Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g88 9/8 tsamba 28-29
  • Chifukwa Chimene Nthanthi Ya Zaumulungu Yonena za Ufulu Siiri Yankho

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chifukwa Chimene Nthanthi Ya Zaumulungu Yonena za Ufulu Siiri Yankho
  • Galamukani!—1988
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Nthanthi ya Zaumulungu Yolakwika
  • Nchiyani Kwenikweni Chimene Chimathandiza Osauka?
  • Posachedwapa, Sikudzakhalanso Mmphaŵi!
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Tsanzirani Yesu Poganizira Osauka
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Mapeto a Umphaŵi Ayandikira
    Galamukani!—1998
  • Dziko Lopanda Umphawi Layandikira
    Nsanja ya Olonda—2005
Onani Zambiri
Galamukani!—1988
g88 9/8 tsamba 28-29

Lingaliro Labaibulo

Chifukwa Chimene Nthanthi Ya Zaumulungu Yonena za Ufulu Siiri Yankho

NTHANTHI ya zaumulungu yonena za ufulu iri mwapang’ono lingaliro latsopano. Iyo inakulitsidwa zaka makumi aŵiri zapitazo ndi ansembe a Roma Katolika mu South America omwe anaipidwa ndi kusauka koipa kwa ambiri mu nkhosa zawo. Iwo anadzimva kuti kokha mwa kulankhula kwa osauka koposa ponena za zinthu zauzimu sikunali kwenikweni kuwathandizo iwo. M’malomwake, iwo, atsogoleri a chipembedzo, anadzimva kuti anafunikira kuchirikiza masinthidwe a mayanjano abwino ngati anthu anafunikira kuwongokera mwauzimu. Ena anakhoza ngakhale kulengeza masinthidwe.

Ndithudi, sichiri cholakwika kufuna kuwongolera osauka ochulukira. Yesu iyemwini anamva chifundo chokulira kaamba ka anthu a m’tsiku lake. Timaŵerenga kuti: “Koma iye powona makamuwo anagwidwa m’mtima ndi chisoni chifukwa cha iwo, popeza anali okambululudwa ndi omwazikana akunga nkhosa zopanda mbusa.” (Mateyu 9:36) Ndithudi, Yesu analonjeza ufulu kwa awo omwe anamvera ku mawu ake, akumanena kuti: “Mudzazindikira chowonadi, ndipo chowonadi chidzakumasulani.” (Yohane 8:32) Chotero kodi nthanthi ya zaumulungu yonena za ufulu iri njira ya Baibulo kaamba ka mtumiki Wachikristu kuthandizira osauka?

Nthanthi ya Zaumulungu Yolakwika

Ayi, kaamba ka zifukwa zambiri. Kaamba ka chinthu chimodzi, thayo loyambirira la mtumiki Wachikristu liri khalidwe lauzimu la nkhosa zake, ndipo palibe umboni wakuti ngati khalidwe la munthu wosauka lawongokera, iye adzakhala wokhoterera kwambiri ku kuwongokera kwauzimu. Ndithudi, maiko olemera kwambiri a North America ndi Europe, mosasamala kanthu za kukhala kwawo bwino kwambiri, amasauka ku mavuto okulira auzimu. Kusawona mtima, chisembwere, kuipsya ana ndi nkhalamba, ndi umbombo—kungotchula zochepa zokha—ziri zochulukira. Ndipo m’malo ena chikondwerero mwa Mulungu chaferatu.—2 Timoteo 3:1-5.

Mowonjezereka, nthanthi ya zaumulungu yonena za ufulu sinali njira imene Yesu anachitira kuthandiza osauka, ndipo Yesu ali Chitsanso Chachikulu kwa Akristu enieni. (1 Petro 2:21) Pamene Yesu anali padziko lapansi, anakhala pakati pa anthu omwe anali olamulidwa ndi mphamvu za ulamuliro wolowelera ndipo anasauka pa manja a osonkhetsa misonkho abodza. Opanda chithandizo chochulukira pakati pa iwo kaŵirikaŵiri anali minkhole ya ziwalo za olanda za gawo lolamulira. (Mateyu 22:21; Luka 3:12, 13; 20:46, 47) Komabe, Yesu sanadzilowetse mu nthanthi ya ndale zadziko kapena kuchirikiza kwa mayanjano kuyesera kuwongolera unyinji wawo. M’malomwake, iye analalikira “mbiri yabwino ya ufumu.”—Mateyu 4:23.

Potsirizira pake, atumiki a chipembedzo omwe amachirikiza nthanthi yonena za ufulu akufunafuna zothetsera za ndale zadziko ku mavuto omwe angathetsedwe kokha m’njira ya Mulungu. Ngakhale kuti nthanthi yawo ikutchedwa nthanthi ya zaumulungu, siiri yozikidwa pa Baibulo. Yesu ananena za ophunzira ake kuti: “Sali a dziko lapansi, monga ine sindiri wa dziko lapansi.” (Yohane 17:16) Chiri chosatheka kulimbikitsa changu cha ndale zadziko ndipo kusakhala “mbali ya dziko.”—Yakobo 4:4.

Nchiyani Kwenikweni Chimene Chimathandiza Osauka?

Motsimikizirika, ngati anthanthi ya zaumulungu yonena za ufulu alibe uthenga wauzimu womwe uli woyenerera kwa osauka kwambiri, tiyenera kunena kuti iwo akulalikira uthenga wolakwika. Yesu anathandiza kwakukulukulu osauka omwe ankachitapo kanthu a m’tsiku lake, ndipo Mboni za Yehova zikuchita chinthu chofananacho lerolino pamene zigawana kulalikira kwa “mbiri yabwino ya ufumu.”—Mateyu 24:14.

Kodi nchiyani chimene chiri mbiri yabwino imeneyi? Kaamba ka nthaŵi yathu, chiri chowonadi chakuti Ufumu wa Mulungu wakhazikitsidwa m’mwamba ndipo posachedwapa udzachotsa kuipa kulikonse ndi kudidikiza kuchoka pa dziko iri lapansi. (Chivumbulutso 11:15, 18) Mwa njirayi, Ufumu wa Mulungu udzathetsa kosatha mavuto a kusauka ndi kudidikiza. Kulankhula za chiyambukiro cha kulamulira kwa Ufumu wa Mulungu, Baibulo limanena kuti: “Ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo, ndipo sipadzakhalanso imfa, ndipo sipadzakhalanso maliro kapena kulira kapena chowawitsa. Zoyambazo zapita.” (Chivumbulutso 21:4) Ndi chiyembekezo chokulira chotani nanga kaamba ka anthu owona mtima!

Koma ndimotani mmene chowonadi chimenechi chonena za Ufumu wa Mulungu chimathandizira anthu osauka? Chabwino, kumbukirani kuti Yesu ananena kuti: “Mudzazindikira chowonadi, ndipo chowonadi chidzakumasulani.” (Yohane 8:32) Chowonadi chimathandiza wina kusangalala ndi ufulu kuchokera ku chikumbutima chodzipatsa mlandu, ufulu wochokera ku mantha a mtsogolo, ndi ufulu kuchokera ku kukhulupirira malaulo kwa chipembedzo.

Ndiponso, munthu amene amaphunzira chowonadi chimenechi amapeza Mabwenzi aŵiri amphamvu kwambiri. Mmodzi ndi Kristu Yesu, yemwe tsopano akulamulira monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Winayo ndi Yehova Mulungu iyemwini, za amene Baibulo limanena kuti: “Umsenze Yehova nkhaŵa zako, ndipo iye adzakugwiriziza. Nthaŵi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.” (Salmo 55:22) Ngakhale ngati munthu wosauka akhala ndi moyo pansi pa dongosolo la ndale zadziko lodidikiza kapena la chuma, Mabwenzi aŵiri omvera chifundowa angamuthandize iye kuchita nazo kupyolera mu mpingo Wachikristu.

Mowonjezereka, kuvomereza ku chowonadi chonena za Ufumu wa Mulungu kumatsogolera munthu kuchotsa zizoloŵezi zoipa ndi kupanga kugwiritsira ntchito kwa chuma chirichonse chimene iye ali nacho. Ayi, munthu wosauka samakhala wolemera moyenerera chifukwa cha kukhala ndi moyo Wachikristu. Koma ngati aika Ufumu wa Mulungu choyamba ndi kukhala ndi moyo mogwirizana ndi miyezo Yake yolungama, m’njira ina kapena inzake zofunika zakuthupi za moyo zimaperekedwa. Chiri monga mmene Yesu analonjezera kuti: “Koma muthange mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake ndipo zonse zimenezo zidzawonjezeredwa kwa inu.”—Mateyu 6:33.

Mfumu Davide wakale anapereka umboni wothuzitsa mtima ku njira imene Mulungu amasamalira kaamba ka Ake. Iye ananena kuti: “Ndinali mwana ndipo ndakalamba, ndipo sindinapenya wolungama wasiyidwa, kapena mbumba zake zirinkupempha chakudya.” (Salmo 37:25) Pali zitsanzo zosaŵerengeka pakati pa Mboni za Yehova lerolino zomwe zimatsimikizira ichi kukhala tero.

Chotero, m’malo mofunafuna zofunkha zosakhalitsa kupyolera m’nthanthi zaumulungu za anthu ndi ziphunzitso za nthanthi, onse, kuphatikizapo osauka, akulimbikitsidwa kusangalala ndi madalitso enieni omwe amadza kuchokera ku kutumikira Mulungu. Awo omwe amatero amavomerezana ndi mtumwi Paulo, kuti “chipembedzo chipindula zonse, popeza chikhala nalo lonjezano la ku moyo uno, ndi la moyo ulinkudza.”—1 Timoteo 4:8.

[Chithunzi patsamba 29]

Kulamulira kwa Ufumu wa Mulungu kuli yankho lokha ku kusauka kwa dziko

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena