Achichepere Akufunsa Kuti . . .
Kodi Kukhala Bwenzi la Mulungu Kuli Kanthu?
BWENZI ali munthu wapadera. Baibulo limalongosola bwenzi lowona kukhala amene amamamatira chifupi kuposa mbale, ali wokhazikika m’chimvero chake ndi mu ubwenzi, amabwera ku chithandizo cha mnzake pa nthaŵi ya mavuto, ndipo amapereka uphungu kwa iye mokhulupirika. (Miyambo 17:17; 18:24; 27:6, 9) Kodi kungakhale unansi uliwonse wabwino kuposa uwu?
Achichepere ambiri amakhulupirira mowona mtima kuti kukhala bwenzi la Mulungu kuli ndi zambiri zopereka. Komabe, nthaŵi zina inu mumavomerezana ndi ena omwe akudzimva kuti unansi wotere ndi Mulungu uli wosatheka kapena wosagwira ntchito. ‘Anthu ambiri akudzinenera kukhala ndi chikhulupiriro mwa Mulungu,’ iwo anganene kuti, ‘koma ngakhale okhulupirira amavutikabe ndipo amapita mu umoyo wofanana ndi uja wa osakhulupirira.’
Motero, kusiyana nkotani? Kodi kuyandikira chifupi ndi Mulungu kulidi kanthu? Kodi kukhala bwenzi la Mulungu kungakupindulitseni nkomwe? Zokumana nazo za achichepere ena lero zasonyeza kuti mapindu a unansi wathithithi ndi Mulungu ali apadera ndipo amapambana unansi uliwonse umene mungakulitse ndi bwenzi lirilonse. Tero motani?
Kuchita ndi Chididikizo
Anthu achichepere ena, omalondola unansi wakuya ndi Mulungu, anena kuti kukhala bwenzi la Mulungu kwawathandiza iwo kuletsa kudzimva koipa. Wa zaka zakubadwa khumi mphambu zisanu ndi zitatu Virginia, amene anakhudzidwa mwakuya ndi kupatukana kwa makolo ake, akuvomereza: “Ndinada atate anga. Ndinali wokwiya nthaŵi zonse. Monga chotulukapo, ndinayamba kuda anthu onse. Ndinkayesayesa kuvutitsa mabwenzi anga. Ndinali kufuna kupangitsa ena kumva chomwe ndinali kuvutika nacho!”
Tsopano, pambuyo pa kuphunzira Mawu a Mulungu, Virginia mwachimwemwe akuvomereza: “Ndikusintha kotani nanga komwe kwabwera kwa ine! Sindikusulizanso Atate. Ndabwera ku kuzindikira kuti ali kokha mkhole wa dongosolo lowola lochirikizidwa ndi Satana Mdyerekezi. Ndimawalemekeza iwo ndi kukhala bwinopo ndi wina aliyense tsopano.” Inde, chidziŵitso cha Baibulo chimathandiza achichepere monga Virginia kumvetsetsa chifukwa kaamba ka kudera nkhaŵa kwa lerolino ndi kuphunzira mmene angachitire nako.
Kukhala chifupi ndi Mulungu kungathandize inu kuchita ndi kudidikiza kumene mwachiwonekere kukukula. Juana ali mtsikana wa zaka zakubadwa 19 amene atate ake ndi achidakwa. “Nthaŵi zina Atate amabwera kunyumba oledzera ndi kuyamba kutimenya,” iye akutero. Kodi ndimotani mmene iye akupiririra ndi mkhalidwewo? “Pamene ndikudzimva wopsyinjika, ndikudziŵa kuti ndingapite kwa Yehova Mulungu m’pemphero ndi kudzimva wolimbikitsidwa.” Kumdziŵa Mulungu ndi kutsanzira mikhalidwe yake yokoma—yonga ngati chifatso ndi chipiriro—kwathandiza Juana kuphunzira mmene angachitire ndi atate ake.—Agalatiya 5:22, 23.
Sichingakhale chopepuka nthaŵi zonse kwa inu kusonyeza ulemu kwa makolo anu ndi kuwapatsa kulemekezedwa kwawo koyenerera. Koma chimene chimathandiza chiri kwa inu kukhutiritsidwa ndi mphamvu ya Mawu a Mulungu, Baibulo. Mtumwi Yohane akunena kuti “amuna achichepere” olimba ku uzimu a ku mpingo kumene iye analemberako kalata anakhala okhoza ngakhale “kugonjetsa woipayo” chifukwa ‘Mawu a Mulungu anakhalabe mwa iwo.’ (1 Yohane 2:14) Motero, uphungu wa Baibulo monga wotsatirawu umathandiza achichepere onga Juana ndi Virginia: “Polalatidwa tidalitsa; pozunzidwa, tipirira; ponamizidwa, tipempha.”—1 Akorinto 4:12, 13.
Ndiponso, mtumwi Petro akunena kuti chitsanzo chabwino—“mayendedwe anu oyera ndi kuwopa kwanu”—kungapambane pa mawu a ochititsa kudidikizidwa. (1 Petro 3:1, 2) Ngakhale kuti Petro analunjikitsa mawu awa kwa akazi Achikristu, mungapindule kuchokera ku uphungu uwu nanunso.
Ndithudi, sichiri chopepuka nthaŵi zonse kuchita ndi kudidikiza, koma kupereka moyo wanu kwa Yehova ndi pemphero loyenera lokhala ndi cholinga kungapeputse vutolo. Chiri chachisangalalo chotani nanga kudziŵa kuti Yehova amafuna kuthandiza ndipo ali nayo mphamvu ya “kuchita motero mochulukira kupambana ndi mmene nthaŵi zonse tingapemphere, kapena kuganizira”! (Aefeso 3:20, Today’s English Version; Yeremiya 9:24) Ndiponso, Baibulo limatitsimikizira kuti Mulungu “sakhala patali ndi yense wa ife.” (Machitidwe 17:27) Inde, mungakhale ndi bwenzi limene lingafikiridwe nthaŵi zonse.
Miyezo ya Makhalidwe Abwino Apamwamba
Kukhala bwenzi la Mulungu kwathandizanso achichepere kulimirira miyezo yawo yabwino yapamwamba imene imabweretsa chikhutiritso ndi mtendere wa maganizo. (Mateyu 6:13; Masalmo 141:3, 4) Wa zaka zakubadwa khumi mphambu zisanu ndi chimodzi Sofia akuvomereza kuti anakhala ndi kugonana ndi mnyamata pamene anali ndi kokha zaka 14 zakubadwa. Kuyang’ana kumbuyo, Sofia akunena kuti: “Sichinali kufikira pamene ndinayamba kuphunzira Baibulo kuti ndinaganizira kuleka kupita naye kokacheza.” Kuyambira nthaŵiyo, waletsa mayendedwe a makhalidwe oipa ndipo akunena kuti chidziŵitso cha Baibulo chalimbitsa unansi wake ndi Yehova.
Kugonana kwa kunja kwa ukwati kuli kofala m’mbali zambiri za dziko. Mu Mexico mokha, 90 peresenti ya achichepere anenedwa kuti anachita kugonana ukwati usanakhale! Monga chotulukapo, achichepere ambiri avutika ndi zotulukapo zake, zonga ngati ukwati wa ana kapena kubala mwana wa m’thengo. Mkati mwa chaka chimodzi chokha, ana oposa pa miliyoni imodzi anabadwa kwa atsikana a zaka za pakati pa 13 ndi 19 mu Mexico!
Lerolino, pali chitsenderezo chokulira cha kulowetsedwa m’kugonana pa msinkhu wa uchichepere. Koma m’malo mwa kungodziloŵetsa mu kugonana koipa, nchifukwa ninji choyamba osalingalira zotulukapo? Pambali pa zotulukapo mwamsanga mwakuthupi, talingalirani mmene Mulungu amakhudzidwira ngati tiswa lamulo lake. Satana wapereka chitokoso kwa Mulungu, akudzinenera kuti pansi pa chiyeso munthu sangakhoze kukhalabe wokhulupirika kwa Iye. Motero Yehova akulimbikitsa kuti: “Mwananga, khala wanzeru, nukondweretse mtima wanga; kuti ndimuyankhe yemwe anditonza.” (Miyambo 27:11) Talingalirani ponena za icho: Kodi mudzaswa lamulo la Mulungu mwa kupangitsa Satana kukhala wachimwemwe ndi Mulungu kukhala wachisoni?—Yerekezani ndi Masalmo 78:38-41.
Chitetezo chokulira kulinga ku mkhalidwe woipa chiri kwa inu kukulitsa unansi wanu waumwini, wathithithi ndi Yehova.
Palibe Kuyesedwa Kopambana kwa Umunthu
Kumbali ina, achichepere ena akuzengereza ponena za kukhala olowetsedwa ndi Mulungu. “Ndiri wa mantha kwakukulu,” akutero mtsikana wa zaka zakubadwa 14, “m’chakuti ngati ndilandira Mulungu, adzatenga malo kotheratu. Ndiri kwakukulukulu wa umunthu wandekha, koma ndimafuna kutsegula mtima wanga. Ndiridi wokhadzuka pakati ndi wosokonezeka. Ndimangofuna kuphunzira ndi kuyamba pang’onopang’ono. Ndidzimva kuti ngati ndifulumizidwa, ndidzakhala wamatha ndi kuleka.” Kodi mumadzimva m’njirayi?
Ngati ndi tero, mungakhale wotonthozedwa ndi chenicheni chakuti Mulungu adzakuthandizani kupyola vuto lirilonse m’moyo. “Sichiri chiyeso chopambana pa cha umunthu chimene mwakhala mutakhala nacho,” Baibulo likutero. “Koma Mulungu ali wokhulupirika amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.” (1 Akorinto 10:13) Kodi ndi zowonjezereka zotani zimene mungafunsire?
Koma simungapemphere kaamba ka thandizo ndi kuŵerenga mabukhu a mikhalidwe yoipa, kupita ku makanema oipa, kapena kumaseŵera limodzi ndi wa chiwalo chosiyana. Ngakhale kuti pemphero liri ndi kufunikira koyambirira—monga mmene kulankhulana kuliri kofunikira mu unansi waumwini uliwonse—muyenera kugwirira ntchito pa chimene mumapempha m’pemphero!—Luka 11:9, 13.
Mtsogolo Mowala!
Ngakhale kuli tero, mtengo umene muyenera kulipira—kuyesayesa kolowetsedwamo m’kusungilira ubwenzi wanu ndi Mulungu—uli waung’ono kwambiri kuyerekeza ndi madalitso a mtsogolo amene Mulungu walonjeza. Noe wa zaka zakubadwa 17 akunena kuti: “Yehova akupereka kwa ife mtsogolo mowala: Moyo ndi chimwemwe chosatha m’paradaiso wa pa dziko lapansi! Ichi ndi chinthu chimene palibe munthu aliyense angapereke!”
Mawu a Mulungu amalonjeza kuti “katsala kanthaŵi ndipo oipa adzatha psyiti . . . olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.” (Masalmo 37:10, 29) Monga wopatsa woolowa manja wa “mphatso iriyonse yabwino ndi chopereka chirichonse changwiro,” Yehova amasangalala m’kupereka mphoto kwa Mboni zachichepere zokhulupirika ndi madalitso.—Yakobo 1:5, 17; Masalmo 35:27; 84:11, 12; 149:4.
Motero kukhala bwenzi la Mulungu kulidi kanthu. Mulungu amakusamalirani. Pamene mukhala ndi vuto, amafuna kukuthandizani. Ali wopezeka nthaŵi yonse. Ali ndi mphamvu ya kukuthandizani ndi vuto lirilonse m’moyo. Ndipo ali Yehova yekha amene angakupatseni moyo wosatha—chinthu chapadera choposa cha mabwenzi a Mulungu.—Chivumbulutso 21:3, 4; Mateyu 25:46.
[Chithunzi patsamba 14]
“Abrahamu anatchedwa ‘bwenzi la Mulungu.’ Yesu anatcha ophunzira ake ‘abwenzi anga.’ . . . Motero nanenso ndingakhale bwezi lawo!”