Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g90 6/8 tsamba 8-9
  • Mapindu a Makhalidwe Abwino Amene Amabweretsa Chimwemwe

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mapindu a Makhalidwe Abwino Amene Amabweretsa Chimwemwe
  • Galamukani!—1990
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zotulukapozo
  • Maziko a Makhalidwe Abwino Koposa
  • Mapindu Achikale?
  • Mapindu Amene Amakupangani Kukhala Wachimwemwe
  • Muziwaphunzitsa Kufunika Kokhala ndi Makhalidwe Abwino
    Galamukani!—2019
  • Kutsatira Mfundo Zosasinthasintha
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Makhalidwe Abwino Angakuthandizeni Kuti Muzisangalala
    Galamukani!—2013
  • Mapindu Osintha ndi Kupita kwa Mbiri
    Galamukani!—1990
Onani Zambiri
Galamukani!—1990
g90 6/8 tsamba 8-9

Mapindu a Makhalidwe Abwino Amene Amabweretsa Chimwemwe

KODI mwana angachitenji ngati wasiyidwa patsogolo pa gome limene ladzazidwa ndi zakudya zabwino kuphatikizapo masiwiti? Ngati palibe amene amtsogolera, mwachidziŵikire iye angakonde kusankha kudya zimene amakonda kwambiri—mwinamwake masiwiti—kufikira atadwala.

Kulankhula mwa makhalidwe abwino, munthu wayang’anizana ndi zosankha. Kodi nchiyani chimene akufuna kwambiri? Moyo wabanja wachimwemwe ndi mtsogolo mwachisungiko kapena, mosasamala kanthu za zotulukapo, moyo wa tsiku ndi tsiku wozikidwa pa chisangalalo? Mosasamala kanthu za zimene angasankhe, chosankha chake chidzaumba moyo wake ndipo chidzayambukira mtsogolo mwake—mwaubwino kapena moipa.

Zotulukapozo

Zipatso za kusintha m’zakugonana ndi ufulu wosaikiridwa malire sizinakhale zabwino. Anthu amene anachita zinthu monga mmene anafunira akumana ndi mavuto ambiri osafunidwa: nyumba zosweka, mimba zosafunidwa, imfa yochititsidwa ndi AIDS ndi matenda ena opatsirana mwakugonana, miyoyo yosakazidwa ndi kugwiritsira ntchito molakwa mankhwala ogodomalitsa, ndi zotulukapo zina zosakhumbika. Zotulukapo zoipa zimenezi zimayenerera kulongosola kodziŵika kwa Baibulo pa Miyambo 16:25: ‘Iripo njira iwoneka kwa mwamuna ngati yoongoka, koma matsiriziro ake ndi njira za imfa.’—Onaninso Agalatiya 5:19-21.

Dyera lopitirira muyeso ndi ufulu wopanda nawo thayo zikuyenereranso kalongosoledwe ka nthaŵi yathu kopezeka pa 2 Timoteo 3:1-4: ‘Koma zindikira ichi, kuti masiku otsiriza zidzafika nthaŵi zowawitsa. Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, odzitamandira, odzikuza, amwano, osamvera akuwabala, osayamika, osayera mtima, opanda chikondi chachibadwidwe, osayanjanitsika, akudyerekeza, osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino, achiwembu, aliuma olimbirira, otukumuka mtima, okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu.’

Maziko a Makhalidwe Abwino Koposa

Zonsezi zikusonyeza kufunika kwa magwero a mapindu oposa a munthu kotero kuti tingayende mwanzeru m’nthaŵi zino zovuta. Yeremiya, mmodzi wa alembi a Baibulo, anavomereza zimenezi pamene ananena kuti: ‘Inu Yehova, ndidziŵa kuti njira ya munthu siri mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.’—Yeremiya 10:23.

Koma kodi ndani amene angakhazikitse maziko kaamba ka mapindu abwino koposa a makhalidwe abwino? M’bukhu lake lakuti Cours de philosophie, profesa Wachifrenchi Armand Cuvillier akulongosola kuti iye, mofanana ndi anthu anthanthi ambiri, watenga “umunthu wa munthu kukhala phindu lamaziko.” Komabe, iye akutikumbutsa kuti malamulo onse a makhalidwe abwino ozikidwa pa munthu ngosalimba ndipo m’kupita kwa nthaŵi angalowedwe mmalo ndi ena.

Wopanga makina kaŵirikaŵiri amakhala munthu wofikapo kuwapanga kugwira ntchito bwino koposa. Ziri momwemonso ndi Mulungu ndi munthu. Monga Mlengi wa munthu, Yehova ali m’malo abwino akumusonyeza mapindu amene ayenera kukhala nawo, ndi chifukwa chake. M’Baibulo, Yehova amadzitcha kukhala Amene ‘akutiphunzitsa kupindula, Amene akutitsogolera m’njira yoyenera ife kupitamo.’—Yesaya 48:17.

Mapindu Achikale?

Kodi mapindu a makhalidwe abwino Abaibulo angagwiritsiridwe ntchito m’nthaŵi yathu? Zoposa zaka 1,900 zapitazo, mtumwi Paulo anapereka ndandanda ya mikhalidwe imene imafunikira kwa atumiki a Mulungu. Iye anatchula ‘chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso.’ Kodi mikhalidwe imeneyi njosafunika kwambiri lerolino? Kutalitali! Pamene kuli kwakuti mikhalidwe yasintha, malamulo amakhalidwe abwino apamwamba ameneŵa adakali abwino koposa.—Agalatiya 5:22, 23.

Zofananazo zinganenedwe ponena za zinthu zimene Baibulo limaletsa. Mwachitsanzo, kodi Mulungu anawonongeranji mizinda ya Sodomu ndi Gomora? Wophunzira Yuda akulongosola kuti chinali chifukwa chakuti nzika zake “zinadzipereka zokha ku mkhalidwe wachisembwere ndi zoipa.” Yuda akuwonjezera kuti kuwonongedwa kwawo kumatumikira monga “chenjezo losatha.” Popeza kuti mbiri imeneyi ndi zochitika zina zofanana nazo “zinalembedwa kutilangiza,” “kutichenjezaife,” maphunziro a makhalidwe abwino ochokera ku izo adakali ogwira ntchito.—Yuda 7, Phillips; Aroma 15:4; 1 Akorinto 10:11.

Mapindu Amene Amakupangani Kukhala Wachimwemwe

Kumbukirani kuti Baibulo nlapadera. Lilandireni, ‘osati monga mawu a anthu, komatu monga momwe ali ndithu, mawu a Mulungu.’ (1 Atesalonika 2:13) Pa mabuku mamiliyoni ambiri amene alimo m’dziko, Baibulo lokha ndilo ‘louziridwa ndi Mulungu, ndipo lingawongolere zinthu.’ (2 Timoteo 3:16) Ilo lokha ndilo lingatipatse mapindu abwino koposa ndi kusonyeza mmene amatsogozera ku moyo wamuyaya m’dziko latsopano. Ndithudi, kulisanthula ilo ndiko njira yanzeru.

Zimenezo ndizo zimene mwamuna wachichepere wotchedwa Joël anachita. Zaka zingapo zapitazo, iye anayenda m’makwalala a tauni yakwawo mu Falansa ndi achichepere ena—okhala ndi zida. Iye anali wodziŵika chifukwa cha kupsya kwake mtima msanga, ndiponso adali wogulitsa mankhwala ogodomalitsa ndi wachisembwere. Joël anaphunzira ponena za Baibulo ndi chiyembekezo chimene limabweretsa, ndipo, m’kupita kwa nthaŵi, anasintha kotheratu, kuleka machitachita onse amene Baibulo limatsutsa. Mabwenzi ake angapo anakhutiritsidwa kuti iye anapeza chowonadi, chotero nawonso anapanga masinthidwe aakulu m’miyoyo yawo ndipo anabatizidwa monga Mboni za Yehova.

Ndithudi, ambiri a awo amene amakhala Mboni za Yehova sanali kutsogoza moyo wosalingana ndi malamulo amakhalidwe abwino a Baibulo monga mmene anachitira Joël ndi mabwenzi ake. Koma onse amene amakhala Mboni amavomereza kulingaliranso mapindu otsogoza miyoyo yawo—ngakhale ngati sadali anthu oipa—ndipo akhutiritsidwa kuti apeza dongosolo la mapindu limene lingawapange kukhala achimwemwe.

Kuzungulira dziko lonse, pafupifupi Mboni mamiliyoni anayi zikuyesera kukhala mogwirizana ndi malamulo amakhalidwe abwino ameneŵa tsiku lirilonse, mosasamala kanthu za dziko kapena mtundu wa chitaganya umene amakhalamo. Iwo amaikanso zabwino za Ufumu wa Mulungu choyamba, kupatsa mapindu auzimu malo oyamba m’miyoyo yawo. Kodi bwanji osalandira chiitano chawo chokuthandizani kusanthula madalitso amene mungapeze kuchokera ku mapindu ameneŵa? ‘Mtendere wochuluka’ walonjezedwa kwa awo amene akupanga chosankha chimenechi.—Salmo 119:165; Mateyu 6:33.

[Chithunzi patsamba 9]

Anthu amafunikira mapindu amene amapyola nthanthi za anthu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena