndi kusiyana kochepa, iwo analabadira lamulo la kuchoka osazengeleza. Kokha mazana ochepa a apolisi, amuna ozima moto, ndi anthu ena ogwira ntchito anakhala pa chisumbucho, pamodzi ndi chiŵerengero chochepera cha aja omwe anakana kuchoka.
Koma kodi nkuti komwe anthu ochokawo anakhala? Kodi ndani omwe adzawasamalira? Kodi ndimotani mmene Mboni za Yehova zinakhalira pa chisumbucho?
[Chithunzi/Mapu patsamba 21]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
OSHIMA
MT. MIHARA
Tokyo
Shimoda
Inatori
Sakurajima
Ito
Atami
Ebina
[Chithunzi] Oshima
Okata
Kitanoyama
Matope oyenda
Chiboo cha pakati Na.2
Kuphulika
Chiboo cha pakati Na.1
Mkombero wakunja wa chiboo cha pakati
Sashikiji
Port Habu
MT. MIHARA
Nomashi
Motomachi
Bwalo la ndege
[Chithunzi patsamba 19]
“Amuna ozima moto ananditenga ine mokakamiza ndipo anandipangitsa kuchoka”