Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g88 4/8 tsamba 24-28
  • Malamulo aku United States ndi Mboni za Yehova

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Malamulo aku United States ndi Mboni za Yehova
  • Galamukani!—1988
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kupeza Kuyenera kwa Aliyense
  • Alaliki kapena Amalonda?
  • Kuchita Sawatcha ku Mbendera
  • Kuthandiza kwa Mboni
  • Zochitika m’Mbiri ya Ufulu wa Kulankhula
    Galamukani!—1996
  • Khoti Lalikulu Ligamula Kuti Pakhale Ufulu Woyankhula
    Galamukani!—2003
  • Kuteteza Uthenga Wabwino Mwalamulo
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Kodi Ufulu wa Chipembedzo Umatanthauzanji kwa Inu?
    Nsanja ya Olonda—1997
Onani Zambiri
Galamukani!—1988
g88 4/8 tsamba 24-28

Malamulo aku United States ndi Mboni za Yehova

Chaka cha 1987 chimafikitsa kukumbukira kwa chi-200 kwa Lamulo la United States. Pokhala ndi chisamaliro chikuperekedwa ku chikumbukiro cha mazana aŵirichi, Mboni za Yehova mu United States ndi kuzungulira dziko lonse zikukumbutsidwa za kumenyera kwawo mu dzikolo kuchinjiriza ndi kukhazikitsa mwalamulo kuyenera kwawo kwa kufalitsa malingaliro a chipembedzo chawo.

KODI Lamulo limatanthauzanji kwa inu? Kuchitira chitsanzo, yerekezani kuti m’mudzi mwanu inu munafuna kugawira m’makwalala ndi kuchokera kunyumba ndi nyumba chidziŵitso chosindikizidwa chomwe mudadzimva kuti chinali chodetsa nkhaŵa kwa anthu. Koma bwanji ngati munadziŵa kuti kugawira zofalitsidwazo kunali kuswa kwa lamulo loikidwa kutsimikizira mtendere waunyinji ndi chilongosoko chabwino? Kapena bwanji ngati inu mukafunikira kupempha chilolezo cha kuchita tero, ndipo nduna sizinakhoze kukupatsani? Kapena ngati munafunikira kugula laisensi ndipo kuchita tero kukatanthauza kudidikiza kwa za chuma kwa inu?

Uwu unali mkhalidwe umene Mboni za Yehova zinadzipeza izo zeni kumbuyoko m’ma-1930 ndi ma-1940. Iwo anafuna kugawira zinthu zosindikizidwa zokhala ndi kawonedwe ka chipembedzo chawo. Komabe, m’mbali zambiri malamulo a kumaloko ndi zogamula zinkagwiritsiridwa ntchito kuwaletsa iwo. Chotero, apilu inapangidwa pa magwero a Lamulo la U.S., lomwe limatsimikizira ufulu wa kulankhula ndi kudzilongosolera. Koma m’malo mofuna kuchinjiriza kuyenera kwa malamulowa, iwo anafunikira kutenga nkhaniyo ku bwalo la milandu. Tiyeni tiwone mmene Lamulo linaperekera kuyenera kwa aliyense.

Kupeza Kuyenera kwa Aliyense

Molingana ndi kugamula kulikonse, lamulo limapanga kachitidwe ka kukwaniritsa chinachake—m’kayang’anidweka boma la anthu. Monga momwe chinalongosoledwera m’Kulongosola kwa Ufulu wa Kudzilamulira kwa United States, maboma amapangidwa pakati pa anthu kusungilira kaamba ka zolamuliridwa zina za “Kuyenera kosakhala kwa kunja.”

Mawu Otsegulira a Lamulo la ku U.S. ali ndi mutu umenewu ndipo amalongosola kuti Lamulolo linasankhidwa ndi kukhazikitsidwa kusungilira “Madalitso a Ufulu” kaamba ka anthu. Kulembedwa kotsirizira kwa Lamulolo kunatsirizidwa pa Independence Hall mu Philadelphia, Pennsylvania, pa September 17, 1787. Lamulo limeneli liri lachilendo chifukwa chakuti liri Lamulo lolembedwa kale kwambiri lomwe lidakali kugwira ntchito.

Lamulo la U.S. ladziŵika kaamba ka kusakhulupirira kwake maboma amphamvu kwambiri ndi kutukula kwake ufulu wa aliyense popanda kusokonezedwa ndi boma. Pakati pa mbali zodziŵika bwino kwambiri za Lamulolo ziri kutsimikizira kwake kwa ufulu wa chipembedzo, ufulu wa kulankhula, ndi ufulu wa kudzilongosolera. Maufulu amenewa sanalongosoledwe mu Lamulolo poyamba kukhala atalembedwa ndi kuvomerezedwa. Iwo anawonjezeredwa mu 1791 monga khumi oyambirira kukonzedwanso, odziŵika mofala monga Ndandanda ya Kuyenera.

Maufulu olongosoledwa mu Ndandanda ya Kuyenera ali a aliyense payekha ndipo sali kaya odalira pa chilolezo cha boma kapena okhoza kusinthidwa ndi boma. Ngati ndi tero, nchifukwa ninji, chimene anthu afunikira kumenyera kaamba ka kuyenera kwawo m’mabwalo a milandu? Chifukwa chakuti panthaŵi zina mabungwe a malamulo, omagwira ntchito mu chimene ankachilingalira kukhala chikondwerero chaunyinji, apereka malamulo omwe amapanga polekezera pa malamulo a kuyenera kumeneko.

Monga mmene bwalo la milandu lalikulu lina mu United States linawonera kuti: “Kudidikiza kwa unyinji pa kuyenera kwa aliyense payekha kapena oŵerengeka opanda chithandizo kwakhala nthaŵi zonse kukulingaliridwa kukhala monga imodzi ya ngozi zazikulu za maboma otchuka.” Kunali kudidikiza kumeneku kumene kunayang’anizana ndi Mboni za Yehova mu United States mkati mwa ma-1930 ndi ma-1940.

Alaliki kapena Amalonda?

Pamene nkhondo ya dziko yachiŵiri inayandikira, ntchito ya kulalikira kwapoyera ya Mboni za Yehova inali chochititsa chizunzo chachikulu. Malamulo a m’Mizinda ofuna andawala ndi amalonda kukhala ndi chilolezo anagwiritsiridwa ntchito molakwika pa ntchito ya kulalikira ya Mboni. Akumazindikira kuti kugwiritsira ntchito kumeneku kwa malamulo oterowo kunaswa kuyenera kwa malamulo awo, Mboni zinatokosa malamulo amenewa mwa kumapitiriza ndi ntchito yawo ya kulalikira popanda choyamba kupeza chilolezo. (Marko 13:10; Machitidwe 4:19, 20) Monga chotulukapo, Mboni zambiri zinagwidwa.

Ngati mabwalo a milandu a ang’ono anapanga malamulo motsutsana ndi iwo, Mboni sizinalipire chirichonse koma m’malomwake zinangopita ku ndende. Izo zinapitirizabe kuchita apilu milandu imeneyo kwa okhala ndi malamulo okulira mu dongosolo la bwalo la milandu kumene kunali kothekera kotero kuti zimange magwero a zigamulo zowakomera omwe akachotsapo kusokoneza kopanda lamulo kumeneko ndi ntchito yawo. Pamene nthaŵi inapita, Bwalo la Milandu Lalikulu la U.S. linachotsapo mobwerezabwereza malamulo amenewa kukhala kaya opanda lamulo mwa iwo okha kapena kukhala akugwira ntchito, ndipo kuweruzidwa kwa Mboni za Yehova kunabwezedwa.

M’kuwonjezera ku lamulo la chilolezo, malamulo okhoma msonkho wa laisensi ankagwiritsiridwa ntchito kuletsa ntchito yolalikira ya Mboni za Yehova. Akumawona msonkhowo kukhala monga kuletsa kosakhalitsa pa ntchito yawo ya umulungu yolalikira, Mboni za Yehova zinakana kuulipira iwo. Kachiŵirinso, Mboni zambiri zinamangidwa, ndipo kachiŵirinso Bwalo la Milandu Lalikulu linalamulira mokomera ufulu wa kulankhula ndi kulambira.

Bwalo la Milandu linalongosola kuti mwaŵi wa kufalitsa mwaufulu ziphunzitso za chipembedzo ndi masamba osindikizidwa “umakhalapo popanda ulamuliro wa boma. Iwo uli wotsimikiziridwa kwa anthu ndi lamulo la bwalo la milandu lalikulu.” Mofupikitsidwa, boma silikanakhoza kuchotsapo chimene Lamulo linachiika kale.

Kuchita Sawatcha ku Mbendera

Mboni za Yehova zakhala nthaŵi zonse nzika zosunga lamulo zomwe sizimalingalira kusapereka ulemu mwa kukana kwawo kuchita sawatcha ku mbendera ya dziko lirilonse. Mboni zimakhulupirira kuti ntchito yawo yokulira ndi kulambira kuli kwa Mulungu wawo ndi Mpangi, Yehova. (Luka 4:8) Kupereka kulambira kotheratu ku ulamuliro uliwonse wa dziko lapansi kukakhala kuika zikondwerero za kudziko patsogolo pa zikondwerero zauzimu. (Machitidwe 5:29) Mosasamala kanthu ndi zolinga zowona zimenezi, kukana kwa Mboni kuchita sawatcha ku mbendera kwakhala kaŵirikaŵiri kosamvetsetsedwa ndi kugwiritsiridwa ntchito monga maziko a kuzunza.

Pamene nkhondo ya dziko yachiŵiri inkayandikira, mabungwe a masukulu a kumaloko ndi opanga lamulo a boma mu United States analengeza lamulo la kuchita sawatcha ku mbendera kuti achirikize umodzi wa dziko ndi chisungiko. Mosasamala kanthu za ukulu wa lingaliro lofala m’kuchirikiza zofunika zimenezi za kuchita sawatcha ku mbendera, Mboni za Yehova molimbika zinakana kutsutsa malamulo awo ozikidwa pa Baibulo.

M’kubwereramo mu mkhalidwewo, Bwalo la Milandu Lalikulu la U.S. linalongosola kuti pamene kuli kwakuti mabungwe a masukulu mosakaikira anali ndi malamulo ogwira ntchito ofunika ndi apamwamba, kugwira ntchito kumeneko kunafunikira kuchitidwa mkati mwa malire a Lamulo. Bungwe la sukulu silinali laufulu kusokoneza kuyenera kofunika kwa lamulo koperekedwa kwa munthu aliyense. Bwalo la Milandu Lalikulu chotero linasunga kuti lingaliro la bungwe la sukulu lonena za kachitidwe ka kuika chiyamikiro kaamba ka mbendera ndi ufuko wa utundu sikunapitirire chikumbumtima cha ufulu wa kuyenera kwa lamulo kwa wophunzirayo m’nkhani za chipembedzo.

Bwalo la Milandu Lalikulu silinali losadziwa za ukulu wa chigamulo chake kulinga ku kuyesayesa kwa nkhondo ya dziko komwe kunkachitidwa. Koma Bwalo la Milandu silinasinthe kugwira ntchito kwake ndipo linalongosola kuti pansi pa Lamulo la U.S., “ufulu wa kusiyana siuli wolekezera ku zinthu zomwe sizimagwira ntchito kwambiri. Kumeneko kukhala mthunzi wopanda pake waufulu. Mbali ya nsonga yake iri kuyenera kwa kusiyana ponena za zinthu zomwe zimagwira mtima wa lamulo lomwe liripo.”

Bwalo la Milandu Lalikulu linatsiriza lingaliro lake la kuchita sawatcha ku mbendera ndi ndemanga yotsatirayi: “Ngati pali mbali yokhazikitsidwa mu unyinji wa lamulo lathu, iri yakuti kulibe nduna, yaikulu kapena yaing’ono, yomwe ingakhoze kulongosola chomwe chidzakhala chosiyana m’ndale zadziko, utundu, chipembedzo, kapena nkhani zina za malingaliro kapena kukakamiza nzika kukana chikhulupiriro chawo ndi mawu kapena kachitidwe.”

Kuthandiza kwa Mboni

Mu zonsezo, Mboni za Yehova zakhala zachipambano m’kuchita apilu 23 ku Bwalo la Milandu Lalikulu la U.S. Izo zapanga kuthandizira kwakukulu ku kugwira ntchito kwa lamulo la United States, monga momwe kwawonedwera ndi ophunzira malamulo ambiri. Ndipo chikanakhala chosatheka ngati Mboni za Yehova sizinafune kuvutika ndi kusayenera, kumenyedwa, ndi kuikidwa m’ndende m’kuyesayesa kwawo kukhala omvera kwa Mulungu wawo.

Kunena kuti lamulo la kuyenera kwaufulu wa chipembedzo, ufulu wa kulankhula, ndi ufulu wa kudzilongosolera lapititsidwa patsogolo ndipo lalongosoledwa bwino kwambiri chifukwa cha chipiriro cha Mboni ndithudi chiri kokha chotulukapo chapambali cha cholinga chokulira cha Mboni cha kutumikira Yehova m’chigwirizano ndi Mawu ake Oyera.

Mboni za Yehova ziri za chisangalalo kaamba ka mwaŵi wa kutumikira Mfumu ya Chilengedwe, Yehova Mulungu, ndipo zagwiritsira ntchito zinthu zosiyanasiyana, kuphatikizapo zichinjirizo zopatsidwa ndi Lamulo lokhalapo kwa zaka 200 la U.S., kufikiritsa malekezero amenewo.

[Bokosi patsamba 28]

Lamulo Lichirikiza Mboni Kachiŵirinso

Pa June 10, 1987, mabwalo amilandu kachiŵirinso analamulira mokomera ufulu wa chipembedzo kaamba ka Mboni za Yehova pa maziko a lamulo. Monga momwe zinachitidwira ripoti mu “The New York Times,” Bwalo la Milandu la Apilu la U.S. kaamba ka gawo Lachisanu ndi Chinayi linapereka lamulo kuti ufulu wa kuchita m’chigwirizano ndi chikhulupiriro chawo cha chipembedzo “ufunikira kulekereredwa ndi chitaganya, pansi pa Lamulo, ‘monga mtengo woyenera kulipira kuti tichinjirize kuyenera kwa kusiyana kwa chipembedzo kumene nzika zonse zikusangalala nako.’” Mlanduwu unaphatikizapo kuyenera kwa Mboni kwa kulabadira lamulo la Baibulo lakuti ‘musamlandire iye kunyumba ndipo musamlankhule’ kwa awo omwe “sakhala m’chiphunzitso cha Kristu.”—2 Yohane 9-11.

[Chithunzi patsamba 26]

Independence Hall, Philadelphia, kumene Lamulo linapangidwa

[Mawu a Chithunzi]

Philadelphia Convention and Visitors Bureau

[Chithunzi patsamba 26]

Lamulo loyambirira likusungidwa Mosungira Zinthu Zakale za Dziko

[Mawu a Chithunzi]

U.S. National Archives

[Mawu a Chithunzi patsamba 24]

Architect of the Capitol, Washington, D.C.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena