Lingaliro Labaibulo
Kodi Muyenera Kumvera Malamulo Khumi?
MUNALI m’chaka cha 1513 B.C.E.a pamene chala cha Mulungu chinalemba pa mwala. Kuyambira pamenepo Malamulo Khumi akhala akulembedwanso ndi anthu ndi kufalitsidwa kuzungulira pa dziko lonse. Mazana a mamiliyoni a anthu aŵerenga iwo, ndipo ambiri adziŵa iwo pamtima. Mwinamwake palibe mpambo wina wa malamulo womwe walandira chisamaliro chofalikira choterocho. Funso liri, pa chikumbukiro chake cha 3,500 mu 1988: Kodi Malamulo Khumi adakali amphamvu kotero kuti muyenera kumvera iwo?—Eksodo 20:1-17; 31:18.
Ndi Kwa Ndani Kumene Iwo Anapangidwira?
Mulungu anapereka Malamulo Khumi kwa anthu omwe ankadziŵika monga Aisrayeli. M’mawu ake otsegulira, iye anachimveketsa kuti kunali kwa mtundu umodzi umenewu kumene iye analankhula kuti: “Ine ndine Yehova Mulungu wako, amene ndinatulutsa iwe ku dziko la Igupto, ku nyumba ya akapolo.” Ichi chikusonyeza kuti Malamulo Khumi anapangidwa kukhala mbali ya lamulo la mtundu.—Eksodo 20:2.
Anapatsiridwa kwa Akristu?
Ngakhale kuli tero, kodi Malamulo Khumi a mtundu wa chilengedwe chonse oterowo anayenera kukhala amphamvu ndi kugwira ntchito kwa omwe sanali Aisrayeli? Ayi. Zaka mazana pambuyo pake pamene mpingo Wachikristu unapangidwa, lamulo limeneli silinapatsiridwe kwa iwo. Nchifukwa ninji? Chifukwa Baibulo limanena kuti “Kristu ali chimaliziro cha Lamulo.” (Aroma 10:4) Kodi chimenecho chimatanthauzanji?
Kuti tichitire chitsanzo, kubwerera mu 1912 kudumpha m’mwamba kopambana kwa dziko lonse kolembedwa kunali mamita 2.01. Zaka makumi asanu ndi aŵiri mphambu zisanu pambuyo pake, mu 1987, cholemberacho chinali mamita 2.43. Payenera, ngakhale kuli tero, kukhala malire omalizira ku utali umene munthu angadumphe mtengo wopingasa wochirikizidwa ndi mizati iŵiri. Ngwazi yomwe idzafikira malire amenewa idzamaliza zolembedwa za kudumpha kwa dziko lonse. Iye anganenedwenso kukhala “chimaliziro” cha izo. Tsopano, ndimotani mmene tingagwiritsire ntchito ichi ku Malamulo Khumi?
Pamene Mulungu anapanga “Lamulo,” limene linakupatira Malamulo Khumi limodzi ndi malamulo ena 600 ndi zitsogozo, ndi kupereka iwo kwa Aisrayeli, iye anakhazikitsa chonulirapo kapena muyezo wa ungwiro. Iye anaika mtengo wopingasa pa malo apamwamba koposa, kunena kwake titero. Lamulo la umulungu limeneli linali la muyezo wapamwamba wotero wa makhalidwe abwino womwe kokha munthu wangwiro akanaufikira. Mlaliki 7:20 amanena kuti: “Kulibe wolungama pansi pano amene achita zabwino osachimwa.”
Chotero mtengo wopingasawo—muyezo wolungama wa Mulungu—unaikidwa pamwamba kwambiri kaamba ka Aisrayeli opanda ungwiro, kapena Ayuda. Nchifukwa ninji? Mtumwi Wachikristu Paulo akulongosola: “Chinawonjezedwa [Lamulo] chifukwa cha zolakwa, kufikira ikadza mbewu [Mesiya, kapena Kristu] imene adailonjezera.” (Agalatiya 3:19) Ndi Lamulolo, Mulungu anasonyeza Ayuda kuti iwo anali olakwira lamulo opanda ungwiro, osakhoza kufikira chonulirapo cha kukhala olengezedwa kukhala olungama chifukwa cha ntchito za iwo eni.
Panali kokha mmodzi yemwe akakhoza kudumpha mtengo wopingasa umenewo: Mesiya wobwera wolonjezedwayo, kapena Kristu. Chotero, muyezo wapamwamba umenewo unaikidwa pamaso pa Ayuda monga chinachake choyenera kunulirapo pamene anali kuyang’ana kutsogolo kaamba ka Ngwazi yomalizira, Mesiya, kudumpha uwo kamodzi ndi kwa nthaŵi zonse.
“Kutsogolera kwa Kristu”
M’chigwirizano ndi ichi, Paulo akupitiriza m’mutu wachitatu wa Agalatiya, versi 24: “Momwemo Chilamulo chidakhala namkungwi wathu wakutifikitsa kwa Kristu, kuti tikayesedwe olungama ndi chikhulupiriro [mwa iye].” Namkungwi m’nthaŵi za Baibulo anatsogoza mwana kwa mphunzitsi wake ndipo analinso kulangiza ndi kulanga mwanayo.
Malamulo Khumiwo, limodzinso ndi Lamulo lonse, mwakutero akakonzekeretsa Ayuda kaamba ka Mesiya ndi kuwatsogoza iwo kwa iye. Pamene Yesu anabwera, kukhala pakati pawo, ndi kufa womvera mwangwiro ku Lamulo, iye anakhala “chimaliziro cha Lamulo.” Kenaka Mulungu anachotsa mtengo wopingasa umenewo, monga mmene kunaliri, ndi kupereka kwa Ayuda chinachake chabwinopo. Tsopano iwo “monga mphatso ya ulere” pomalizira anakhala “olengezedwa olungama ndi chisomo chake mwa chiwombolo cha Kristu Yesu.”—Aroma 3:24.
Paulo akunenanso kuti, “Simuli a Lamulo koma achisomo” ndipo, “Ngati mzimu ukutsogolerani, simuli omvera lamulo.”—Aroma 6:14; Agalatiya 5:18.
Chimene Muyenera Kumvera
Tsopano, popeza Akristu sali “pansi pa lamulo,” kodi iwo chotero ali omasuka ku zoletsa za makhalidwe abwino? Kutalitali. Monga mmene Paulo anasonyezera, Akristu akutsogozedwa ndi mzimu woyera wa Mulungu, ndipo sutsogoza aliyense mu chimo. Umawafulumiza iwo kusachita machimo olongosoledwa mu Malamulo Khumi. Mwachitsanzo, ngati muŵerenga 1 Akorinto 6:9, 10, mudzapeza malamulo angapo Achikristu omwe ali ofanana ndi ena a Malamulo Khumi. Iwo ali zoletsa zotsutsa kulambira mafano, chigololo, kuba, ndi kusirira.
Kristu nayenso anafupikitsa Lamulo lakale, lomwe linaphatikizapo Malamulo Khumi, ndi malamulo a akulu aŵiri awa: “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse ndi moyo wako wonse ndi nzeru zako zonse” ndi, “Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini.” (Mateyu 22:37-39) Mwa kukalamira kumvera iwo, kufunsira kaamba ka chikhululukiro pamene tilakwa, ndi kusonyeza chikhulupiriro mu dipo la Kristu, mudzapeza chisomo chochokera kwa Mulungu ndi chivomerezo Chake kaamba ka moyo wosatha.—2 Atesalonika 2:16.
[Mawu a M’munsi]
a Onani tsatanetsatane mu chofalitsidwa cha Watch Tower Society Aid to Bible Understanding, tsamba 333.