Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g88 9/8 tsamba 24-26
  • Kulekeka kwa Zida za Nyukliya—Motani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kulekeka kwa Zida za Nyukliya—Motani?
  • Galamukani!—1988
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zochititsa ndi Zothetsera
  • Boma la Dziko—Lenileni!
  • Potsiriza Pake Tsogolo Lopanda Choopsa!
    Galamukani!—1999
  • Kodi Ndani Amene Angabweretse Mtendere Wokhalitsa?
    Galamukani!—1996
  • Kupanikiza kwa Nyukliya
    Galamukani!—1988
  • Kuopa Nyukiliya—Sikunathe Ngakhale Pang’ono
    Galamukani!—1999
Onani Zambiri
Galamukani!—1988
g88 9/8 tsamba 24-26

Kulekeka kwa Zida za Nyukliya—Motani?

WATHU uli m’mbadwo wa kudera nkhaŵa. Ukwati wa sayansi ku mkhalidwe wa nkhondo watulutsa zida zikwi zingapo za mphamvu ya kupha yosayerekezedwa, akupha osasankha omwe ali ndi mphamvu ya kupha anthu.

Kunena kuti munthu ali wofunitsitsa kupha munthu mnzake kukupangitsa kusakhazikika. Komabe, zikhoterero zakupha za munthu zinasonyezedwa chifupifupi kuchokera ku chiyambi. Limasimba tero Baibulo kuti: “Ndipo panali pamene anali kumunda Kaini anamuwukira Abele mphwake namupha.” (Genesis 4:8) Munthu wakhala akupha munthu mnzake chiyambire pamenepo. Ndipo pamene kuli kowona kuti chiyambire 1945 munthu wabweza dzanja lake ku kugwiritsira ntchito zida za nyukliya mu nkhondo, lathu lakhalabe zana la kupha anthu m’mbiri. Mowonekera, vuto siliri zida zenizenizo.

Zochititsa ndi Zothetsera

Ophunzira ena amadzimva kuti popeza kuti ali anthu omwe amamenya nkhondo, zochititsa zifunikira kupezedwa m’chibadwa cha munthu iyemwini. Mogwirizana ndi kawonedweka, anthu amamenya nkhondo chifukwa cha dyera, kupusa, ndi zochititsa zankhalwe zosatsogozedwa bwino. Kulongosola kumasiyanasiyana, koma ambiri amadzimva kuti mtendere ungabwere kokha kupyolera mwa kusintha kawonekedwe ndi mkha-lidwe wa munthu iyemwini.

Ena amanena kuti popeza kuti nkhondo zimamenyedwa pakati pa mitundu, zochititsa za nkhondo zimakhala m’kapangidwe ka dongosolo la ndale zadziko la mitundu yonse. Chifukwa chakuti dziko lirilonse lolamulira limachita molingana ndi zofuna zake ndi zikhumbo, kukanthana mwachiwonekere kumachitika. Popeza kuti palibe kugwirizana, njira zodalirika za kugwirizanitsa kusiyanako, nkhondo zimawulika.

M’kufufuza kwake kwa zochititsa nkhondo, wophunzira Kenneth Waltz wawona kuti “boma la dziko liri chothetsera kaamba ka nkhondo ya dziko.” Koma iye wawonjezera kuti: “Chothetsera, ngakhale kuti chingakhale chosafikirika m’chenicheni, chiri chosakhoza kufikirika mogwira ntchito.” Ena amavomereza. Mkonzi Ben Bova walongosola m’magazini ya Omni kuti: “Mitundu ifunikira kugwirizana kupanga boma limodzi lomwe lingalamulire zida ndi kuchinjiriza nkhondo.” Komabe, iye akunenanso kuti: “Anthu ambiri amawona boma la dziko loterolo monga kachidutswa m’mlengalenga, loto la chinyengo la sayansi lomwe silingakhale lowona.” Kulephera kwa Mitundu Yogwirizana kumabweretsa mathedwe osakhutiritsa amenewa. Mitundu yakhala yosafunitsitsa kupereka ulamuliro wawo ku gulu limenelo kapena lina lirilonse!

Boma la Dziko—Lenileni!

Baibulo, ngakhale kuli tero, limatitsimikizira ife kuti Mulungu iyemwini walinganiza boma la dziko lenileni. Mamiliyoni mosadziŵa apemphera kaamba ka boma limeneli pamene amapereka Pemphero la Ambuye kuti: “Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga kumwamba, chomwecho pansi pano.” (Mateyu 6:10) Mutu wa boma la Ufumu limenelo ali Kalonga wa Mtendere, Yesu Kristu. Baibulo limalonjeza ponena za boma limeneli kuti: “Lidzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse,” kapena maboma aumunthu.—Danieli 2:44.

Boma la dziko limeneli lidzabweretsa mtendere wowona ndi chisungiko, osati mwa kuchinjiriza kwa nyukliya kapena kupyolera m’dongosolo lakuya la zida zochinjirizira zapamwamba kapena misonkhano yosakhazikika ya ndale zadziko. Salimo 46:9 imalosera kuti Yehova Mulungu “aletsa nkhondo kumalekezero a dziko lapansi. Athyola uta nadula nthungo; atentha magareta ndi moto.” Ichi chimatanthauza kuwononga kwa zida zonse, kuphatikizapo ziŵiya za nyukliya.

Koma bwanji ponena za mkhalidwe wonga wa nkhondo wa munthu iyemwini? Pansi pa boma la kumwamba la Mulungu, okhala padziko lapansi “adzasula malupanga awo akhale zolimira ndi nthungo zawo zikhale anangwape. Mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sudzaphunziranso nkhondo.” (Yesaya 2:4) Anthu mamiliyoni atatu lerolino ayamba kale kukhala molingana ndi lemba la Baibulo limeneli. Iwo ali Mboni za Yehova.

Mboni zimenezi zimakhala m’maiko oposa 200 ndipo zimadza kuchokera ku chiyambi cha magulu osiyanasiyana. Asanakhale Akristu owona, ena a iwo anali onga ankhondo, mwinamwake ngakhale achiwawa. Koma monga chotulukapo cha kutenga chidziŵitso cha Mulungu, iwo tsopano amakana kutenga zida molimbana ndi anzawo kapena wina aliyense. Kaimidwe kawo ka uchete pamaso pa kukanthana kwa ndale zadziko kali nkhani ya zolembedwa za mu mbiri. Kaimidwe ka mtendere kamene Mboni za Yehova zatenga m’mitundu yonse kamachitira umboni ku chenicheni chakuti dziko lopanda nkhondo ndi zida za nyukliya liri lothekera.

Anthu mamiliyoni angapo omwe ali ndi moyo lerolino anabadwira mumbadwo wa nyukliya ndipo akuyembekezera kufera mmenemo—ngati iwo sadzafa chifukwa cha iyo. Mboni za Yehova sizimagawana kawonedwe ka chizimezime koteroko. Chikhulupiriro chawo chimaikidwa mokwanira mu Ufumu ndi mwa Mulungu wawo, Yehova, kwa amene “palibe mawu adzakhala opanda mphamvu.”—Luka 1:37.

[Chithunzi patsamba 25]

Baibulo limalosera kuti ali Mulungu yemwe adzathetsa zida za nkhondo

[Chithunzi patsamba 26]

Pansi pa boma la kumwamba la Mulungu, dziko lapansi lidzakhala lopanda nkhondo ndi zida zosakaza

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena