Kodi Malamulo Khumi Amatanthauzanji kwa Inu?
MKATI mwa miyezi itatu ya kuwomboledwa kwawo kuchoka mu Igupto mu 1513 B.C.E., Aisrayeli anamanga msasa kutsogolo kwa Phiri la Sinai m’chipululu. Pamene Yehova anaitana, mneneri Mose anakwera phirilo ndipo anamva Mulungu akulonjeza kuti Iye akapanga mtundu wa Israyeli kukhala “chuma [Chake] chapadera kuposa mitundu yonse ya anthu.” Kenaka Mose anauza anthuwo kudzera mwa akulu a mtunduwo. “Ndipo anthu onse anavomera pamodzi nati, Zonse adazilankhula Yehova tidzazichita.”—Eksodo 19:1-8.
Pambuyo pake, Mulungu analongosola momvekera Malamulo Khumi kwa Mose, akumayamba malamuloŵa ndi ndemanga yakuti: “Ine ndine Yehova Mulungu wako, amene ndinatulutsa iwe ku dziko la Aigupto, ku nyumba ya akapolo.” (Eksodo 20:2) Decalogue imeneyi inali ya Aisrayeli, amene adauzidwa mu Lamulo Loyamba kuti: “Usakhale nayo milungu ina koma ine ndekha.”—Eksodo 20:3.
Potsatira izo, Yehova anampatsa Mose malangizo m’malamulo ena aumulungu kwa Israyeli. (Eksodo 20:4–23:19) Onse pamodzi, anakhala malamulo 600. Ndipo chinali chosangalatsa chotani nanga kudziŵa kuti mngelo wa Mulungu anali kuyenda patsogolo pa mtunduwo kukonzekera njira yopita ku Dziko Lolonjezedwa! (Eksodo 23:20-22) Yehova analengeza kuti: “Ndidzachita zozizwa pamaso pa anthu ako onse, sizinachitika zotere ku dziko lonse lapansi, kapena ku mtundu uliwonse wa anthu; ndipo anthu onse amene uli pakati pawo adzawona ntchito ya Yehova, pakuti chinthu ndikuchitirachi nchowopsya.” M’malo mwake, kodi Mulungu anafunanji kwa anthuŵo? “Dzisungire chinthu ndikuuza lerolino.” Inde, chimvero ku malamulo ndi zitsogozo zonse za Yehova chinali chofunika.—Eksodo 34:10, 11.
Zimene Mawu Khumiwo Anatanthauza kwa Israyeli
Monga chotulukapo cha kuthaŵa kwawo kotetezeredwa mwaumulungu kuchoka ku ukapolo Wachiigupto, Aisrayeli anadziŵa dzina la Mulungu m’lingaliro latsopano. Yehova anakhala Moombolo wawo. (Eksodo 6:2, 3) Chotero, lamulo lachitatu linakhala ndi tanthauzo lapadera kwa iwo, popeza iwo analetsedwa kutchula dzina laumulungulo mwachabe.—Eksodo 20:7.
Koma bwanji ponena za lamulo lachinayi, lomwe limakhudza tsiku la Sabata? Lamulo limeneli linasonyeza ulemu kaamba ka zinthu zopatulika, monga momwe Yehova poyambapo anali ataneneratu pokhazikitsa ‘kusunga sabata’ m’chigwirizano ndi kutola mana. (Eksodo 16:22-26) Chifukwa chakuti Aisrayeli ena sanamvere pa nthaŵi yomweyo, Yehova anawakumbutsa momvekera kuti iye anaŵapatsa lamulo limenelo. “Taonani, popeza Yehova anakupatsani Sabata, . . . Ndipo anthu anapumula pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri.” (Eksodo 16:29, 30) Pambuyo pake, Yehova anasonyeza mmene kakonzedwe kameneka kanaliri kapadera, akumalongosola kuti: “Ndicho chizindikiro chosatha pakati pa ine ndi ana a Israyeli.”—Eksodo 31:17.
Kenaka, lingalirani lamulo lapadera lakhumi, loletsa kusirira. Pano pali lamulo lomwe palibe munthu yemwe akanalilimbitsa. Munthu Wachisrayeli aliyense anali woŵerengera kwa Mulungu wake, Yehova, yemwe anafufuza mtima wa munthu aliyense payekha kuti apeze zolinga zake.—Eksodo 20:17; 1 Samueli 16:7; Yeremiya 17:10.
Lingaliro Losinthidwa
Yesu Kristu, yemwe anabadwira mu mtundu wa Israyeli, anauza ophunzira ake kuti: “Musaganize kuti ndinadza ine kudzapasula chilamulo kapena aneneri: sindinadza kupasula, koma kukwaniritsa.” (Mateyu 5:17) Kwa Akristu Achihebri mtumwi Paulo adalemba kuti: ‘Chilamulo chiri nawo mthunzi wa zokoma zirinkudza, osati chifaniziro chenicheni cha zinthuzo.’ (Ahebri 10:1) Ngati inu munali Mhebri wotembenuzidwira ku Chikristu, kodi mukanamvetsetsa motani ndemanga zimenezi? Ziŵalo zina za mpingo woyambirira Wachikristu zinakhulupirira kuti mazana onse a malamulo amene Mulungu anapereka kupyolera mwa Mose, kuphatikizapo Malamulo Khumi, ankagwirabe ntchito. Koma kodi limenelo linali lingaliro lolondola?
Lingalirani mawu aŵa a Paulo kwa Ayuda omwe anakhala Akristu m’chigawo cha Galatiya: “Ife ndife Ayuda pachibadwidwe, ndipo sitiri ochimwa a kwa amitundu; koma podziŵa kuti munthu sayesedwa wolungama pa ntchito ya lamulo, koma mwa chikhulupiriro cha Yesu Kristu, ifedi tinakhulupirira kwa Yesu Kristu, kuti tiyesedwe olungama ndi chikhulupiriro cha Kristu, ndipo si ndi ntchito za lamulo.” (Agalatiya 2:15, 16) Ndithudi, kaimidwe kolungama ndi Mulungu sikanadalire pa chimvero changwiro ku Chilamulo cha Mose, popeza kuti mu mkhalidwe waumunthu wopanda ungwiro, chimenecho chinali chosatheka. Paulo anawonjezera kuti: “Onse amene atama ntchito za lamulo liwakhalira temberero; pakuti kwalembedwa, Wotembereredwa aliyense wosakhala m’zonse zolembedwa m’bukhu la chilamulo, kuzichita izi. . . . Kristu anatiombola ku temberero la chilamulo, atakhala temberero m’malo mwathu.”—Agalatiya 3:10-13.
Ngati atsatiri a Yesu Achiyuda sanalinso pansi pa temberero la Chilamulo, kodi Akristu alionse anali ndi thayo la kusunga malamulo onse operekedwa kwa Israyeli? Kwa Akolose, Paulo adalemba kuti: ‘[Mulungu] mwachifundo anatikhululukira ife zolakwa zathu ndipo adatifafanizira cha pa ifecho cholembedwa m’zoikikazo, chimene chinali chotsutsana nafe: ndipo anatichotsera pakatipo, ndi kuchikhomera ichi pa mtengo wozunzirapo, [wa Kristu].’ (Akolose 2:13, 14) Mosakaikira, Akristu ambiri oyambirira anafunikira kuwongolera kulingalira kwawo ndi kuzindikira kuti ‘anamasulidwa kuchilamulo.’ (Aroma 7:6) Mwa kusonyeza chikhulupiriro mu imfa ya dipo ya Yesu, yomwe inathetsa Chilamulo ndi kutsegula njira kaamba ka kukhazikitsidwa kwa “pangano latsopano” lonenedweratulo, iwo anali ndi chiyembekezo cha kupeza kaimidwe kolungama ndi Yehova.—Yeremiya 31:31-34; Aroma 10:4.
Zimene Amatanthauza kwa Ife
Kodi izi zimatanthauza kuti Malamulo Khumi, mbali yaikulu ya Chilamulo, alibe tanthauzo lirilonse kwa Akristu? Ndithudi ayi! Ngakhale kuti Mawu Khumiwo sali omangirira mwalamulo pa Akristu, malamulo ameneŵa akupitirizabe kupereka chitsogozo chabwino, monga mmene amachitira malamulo ena a Chilamulo cha Mose. Mwachitsanzo, Yesu adati malamulo aŵiri aakulu koposa ndi aja a chikondi kwa Mulungu ndi mnansi. (Levitiko 19:18; Deuteronomo 6:5; Mateyu 22:37-40) Popereka uphungu kwa Akristu Achiroma, Paulo anagwira mawu lamulo lachisanu ndi chimodzi, lachisanu ndi chiŵiri, lachisanu ndi chitatu, ndi lakhumi, akumawonjezera kuti: “Lamulo lina lirilonse limangika pamodzi m’mawu ameneŵa, kuti, Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe wekha.”—Aroma 13:8, 9.
Chotero, monga mbali ya Mawu ouziridwa a Mulungu, kodi Malamulo Khumi ali ndi chifuno chotani lerolino? Iwo amavumbula lingaliro la Yehova pa nkhani. (2 Timoteo 3:16, 17) Lingalirani mmene amachitira choncho.
Malamulo anayi oyambirira amagogomezera mathayo athu kwa Yehova. (Loyamba) Ali Mulungu amene akufunabe kudzipereka kotheratu. (Mateyu 4:10) (Lachiŵiri) Palibe mlambiri wake ndi mmodzi yense amene ayenera kugwiritsira ntchito mafano. (1 Yohane 5:21) (Lachitatu) Kugwiritsira kwathu dzina la Mulungu kuyenera kukhala koyenera ndipo kolemekezeka, osati konyoza konse. (Yohane 17:26; Aroma 10:13) (Lachinayi) Moyo wathu wonse uyenera kuzikidwa pa zinthu zopatulika. Ichi chimatitheketsa kupumula, kapena ‘kusunga sabata,’ ku njira yachilungamo chaumwini.—Ahebri 4:9, 10.
(Lachisanu) Chimvero cha ana kwa makolo awo chikutumikirabe monga maziko a umodzi wa banja, chikumabweretsa madalitso a Yehova. Ndipo ndi chiyembekezo chabwino koposa chotani nanga chimene “lamulo loyamba lokhala nalo lonjezano” limeneli limapereka! Sikokha “kuti kukhale bwino ndi iwe” komanso “kuti ukhale wa nthaŵi yaikulu padziko.” (Aefeso 6:1-3) Popeza tsono tikukhala “m’masiku otsiriza” a dongosolo iri loipa, chimvero chaumulungu chimenecho chimapereka kwa achichepere chiyembekezo cha kusafa konse.—2 Timoteo 3:1; Yohane 11:26.
Chikondi cha mnansi chidzatiletsa kusamuvulaza kupyolera m’zochita zoipa zoterozo zonga ngati (Lachisanu ndi chimodzi) kupha, (Lachisanu ndi chiŵiri) chigololo, (Lachisanu ndi chitatu) kuba, ndipo (Lachisanu ndi chinayi) kupanga ndemanga zabodza. (1 Yohane 3:10-12; Ahebri 13:4; Aefeso 4:28; Mateyu 5:37; Miyambo 6:16-19) Koma bwanji ponena za zolinga zathu? Lamulo (Lakhumi), loletsa kusirira, limatikumbutsa kuti Yehova amafuna kuti zolinga zathu zidzikhala zoongoka nthaŵi zonse m’maso mwake.—Miyambo 21:2.
Ndi matanthauzo othandiza otani nanga amene timapeza m’Malamulo Khumi! Popeza ali ozikidwa pa malamulo a makhalidwe abwino aumulungu amene sadzakhala konse achikale, tiyenera kuŵawona iwo monga zokumbutsa zamtengo wake za mathayo athu a kukonda Mulungu ndi mnansi.—Mateyu 22:37-39.
[Chithunzi patsamba 6]
Imfa ya Yesu inathetsa Chilamulo, kuphatikizapo Malamulo Khumi operekedwa kwa Aisrayeli pa Phiri la Sinai