Kodi Chimene Chimachititsa Vutolo Nchiyani?
“SIKWABWINO kuthirira banja m’chere wopambanitsa!” akufuula tero maiyo. “Komatu chakudyachi chiribe m’chere chiri zii!” aumirira tero mkazi wa mwana wake. Mayiyo atangofulatira iye asiranso mchere pang’ono.
Pokhala ndi aliyense wa iwo akuchita zikhumbo zake, aŵiri onsewo potsirizira pake akudya zakuya zimene nnena ndi mmodzi wa iwo akusangalala nazo. Koma zotulukapo zake zingakhale zoipirapo kuposa pamenepo. Kusemphana kwa apongozi kungatsogolere kukukangana kwa m’maganizo ndi m’malingaliro kumene kumatha zaka zambiri.
Kwa ambiri, kukangana kwa mtundu umenewu kumawonekera kukhala kosapeweka. “Mosasamala kanthu za kumvana kumene banja lingawonekere kukhala nako, pali kuthekera kwa kukangana kwa amayi ndi mpongozi wawo,” akulemba tero Dr. Shigeta Saito, wapampando wa Japan Mental Hospital Association. Koma vutolo silolekezera Kummaŵa.
Mlembi wa Galamukani! mu Italiya akusimba kuti “mwambo wa kukwatira ndi kusamuka kukhala kaya ndi makolo amkwati kapena mkwatibwi wapangitsa mavuto m’mabanja ambiri, ndipo kaŵirikaŵiri mkazi wokwatidwa amavutika chifukwa cha mkhalidwe wodudukira ndi wankhalwe wa apongozi ake.”
Ponse paŵiri m’maiko a Kummaŵa ndi a Kummadzulo, manyuzipepala ndi magazine amadzala ndi madanga opereka uphungu waumwini wophatikizapo mikangano ya apongozi. Pamenepa, kodi chingakhale chikupangitsa mavutowo nchiyani?
Kodi Amapanga Zosankha Ndani?
Pamene akazi aŵiri agwiritsira ntchito kitchini imodzi, vuto kaŵirikaŵiri limakhala iri: Kodi adzapanga zosankha ndani? “Zimene timakonda ndi njira yochitira zinthu zimasiyana, ndipo ndinavutika maganizo nthaŵi iriyonse pamene kusamvana kunabuka,” akutero mkazi wina amene anakhalapo ndi apongozi ake kwa zaka zoposa 12.
“Kwa zaka khumi zoyambirira, tinasemphana pankhani zazing’ono,” akuvomereza tero mpongozi wina. Kusemphana kungayambire pa zinthu zazing’ono zonga ngati mmene mashati angaikidwire pa nsambo yoyanikira zovala. Ngakhale ngati akaziwo sakhala m’nyumba imodzimodziyo, mkhalidwewo ungakhale wovutitsa. Mpongozi wodzacheza yemwe amanena mawu onga akuti, “Mwana wanga samakonda nyama yake kuphikidwa mwanjirayo,” angapangitse vuto losatha. Zonsezi zikuphatikizapo mfundo ija ya kudziŵa yemwe ayenera kupanga zosankha ndipo kaamba ka ayani.
Posonya kunkhaniyi, Takako Sodei, wachiŵiri kwa profesala wa makhalidwe apanyumba pa Yunivesite ya Akazi pa Ochanomizu akuti: “Kaya wina amakhala ndi mwana wake wamwamuna limodzi ndi mpongozi wake kapena mwana wake wamkazi limodzi ndi mkamwini, kuli kosatheka kuti banja lichirikize akazi okwatidwa aŵiri opikisanirana ulamuliro. Kuli koyenerera kukhala ndi malo okhala osiyana kapena kusintha m’khalidwewo ndi kulola mmodzi kukhala wosamalira nyumba ndipo winayo kukhala mthandizi wa wosamalira nyumbayo.” Mibadwo iŵiriyo iyenera kufikira pakumvana koyenerera kozikidwa pa mkhalidwe wakuthupi ndi wamaganizo ndi zokumana nazo za okalamba, kapena kupanda chidziŵitso kwa achicheperewo.
Nkhani ya Zobisika
Pamene mibadwo iŵiri kapena yoposerapo ikhala m’nyumba imodzi, ziŵalo zabanja ziyenera kulepa zochita zawo zobisika kumlingo wakutiwakuti. Komabe, pankhaniyi, chiŵalo chirichonse mwachidziŵikire chikakhala ndi muyezo wosiyana. Banja laachicheperepo lingakhumbe kukhala ndi zochitika zobisika zochulukirapo, pamene okalamba angalakalake mayanjano owonjezereka.
Mwachitsanzo, mkazi wa mwana wina wokhala pafupi ndi Tokyo analingalira kuti apongozi ake ankadodometsa nthaŵi zobisika za okwatiranawo. Motani? Mwakumperekera zovala zake ndi zamwamuna wake, kuzipinda, ndikuziika mmalo ake. Sanakulingalire kukhala choyenera kuti apongozi ake awachitire zinthu zimenezi. Kumbali ina, apongozi ake, a Tokiko, anaipidwa nazo pamene mpongozi wawo, posesa m’nyumbamo, anachotsa zinthu zimene Tokiko anazikonda kwa zaka zambiri.
Kududukira m’zobisika kungakhale kopambanitsa. Tom ndi mkazi wake, yemwe anasamalira amake a Tom okalambawo, ankavutika maganizo ndi maulendo obwerezabwereza a mayiyo m’chipinda chawo chogona pakati pausiku. Chifukwa chochitira tero? “Ndinafuna kudzawona ngati Tom anali bwino,” anatero mayiyo. Vutolo linathetsedwe atasamukira m’nyumba ya zipinda zosanja ziŵiri ndipo maiyo ataletsedwa kukwera m’nyumba yapamwambayo.
Komabe, m’mabanja ambiri, mavuto amakuladi patadza mbadwa wachitatu.
Kusamalira Ana
M’nthaŵi zamakono, nkozolowereka kwa mayi wachichepere kuŵerenga mabuku osiyanasiyana kuti apeze uphungu wonena za kusamalira ana. Kumbali ina, agogo, pokhala ndi chizolowezi cha zaka zambiri m’kuphunzitsa ana, mwachibadwa amalingalira kukhala oyenerera kupereka uphunguwo. Komabe, kaŵirikaŵiri uphunguwo, umawonedwa kukhala kusuliza, ndipo kukangana kumatulukapo.
Takako anakumana ndi vuto limeneli pamene anali kulanga mwana wake wamwamuna wamng’onoyo. Apongozi ake ndi agogo a mwamuna wake anathamangira m’chipinda chake kukamletsa, akumafuuladi kwambiri kuposa kulira kwa khandalo. Atawona kukhala wowopsezedwa, Takako analeka kulanga mwana wakeyo. Pambuyo pake, pamene atazindikira kufunika kwa kepereka chilango, iye anasankha kuyambiranso kulangizako.—Miyambo 23:13; Ahebri 12:11.
Mayi wina wa ku Yokohama analimbananso ndi apongozi ake pambuyo pa kubadwa kwa ana. Amayi wa anawo anavutika maganizo chifukwa chakuti agogowo anapatsa anawo zakudya zomwetsa madzi asanadye chakudya chenicheni kotero kuti anakhala okhuta panthaŵi ya chakudya chenicheni.
Pothirira ndemanga vutolo, Dr. Saito akuti: “[Agogo] amapatsa adzukulu awo maswiti ndi zomwetsa madzi zina. Iwo amakhutiritsa zikhumbo zadyera za mwana. Kunena mwachidule, iwo amalekelera adzukulu awo kwa nthaŵi yonse.” Iye akulangiza kuti amai achichepere ayenera kumveketsa kuti sadzamana mwana chilango.
Kulimbanira Chikondi
M’kukangana uku kwa apongozi ndi akazi a ana awo, muli kanthu kena kachilendo kwambiri kamene kakuchitika. “Mmaganizo,” akulongosola tero Dr Saito, “mayi amalingalira kuti mpongozi wawo wawatsomphola mwana wawo. Ndithudi, iwo samatulutsa maganizo oterowo mwa mawu, popeza kuti kutero kukakhala chibwana chonkitsa. Koma, mkatimo, ganizo la kulandidwa chikondi cha mwana wawo limakhala lozama mumtima mwawo.” Chotulukapo chimakhala unansi wosalimba, ngati kusali udani weniweni pakati pawo.
Chikhoterero chimenechi chimawonekera kukhala chikukula pamene kuchuruka kwa ana m’mabanja kukuchepa. Pokhala ndi ana ochepera owasamalira, mayiyo amadziwona kukhala woyandikana kwambiri ndi mwana wake. Pambuyo pa kukhala ndi mwana wawo zaka zambiri, iwo amadziŵa bwino lomwe zimene amakonda ndi zimene samakonda. Ngakhale kuti mkwatibwi watsopanoyo amakhala wodera nkhawa ndi kukondweretsa mwamuna wake, iye amasowa chidziŵitso chathithithi chonsechi, ndiko kuti, poyambirira. Chotero mzimu wopikisana ungayambike mosavuta, mayi ndi mpongozi wake akumalimbanirana chikondi cha mwamuna mmodziyo.
Kusintha Komvetsa Chisoni
M’nthaŵi zakale mu Japan pansi pa chiphunzitso cha Confucius, pamene mikangano yabanja yoteroyo inkachitika, mpongoziyo ankathamangitsidwa—kusudzulidwa. Ndipo nkhaniyo inali kuthera pompo. Komabe, lerolino, mkhalidwewo ngwosiyana.
Chiyambire Nkhondo Yadziko II, mbadwa wa achichepere wakhala ndi ulamuliro pakayendetsedwe ka banja, ndipo mbadwo wa okalamba ukutaikiridwa ndi chisonkhezero ndi ulamuliro wawo. Pang’ono ndi pang’ono, mkhalidwewo wasintha. Tsopano makolo okalamba akunyanyalidwa m’zipatala ndi m’nyumba zina. Nkomvetsa chisoni motani nanga kuwona mkhalidwe umenewu m’chitaganya chimene kulemekeza okalamba kunali mkhalidwe wozolowereka!
Kodi chikhoterero cha kunyanyala okalamba chingathetsedwe motani? Kodi pali njira iriyonse mu imene akazi aŵiri angakhalire limodzi mwamtendere m’nyumba imodzi?
[Chithunzi patsamba 23]
Kuvomerezana kwabwino kuyenera kufikiridwa ponena za amene adzapanga zosankha