Chigawo 1
Kodi Mulungu Amatisamaliradi?
1, 2. Kodi ndi funso lotani limene anthu amafunsa ponena za Mulungu, ndipo chifukwa ninji?
PANTHAŴI ina mmoyo wanu, mungakhale mutafunsa kuti: ‘Ngati kuli Mulungu amene amatisamaliradi, kodi n’chifukwa ninji walola kuvutika kochuluka chonchi?’ Tonsefe tinavutikapo kapena tikudziŵa wina wake amene watero.
2 Ndithudi, m’mbiri yonse anthu amva kupweteka ndi chisoni kuchokera kunkhondo, nkhalwe, upandu, chisalungamo, umphaŵi, matenda, ndi imfa za okondedwa. M’zaka za zana lathu la 20, nkhondo zapha anthu oposa mamiliyoni 100. Mamiliyoni ena mazana ambiri avulazidwa kapena atayikiridwa ndi nyumba ndi chuma. Zinthu zambiri zochititsa mantha zachitika m’nthaŵi yathu, zikumadzetsa chisoni chachikulu, misozi yochuluka, ndi lingaliro la kusoŵa chiyembekezo kwa anthu osaŵerengeka.
3, 4. Kodi ndi motani mmene ambiri amalingalilira ponena za kuloleza kwa Mulungu kuvutika?
3 Anthu ena akwiya ndipo alingalira kuti ngati Mulungu aliko, iye kwenikweni samatisamala. Kapena iwo angalingaliredi kuti kulibe Mulungu. Mwachitsanzo, mwamuna wina amene anavutika ndi chizunzo cha fuko chimene chinachititsa imfa yamabwenzi ndi achibale m’Nkhondo Yadziko I anafunsa kuti: “Kodi Mulungu anali kuti pamene tinamfuna?” Wina amene anapulumuka kuphedwa kwa mbanda kwa mamiliyoni ambiri kochitidwa ndi Anazi m’Nkhondo Yadziko II anali wachisoni kwambiri ndi kuvutika kumene anawona kotero kuti anati: “Ngati mukananyambita mtima wanga, ukanakutulutsirani poizoni.
4 Chotero, anthu ambiri sakumvetsetsa chifukwa chake Mulungu wabwino akalolera zinthu zoipa kuchitika. Iwo amakayikira ngati iye amatisamaliradi kapena ngati ndi iko komwe iye aliko. Ndipo ambiri a iwo amalingalira kuti kuvutika kudzakhala mkhalidwe wa anthu nthaŵi zonse.
Kusiyapo ngati kutasonyezedwa mwa njira ina, Mawu ogwidwa a Malemba n’ngochokera mu Revised Union Nyanja Version ndi New World Translation of the Holy Scriptures—With References, Kope la 1984, NW akumakhala chidule chake
[Chithunzi pamasamba 2, 3]
Kodi dziko latsopano lopanda kuvutika layandikira?