Mafunso Omwe Amafunikira Kuyankhidwa
NTHAŴI inayake m’kukhalapo kwanu ndi moyo, mungakhale munafunsapo kuti: ‘Ngati Mulungu alikodi, kodi nchifukwa ninji walolera kuipa kochulukaku? Ndipo kodi nchifukwa ninji wakulola kwanthaŵi yaitali chotere, m’mbiri yonse ya anthu? Kodi kuvutikaku kudzatha konse?’
Chifukwa cha kusapeza mayankho okhutiritsa ku mafunso oterowo, anthu ambiri amakwiyitsidwa. Ena amapatuka pa kukhulupirira Mulungu, kapena mwina iwo amampatsa liŵongo la masoka awo.
Mwachitsanzo, mwamuna wina amene anapulumuka Chipiyoyo, kuphedwa kwa anthu mamiliyoni ambiri kochitidwa ndi Nazis m’Nkhondo Yadziko ya II, anakwiyitsidwa kwambiri kwakuti anati: “Mutaunyambita mtima wanga, ungakupheni ndi paizoni.” Mwamuna wina amene anavutika ndi chotulukapo cha chizunzo chodzetsedwa ndi fuko, chimene chinapha mabwenzi ndi ziŵalo zabanja m’Nkhondo Yadziko ya I, mokwiya anafunsa kuti: “Kodi Mulungu ameneyu anali kuti pamene tinkamufuna?”
Chotero, anthu ambiri ngozizwitsidwa nazo. Malinga nkulingalira kwawo, kumamvekera kukhala kosalingalirika kwa Mulungu wodzala ndi ubwino ndi chikondi kulola zinthu zoipa kuchitika kwanthaŵi yaitali chotero.
Zimene Anthu Achita
Nzowonadi kuti anthu achita zoipa zazikulu molimbana ndi ena mkati mwa zaka mazana ambiri—kwenikweni, kwa zaka zikwi zambiri. Ukulu ndi kupweteka kwa zonsezi nkovuta kukulingalira.
Pamene kutsungula kunawonekera kupita patsogolo, anthu adapanga zida zowopsyabe moposerapo za kuwonongera kapena kulemazika nazo ena: mfuti zazikulu, mfuti zachifefe, ndege zankhondo, akasinja, mamisayelo, zida zoponyerako malaŵi a moto, zida za makemikolo ndi za nyukiliya. Monga chotulukapo, m’zaka za zana lino zokha, nkhondo za mitundu zapha pafupifupi anthu miliyoni zana limodzi! Anthu ena mazana a mamiliyoni owonjezereka avulazidwa kapena kuvutika m’njira zina. Ndipo unyinji wa chuma chowonongedwa, monga ngati nyumba ndi katundu, nzosatha kuziyerekeza.
Talingalirani za chisoni chachikulu, kuvutitsidwa, ndi misozi imene nkhondo yapangitsa! Kaŵirikaŵiri kwambiri amene avutika ndiwo anthu wamba opanda liŵongo: amuna ndi akazi okalamba, ana, makanda. Ndipo kaŵirikaŵiri, anthu ambiri amene anadzetsa kuipaku sanalangidwe.
Padziko lonse, kuvutika kudakapitirizabe kufikira tsopano. Tsiku lirilonse, anthu amaphedwa kapena mwinamwake kukhalitsidwa mnkhole wa upandu. Iwo amavulazidwa kapena kufera m’ngozi, kuphatikizapo ‘zochitika zachilengedwe’ zonga ngati namondwe, zigumula, ndi zivomezi. Iwo amavutika ndi kupanda chilungamo, tsankhu, umphaŵi, njala, kapena matenda, kapena m’njira zina zambiri.
Kodi ndimotani mmene Mulungu wabwino adakalengera chinthu chinachake—anthu—amene avutika moipa chotero, mwakaŵirikaŵiri, kwa zaka mazanamazana?
Kupanikiza m’Thupi la Munthu
Kupanikizaku kumawonekera ngakhale m’matupi a anthu. Asayansi ndi ena amene akuphunzira amavomereza kuti thupi la munthu nlopangidwa modabwitsa, mozizwitsa.
Tangolingalirani ziŵalo zake zochepa: diso la munthu lochititsa chidwi, limene palibe kamera imene ingathe kulitsanzira; ubongo wozizwitsa, umene umapangitsa kompyuta yapamwamba kwenikweni kusakhala kanthu; mmene mbali zazing’ono zathupi zimagwirizanirana popanda ife kugwirako; kuzizwitsa kwa kubadwa kwa munthu, kumene kumabweretsa khanda lokongola—chithunzi cha makolo ake—m’miyezi isanu ndi inayi yokha. Anthu ambiri amatsimikiza kuti kakonzedwe ka luso kameneka, thupi la munthu, kadafunikira kulengedwa ndi Wolinganiza waluso—Mlengi, Mulungu Wamphamvuyonse.
Komabe, nchachisoni kuti, thupi lodabwitsa limodzimodzili limafokerafokera. M’kupita kwanthaŵi ilo limagonjetsedwa ndi matenda, ukalamba, ndi imfa. Pomalizira pake ilo limagwera m’nthaka. Nchachisoni chotani nanga! Panthaŵi imenedi munthu amafunikira kupindula ndi zokumana nazo zokundikidwa m’zaka makumi ambiri ndikukhala wanzeru, mpamenenso thupi limafooka. Nkusiyana komvetsa chisoni chotani nanga pomalizira pake, kumene umoyo, thanzi, ndi kukongola kumene kudali kodzala m’thupi pa kuyambika kwake!
Kodi nchifukwa ninji Mlengi wachikondi akapangira chinthu chabwino kwabasi chonga thupi la munthu, ndikungolilola kufa mwachisoni? Kodi nchifukwa ninji iye angapangire chinthu chaluso chimene chimayamba bwino zedi, chodzala ndi ubwino, koma chomwe chimathanso moipa tere?
Mmene Ena Amakulongosolera
Anthu ena anena kuti kuipa ndi kuvutika ndiko ziwiya za Mulungu za kuwongolera mkhalidwe wathu kupyolera m’mavuto. Mtsogoleri wachipembedzo cha Methodist anati: “Kuvutitsidwa kwa abwino m’manja mwa oipa ndiko mbali ya kakonzedwe ka chipulumutso ka Mulungu.” Iye anatanthauza kuti, kuti akonze mkhalidwe ndi kupulumutsidwa, anthu abwino ayenera kuvutika ndi ntchito za anthu oipa, monga mbali ya kakonzedwe ka Mulungu.
Koma kodi tate wachikondi wa munthu angayesere kuwongolera mkhalidwe wa ana ake mwakukonzekera kuwalola kukhalitsidwa m’nkhole wa upandu wolusa? Talingaliraninso, kuti achichepere ambiri amaphedwa m’ngozi kapena kufwambidwa kapena kufa m’nkhondo. Minkhole yachichepere imeneyo sidzakhala konse ndi mwaŵi wina wa kuwongolera mkhalidwe wawo popeza kuti adzakhala akufabe. Chotero lingaliro lakuti kuvutika kumaloledwa kuchitira kuti mkhalidwe uwongoleredwe nlopandatu nzeru.
Palibe tate wa munthu wolingalira bwino wokhala ndi chikondi amene angafune kuvutika kapena tsoka kugwera okondeka ake. Kwenikweni, tate amene angakonzekere okondedwa ake kuti avutike ndi cholinga cha kufuna ‘kukonza mkhalidwe’ akalingaliridwa kukhala wosayenerera, ngakhale wopenga m’maganizo.
Pamenepo kodi kunganenedwe mwanzeru kuti Mulungu, Tate wamkulu wachikondi, Mlengi wa chilengedwe chonse wa nzeru zonse, anakonza dala kuvutika kukhala mbali ya ‘kakonzedwe kake kaamba ka chipulumutso’? Uku kukakhala kumukoloweka ndi mkhalidwe wankhalwe ndi woipa mopambanitsa, mkhalidwe umene tonsefe timaulingalira kukhala wosavomerezedwa ngakhale kwa anthu osaganiza bwino.
Kupeza Mayankho
Kodi ndikuti komwe tingapite kaamba ka mayankho a mafunso onena za kulola kwa Mulungu kuvutika ndi kuipa? Popeza kuti mafunsowo akuphatikiza Mulungu, nkwanzeru kuti tiwone chimene iyemwiniyo akupereka monga mayankho.
Kodi mayankho ake tingawapeze bwanji? Mwa kupita ku magwero amene Mulungu mwiniyo akuti anawalemba monga chotsogoza munthu—Baibulo Loyera, Malemba Opatulika. Mosasamala kanthu za mmene munthu aliyense angawalingalire magwero amenewo, iwo ngoyenerera kuwasanthula, popeza kuti, monga mmene mtumwi Paulo ananenera kuti: ‘Lemba lirilonse adaliuzira Mulungu ndipo lipindulitsa pa . . . chikonzero.’ (2 Timoteo 3:16) Iye analembanso kuti: ‘Pakulandira mawu a Uthenga wa Mulungu, simunawalandira monga mawu a anthu, komatu monga momwe ali ndithu, mawu a Mulungu.’a—1 Atesalonika 2:13.
Kufunafuna mayankho ku mafunso onena za kuloledwa kwa kuipa nkoposatu kuphunzira zaluntha. Mayankho ake ngofunikira kumvetsetsa chimene chikuchitika tsopano lino padziko lapansi, chimene chidzachitika kutsogolo, ndi mmene aliyense wa ife akuyambukiridwira.
Nkwathu kulilola Baibulo, chokambirana nacho banja la anthu cha Mulungu, kuti lidzilankhulire. Nangano, kodi nchiyani chimene limanena ponena za mmene kuvutika kunayambira ndi chifukwa chimene Mulungu amakulolera?
Mfungulo yakuti timvetsetse mayankho ake njokhudza mmene tinapangidwira m’maganizo ndi m’malingaliro. Baibulo limasonyeza kuti Mlengi anaika mwa anthufe mkhalidwe wapadera uwu: kukhumba ufulu. Tiyeni tilingalire mwachidule chimene chaphatikizidwadi muufulu wa anthu ndi mmene ichi chimachitira umboni kulola kwa Mulungu kuvutika.
[Mawu a M’munsi]
a Kaamba ka kufotokozedwa kwaumboni wakuti Baibulo nlouziridwadi ndi Mulungu, onani bukhu lakuti The Bible—God’s Word or Man’s?, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.