Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g90 6/8 tsamba 6-7
  • Mapindu Osintha ndi Kupita kwa Mbiri

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mapindu Osintha ndi Kupita kwa Mbiri
  • Galamukani!—1990
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mapindu Osiyanasiyana Akale
  • Mapindu a Makhalidwe Abwino Osiyana Alerolino
  • Munthu Wakhazikitsa Miyezo Yakeyake ya Mapindu a Makhalidwe Abwino
  • Muziwaphunzitsa Kufunika Kokhala ndi Makhalidwe Abwino
    Galamukani!—2019
  • Mfundo za M’dzikoli Zikusinthasintha
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Kodi Makhalidwe Akumka Kuti?
    Galamukani!—1993
  • Mapindu a Makhalidwe Abwino Amene Amabweretsa Chimwemwe
    Galamukani!—1990
Onani Zambiri
Galamukani!—1990
g90 6/8 tsamba 6-7

Mapindu Osintha ndi Kupita kwa Mbiri

“DONGOSOLO la malamulo amene munthu amatsatira (kapena amafunikira kutsatira) m’moyo wake waumwini ndi moyo wake wamayanjano.” Mmenemo ndi mmene Encyclopœdia Universalis Yachifrenchi ikulongosolera liwu lakuti “makhalidwe abwino.”

Kulongosola kumeneku kumagwiradi ntchito kwa aliyense. Kumaphatikizapo wokhulupirira amene amatsatira malamulo amakhalidwe abwino a chipembedzo chake ndiponso munthu amene samamatira dongosolo lirilonse la makhalidwe kapena chipembedzo koma ali ndi malamulo amakhalidwe abwino ena ake amene amatsogoza moyo wake. Ngakhale wokana ulamuliro, amene amanena kuti alibe “Mulungu ndiponso mbuye,” wasankha mapindu ake, ngati kokha ali ndi kuyenera kwa kupanga zosankha zakezake.

Koma kodi ndiati amene ali maziko a mapindu ameneŵa? Kodi zosankha za makhalidwe abwino zoterozo zazikidwa pa chiyani? Kodi izo zimasintha ndi nthaŵi?

Mapindu Osiyanasiyana Akale

“Spartan” ndilo liwu logwiritsiridwa ntchito m’zinenero zambiri kulongosola kusoŵeka kwa chitonthozo. Liwulo limalozera ku mikhalidwe yankhanza pansi pa imene nzika zachichepere za mzinda wakale Wachigiriki wa Sparta zinaphunzitsidwa. Pokhala olekanitsidwa ndi makolo awo kuyambira pa msinkhu wachichepere kwambiri, iwo anayenera kuphunzira chimvero chotheratu. Cholinga cha kuphunzitsa kumeneku chinali kuwapanga kukhala asilikali oyenera kutsanzira.

Anthu ena anatsatira mapindu osiyana. Mwachitsanzo, Israyeli wakale adali ndi mpambo wa malamulo operekedwa kwa Mose ndi Mulungu. Malamulo amenewo anaphatikizapo ziletso zakadyedwe, zakuthupi, zamakhalidwe, ndi zauzimu. Aisrayeli anayenera kulambira Yehova Mulungu yekha.

Ponena za mkhalidwe wa kugonana, Chilamulo cha Mose chinaletseratu dama, chigololo, kugonana kwa ofanana ziŵalo, ndi kugonana ndi zinyama. Cholinga chake chinali kupatula Aisrayeli kwa anansi awo, osati kokha mwachipembedzo komanso mwamakhalidwe abwino. Ichi chinali chifukwa chakuti anthu ambiri ozungulira Israyeli ankachita kulambira koluluzika, kosakaza kwa kugonana, kuphatikizapo kuchita chigololo kwa amuna ndi akazi kwa pakachisi. Ena anafikira pa kupereka ana awo monga nsembe kwa milungu yawo yonama.

M’zaka za zana loyamba C.E., lamulo lopangidwa ndi bungwe la atumwi Achikristu ndi akulu m’Yerusalemu linalangiza Akristu kutsatira mkhalidwe wabwino wakugonana wofananawo umene Ayuda ankatsatira, akumawauza kuti ‘asale dama.’ Mogwirizana ndi Dictionnaire de la Bible ya Vigouroux, malangizo ameneŵa anali opindulitsa kwambiri, popeza kuti dama linali kuchitidwa mofala pakati pa akunja a nthaŵi imeneyo.—Machitidwe 15:29.

Kuchuluka kwa miyezo ya makhalidwe abwino m’mbiri yonse, ndi nyengo zomasiyanasiyana za kulekerera ndi kusamalitsa kwa malamulo a makhalidwe kunapitirira. Kugonana kwa ofanana ziŵalo, kumene kunatsutsidwa mwamphamvu m’Nyengo Zapakati, kunalekereredwa kwambiri mkati mwa Renaissance (Nyengo ya Kusintha kwa) ku Ulaya. Mu Switzerland, pamene Calvin anakhazikika mu Geneva mkati mwa Kukonzanso, iye anayambitsa nyengo ya makhalidwe abwino osagonjetseka. Kumbali ina, zaka 200 pambuyo pake, French Revolution inapangitsa kukhala alamulo mapindu amene kalelo adali okanidwa. Inayamba kuchilikiza “ufulu wa makhalidwe abwino” atsopano ndi kuchipanga kukhala chopepuka kupeza chisudzulo.

Mapindu a Makhalidwe Abwino Osiyana Alerolino

Lerolino, ngakhale mkati mwa chitaganya chimodzimodzicho, anthu ali ndi miyezo yosiyana ya makhalidwe abwino. Pali awo amene amachilikiza malamulo osamalitsa a makhalidwe abwino, pamene ena amachilikiza “ufulu” wa makhalidwe abwino.

Malamulo a makhalidwe abwino asintha mofulumira. “Kwa anthu ambiri Achifrenchi, chigololo chiri ndi tanthauzo lachindunji. Nchoipa ndipo chosemphana ndi makhalidwe abwino,” likutero bukhu Lachifrenchi lakuti Francoscopie. Komabe, magwero amodzimodziwo akudziŵitsa kuti kwa ena ambiri “kusakhulupirika kwa muukwati sikuwonedwanso kukhala kuthaŵa koma kuyenera, kuyenera kumene sikuyenera kukaikira chikondi chimene okwatiranawo angakhale nacho kwa wina ndi mnzake, koma, mosiyanako, chiyenera kuchilemeretsa ndi kuchilimbikitsa.”

Kuchotsa mimba kuli mbali ina imene malamulo a mkhalidwe asintha mofulumira. Pamene kuli kwakuti kuchotsa mimba kudakali upandu m’maiko ena, kumalekereredwa—ngakhale kulamulidwa—mu ena. Nzosangalatsa kudziŵa kuti French Medical Association inalingalira kuchotsa mimba kukhala upandu kufikira pamene kunaikidwa kukhala kwalamulo mu 1974. Lerolino, anthu ambiri Achifrenchi amalingalira iko kukhala kolandirika mwamakhalidwe.

Komabe, kodi makhalidwe abwino amenewo azikidwa pachiyani? Kodi mapindu athu a makhalidwe abwino ayenera kukhala opanda mphamvu kwenikweni ndi kusintha mogwirizana ndi mikhalidwe?

Munthu Wakhazikitsa Miyezo Yakeyake ya Mapindu a Makhalidwe Abwino

M’zaka mazana onsewa, anthanthi alingalira malingaliro ambiri kuyesera kuyankha mafunso oterowo. Ena alingalira za kukhalapo kwa ‘malamulo a makhalidwe a chilengedwe chonse’ koma sangagwirizane pa lingaliro lakuti kodi ndi kulongosola kwa yani kwa makhalidwe abwino kumene kuyenera kukhala muyezo.

Ena alingalira kuti kudera nkhaŵa kaamba ka munthu mnzako kuyenera kutsogoza mkhalidwe wa munthu. Koma kumene munthu wina amakulingalira kukhala kudera nkhaŵa koyenera kwa ena sikungawonedwe motero ndi winawake. Monga chitsanzo, kwa zaka mazana ambiri osunga akapolo analingalira kuti kudyetsa ndi kupatsa malo ogona kwa akapolo awo kunali kudera nkhaŵa koyenera, koma akapolowo analingalira kuti kudera nkhaŵa koyenera kuyenera kutulukapo m’kumasulidwa kwawo kuchoka mu ukapolo.

Palibe kukaikira kuti kusiyana kwakukulu kwa malingaliro owombana amene anthanthi ali nako ponena za miyezo ya makhalidwe abwino kwasokoneza anthu ambiri. Malingaliro awo sanatulutse muyezo wofala wa makhalidwe abwino, ndiponso kupanga kwawo nthanthi sikunatsogoze banja la anthu ku mtendere ndi umodzi. Kunena zowona, malingaliro awo ambiri ndiponso owombana atsogoza chiŵerengero chokulira cha anthu kutsimikizira kuti muyezo waumwini wa munthu wa makhalidwe abwino ngwabwino mofanana ndi wa “akatswiri.”

Ichi ndicho chifukwa chake ambiri lerolino atsatira lingaliro la wanthanthi Wachifrenchi Jean-Paul Sartre, amene analingalira kuti munthu ayenera kukhala woweruza wa iyemwini ponena za nkhani za makhalidwe abwino. Kulingalira kotereku kwatsatiridwa ndi opita ku tchalitchi ambiri. Mwachitsanzo, akuluakulu Achikatolika akudera nkhaŵa chifukwa chakuti Akatolika ambiri satsatira konse ziphunzitso za tchalitchi pa nkhani za kugonana ndi kugwiritsira ntchito kwa mankhwala oletsa kutenga pathupi oletsedwa ndi tchalitchi.

Phunziro la mbiri yakale ndilakuti malamulo osiyanasiyana a makhalidwe abwino akhazikitsidwa ndi anthu, koma m’kupita kwa nthaŵi malamulo oterowo akaikiridwa, kusinthidwa, kapena kuiwalidwa. Komabe, malamulo amakhalidwe abwino a Baibulo otchulidwa poyambirirapo mu nkhaniyi sali minkhole ya kulingalira kwachinyengo kwa akatswiri anthanthi kapena zitaganya zosintha. Kodi malamulo amakhalidwe abwino Abaibulo oterowo ali ndi phindu lanji lerolino? Kodi nkotheka kuwatsatira?

[Mawu Otsindika patsamba 7]

“KUSAKHULUPIRIKA KWA MUUKWATI SIKUWONEDWANSO KUKHALA KUTHAŴA KOMA KUYENERA”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena