Kodi Ndimphatso ya Moyo Kapena Mpsopsono wa Imfa?
“Kodi ndi anthu angati amene afunikira kumwalira? Kodi ndi imfa zingati zimene mukufuna? Mutipatse chiŵerengero cha imfa zimene mukufuna kuti mukhulupirire kuti ichi chikuchitikadi.”
DON FRANCIS, nduna ya CDC (U.S. Centers for Disease Control), anamenyetsa nkhonya yake pagome pamene ankafuula mawu omwe ali pamwambawo pamsonkhano wa oimira akuluakulu a indasitale ya nkhokwe zosungira mwazi. CDC inkayesera kukhutiritsa ankhokwe zosungira mwazi kuti AIDS inkafalikira kupyolera mwa dongosolo lopereka mwazi la dzikolo.
Osunga mwaziwo sanakhutiritsidwe. Iwo anatcha umboniwo kukhala wopanda mphamvu—kokha nkhani zingapo—ndipo anasankha kusawonjezera kupima kapena kufufuzidwa kwa mwazi. Pamenepo padali pa January 4, 1983. Miyezi isanu ndi umodzi pambuyo pake, prezidenti wa American Association of Blood Banks ananena kuti: “Pali ngozi yochepa kapena palibiretu ngozi kwa anthu aunyinji.”
Kwa akatswiri ambiri, padali umboni wokwanira kupangitsa kachitidwe kena kake. Ndipo chiyambire pamenepo, “nkhani zingapo” zoyambirira zimenezo zakula mochititsa mantha. Isanafike 1985, mwinamwake anthu 24,000 anathiridwa mwazi woyambukiridwa ndi kachilombo ka HIV (Human Immunodeficiency Virus), kamene kamapangitsa AIDS.
Mwazi woipitsidwa ndinjira yokhutiritsa kwambiri yofalitsira kachirombo ka AIDS. Mogwirizana ndi The New England Journal of Medicine (December 14, 1989), painti imodzi ya mwazi inganyamule kachirombo kokwanira kupangitsa kuyambukiridwa 1.75 miliyoni! CDC inauza Galamukani! kuti pofika June 1990, mu United States mokha, anthu 3,506 anali atayambukiridwa kale ndi AIDS yochititsidwa ndi kuthiridwa mwazi, mbali za m’mwazi, ndi kudzalidwa minyewa.
Komatu zimenezo ziri ziŵerengero zokha. Izo sizingayambe kusonyeza kuya kwa masoka amunthu payekha oloŵetsedwamo. Mwachitsanzo, talingalirani za tsoka la Frances Borchelt, wazaka zakubadwa 71. Iye anawauza madokotala mwagogogo kuti sakufuna kuthiridwa mwazi. Komabe iye anathiridwa mwazi. Iye anamwalira mowawitsa ndi AIDS pamene banja lake linkapenyerera popanda thandizo.
Kapena talingalirani za tsoka la msungwana wa zaka 17 zakubadwa amene ankavutika ndi matenda a kumwezi, amene anapatsidwa mayuniti aŵiri a mwazi kuti mwazi wake woperewera uwonjezedwe. Pamene anali ndi zaka zakubadwa 19 ndipo ali ndi pathupi, iye anapeza kuti kuthiridwa mwaziko kunampatsa kachirombo ka AIDS. Pamsinkhu wa zaka 22 iye anayambukiridwa ndi AIDS. Mosasamala kanthu za kuuzidwa kuti akamwalira posachedwapa ndi AIDS, iye anatsalabe wokaikira ngati anapatsira matendawo kwa khanda lake. Ndandanda ya masokawo imapitirizabe, kuyambira pa makanda mpaka okalamba, padziko lonse.
Mu 1987 bukhu lakuti Autologous and Directed Blood Programs linachitira chisoni kuti: “Mwamsanga pamene magulu oyambirira angozi kwenikweni anazindikiridwa, panabwera zosayembekezereka izi: chisonyezero chakuti matenda akupha kwenikweniwa [AIDS] angathe ndipo ankayambukitsidwa ndi mwazi wosonkhedwa mwaufulu. Ichi chinali chachisoni pamagwero onse amankhwala; kuti mphatso yopatsa moyo yamtengo wapataliyi ya mwazi ingatembenuke kukhala chipangizo chodzetsera imfa.”
Ngakhale mankhwala opangidwa ndi plasma anathandiziranso kuwanditsa mliriwu padziko lonse. Odwala matenda a zilonda zosapola, omwe ambiri a awa amagwiritsira ntchito magwero okhala mu plasma oumitsa msanga mwazi pachilonda kuti achilitse matenda awo, anaphedwa. Mu United States, pakati pa 60 ndi 90 peresenti ya awa anayambukiridwa ndi AIDS pamene njira zisanakhazikitsidwe za kupima mankhwalawo kuti awachotsere kachilombo ka HIV.
Chikhalirechobe, mpaka lerolino, mwazi ngwopanda chisungiko ku AIDS. Ndipo AIDS sindiyo ngozi yokha ya kuthiridwa mwazi. Kutalitali.
Ngozi Zimene Zimaposa AIDS
“Uwo ndi msanganizo wangozi kwenikweni umene timaugwiritsira ntchito m’mankhwala,” akunena tero ponena za mwazi Dr. Charles Huggins. Iye ayenera kudziŵadi; pakuti ndiye mtsogoleri wa ntchito ya kuthira mwazi pachipatala cha Massachusetts. Ambiri amaganizira kuti kuthiridwa mwazi nkopepuka mutapeza munthu wina wokhala ndi mwazi wa mtundu wofanana nawo. Koma pambali pa mtundu wa ABO ndi magwero a Rh amene mwazi umafanizidwira nawo mwadongosolo, pangakhale kusiyana kwina 400 kapena kuposapo kosafanana nawo. Monga mmene dokotala wa mtima ndi mitsempha yamwazi Denton Cooley akudziŵitsira motere: “Kuthiridwa mwazi ndiko kudzala chiwalo china mwa munthu wina. . . . Ndiganiza kuti pamakhala kusagwirizana kwina pafupifupi m’kuthiridwa mwazi konse.”
Nkosadabwitsa monga mmene dokotala wina ananenera, kuti kuthira chinthu chocholowanacholowana choterocho, kungathe “kusokoneza” dongosolo lotetezera matenda la thupi. Kwenikweni, kuthiridwa mwazi kumapondereza dongosolo lotetezera matenda kwautali wa chaka chimodzi. Kwa ena, iyi ndiyo mbali yowopsa kwenikweni ya kuthiridwa mwazi.
Kenaka palinso matenda oyambukira. Iwo ali ndi maina achilendo kwenikweni, monga ngati matenda a Chagas ndi a cytomegalovirus. Ziyambukiro zawo zadziŵika kuyambira pamalungo ndikunthunthumira mpaka imfa. Dr. Joseph Feldschuh wa ku Cornell University of Medicine akuti pali mpata 1 mwa 10 wa kuyambukiridwa ndi mtundu wakutiwakuti m’kuthiridwa mwazi. Kuli ngati kuseŵera ndifuwa lonyeka psyu ndimoto. Kufufuza kwaposachedwapa kwasonyezanso kuti kuthiridwa mwazi potumbula matenda akansa kungawonjezere kwenikweni ngozi ya kubwereranso kwa kansayo.
Nkosadabwitsa kuti programu ya wailesi yakanema ina inanena kuti kuthiridwa mwazi kungakhale chotsekereza kuchila chachikulu patakhala kutumbulidwa. Matenda otupa chiwindi amayambukira mazana zikwi zambiri ndipo amapha othiridwa mwazi ena ambiri kuposa mmene imachitira AIDS, koma samafalitsidwa. Palibe munthu amene amadziŵa kuchuluka kwa imfa zake, koma katswiri wa zachuma wotchedwa Ross Eckert akuti kungafanane ndi kugwa kwa ndege ya DC-10 yodzala ndi anthu mwezi uliwonse.
Ngozi ndi Nkhokwe Zosungira Mwazi
Kodi nkhokwe zosungira mwazi zikuvomereza motani kuvumbulidwa kwa ngozi zonsezi za zopangidwa zawo? Wosuliza wina akuti, iwo sakukondwera nako. Mu 1988 Lipoti Lantchito Yotumidwa ndi Prezidenti Kufufuza Mliri wa Kachilombo Kosaululidwa Msanga ndi Zotetezera Thupi Lamunthu inaika liwongo pa indasitaleyo la kukhala “ochedwa mosayenerera” kuchita ndi chiwopsezo cha AIDS. Ankhokwe zosungira mwazi anafulumizidwa kuletsa ziwalo zimene zili m’gulu lokhala pangozi kwenikweni kusasonkha mwazi wawo. Iwo analimbikitsidwa kuwupima mwazi weniweniwo, kuwupepeta kuti awone zizindikiro zakuti wachokera kwa osonkha okhala pangozi. Ankhokwe yosungira mwazi anachedwa. Iwo anazinyalanyaza ngozizo kukhala zosokoneza kwenikweni. Nchifukwa ninji?
M’buku lake lakuti And the Band Played On, Randy Shilts anafotokoza kuti osunga mwazi ena anakutsutsa kupima kowonjezereka “kwakukulukulu pamaziko a anthu wamba. Ngakhale kuti ikuyendetsedwa kwakukulukulu ndi magulu osapanga phindu monga ngati Red Cross, indasitale yamwazi njandalama zambiri, imalandira madola biliyoni imodzi [zikwi miliyoni imodzi] pachaka. Bizinesi yawo ya kupereka mwazi kwa othiridwa mwazi mamiliyoni 3.5 pachaka inawopsezedwa.”
Kuwonjezera apa, popeza kuti nkhokwe zosungira mwazi zosapanga phindu zimadalira kwakukulukulu pa osonkha mwaufulu, iwo anapewa kukwiitsa aliyense wa iwo mwa kupatula gulu lakutilakuti lomwe liri pangozi, makamaka ogonana a ziwalo zofanana. Opititsa patsogolo zoyenerera ogonana a ziwalo zofanana anachenjeza poyera kuti kuwaletsa kusonkha mwazi kukaswa kuyenera kwawo kwalamulo ndikuti kukawabweretsera mtundu wina wa chibalo cha mmaganizo.
Kutaikiridwa osonkha ndikuwonjezera mapimidwe atsopano kukawononganso ndalama zambiri. M’ngululu ya 1983, Nkhokwe Yosungira Mwazi ya ku Stanford University inakhala yoyamba kugwiritsira ntchito antchito opima mwazi, omwe akatsimikizira kaya mwaziwo unachokera kwa osonkha okhala pangozi yaikulu ya AIDS. Osunga mwazi ena anasuliza kachitidweko kukhala machenjera a zamalonda a kukopa odwala ambiri. Kupimako kumawonjezera mitengo. Koma monga mmene okwatirana ena, amene khanda lawo lidathiridwa mwazi popanda kuŵadziŵitsa anenera motere: “Ife motsimikizirika tikanalipirira painti yowonjezereka ya $5” kaamba ka kupimako. Khanda lawo linafa ndi AIDS.
Mfundo Yodziwonjola Mwini
Akatswiri ena amati ankhokwe zosungira mwazi amachedwa kuvomereza ngozi zokhala m’mwazi chifukwa chakuti safuna kupatsidwa liwongo la ziyambukiro za kulephera kwawoko. Mwachitsanzo, mogwirizana ndi lipoti la mu The Philadelphia Inquirer, FDA (U.S. Food and Drug Administration) ili ndi thayo la kutsimikizira kuti nkhokwe zosungira mwazi zikutsatira miyezo yabwino, komatu iyo imadalira kwakukulukulu pa nkhokwe zosungira mwazizi kuti zikhazikitse miyezoyo. Ndipo akuluakulu ena a FDA ndi omwe kale anali atsogoleri mu indasitale ya mwazi. Chotero, kufufuza nkhokwe zosungira mwazi mobwerezabwereza kunachepera pamene ngozi ya AIDS inavumbulidwa!
Nkhokwe zosungira mwazi za ku U.S. nazonso zafikira pa kulembetsa malamulo amene angazitetezere kuzengedwa mlandu. Pafupifupi m’boma lirilonse, tsopano lamulo limati mwazi ndiwo utumiki, osati chopangidwa. Uku nkutanthauza kuti munthu wozenga mlandu ankhokwe yosungira mwazi ayenera kupereka chitsimikizo chakuti ankhokwewo adali osasamalitsa—chotsekereza chalamulo cholimbadi. Malamulo oterowo angapangitse ankhokwe zosungira mwazi kukhala pachisungiko atazengedwa mlandu, komatu mwazi samaupanga kukhala wachisungiko kwa odwala.
Monga mmene katswiri wa zachuma Ross Eckert analingalira, ngati ankhokwe zamwazi akadapatsidwa liwongo la mwazi umene amagwira nawo ntchito, iwo akadachita zambiri kutsimikiza ubwino wake. Osunga mwazi amene analeka kugwira ntchito wotchedwa Aaron Kellner akuvomereza motere: “Mwa lamulo lapang’ono pazamankhwala, mwazi unakhala utumiki. Aliyense anakhala wodekha ndi iyi panyumba, kunena kuti aliyense tikutanthauza onse, kupatulapo mnkhole wopanda liwongo, wodwala.” Iye akuwonjezera motere: “Ife tikadasonyadi pa chisalungamo, koma sitinatero. Tinali odera nkhawa tsoka lathu lokha; kodi kudera kwathu nkhawa wodwala kunali kuti?”
Zotulukapo zikuwonekera kukhala zosapeweka. Indasitale ya nkhokwe zosungira mwazi njokondweretsedwa kwambiri kudzitetezera mwachuma kuposa mmene ikuchitira kutetezera anthu ku ngozi zochokera m’zomwe ikupanga. Ena angalingalire kuti, ‘koma kodi ngozi zonsezi ziridi kanthu ngati mwazi ndiwo mankhwala othekera okha opulumutsira moyo? Kodi mapindu samaposa ngozizo?’ Awa ndimafunso abwino ndithu. Kodi kuthiridwa mwazi konseko nkoyenerera motani?
[Mawu Otsindika patsamba 9]
Adokotala amachita zambiri kudzitetezera okha ku mwazi wa odwala. Koma kodi odwala ngotetezeredwa mokwanira kumwazi wothiridwawo?
[Bokosi/Zithunzi pamasamba 8, 9]
Kodi Mwazi Ngwachisungiko ku AIDS Lerolino?
“NDIMBIRI Yabwino Kumwazi,” unalengeza tero mutu wankhani mu Daily News ya ku New York pa October 5, 1989. Nkhaniyo inasimba kuti mpata wa kuyambukiridwa ndi AIDS m’kuthiridwa mwazi uli 1 mwa 28,000. Iyo inati, dongosolo la kutseka mpata wa kulowereredwa ndi kachiromboko m’mwazi woyenda tsopano lafikira pakukhutiritsa kokwanira 99.9 peresenti.
Ziyembekezo zofananazo zinakula mmaindasitale osungitsa mwazi. Iwo amati, ‘Nkhokwe yosungirako mwazi njachisungiko kuposa ndi kalelonse.’ Prezidenti wa American Association of Blood Banks anati ngozi ya kuyambukiridwa ndi AIDS m’mwazi “yathetsedweratu.” Koma ngati mwazi ngwachisungiko, kodi nchifukwa ninji onse aŵiri makoti ndi madokotala aumamatiza ndi mapepala olembedwapo kuti “ngwa paizoni” ndi “ngwopandiratu chisungiko”? Kodi nchifukwa ninji pogwira nawo ntchito madokotala ena amavala zovala zowoneka ngati mikanjo, nkhope ndi miyendo yawo itaphimbidwa ndi zovala, zonsezi kuchitira kuti asaugwire mwazi? Kodi nchifukwa ninji zipatala zambiri zimapemphera odwala awo kusaina fomu yochotsera ogwira ntchito m’chipatala liwongo la chivulazo cha kuyambukiridwa ndi ziyambukiro zoipa za kuthiridwa mwazi? Kodi mwazi ngwachisungikodi kumatenga onga ngati AIDS?
Chisungikocho chimadalira panjira ziŵiri zogwiritsiridwa ntchito kuchinjiriza mwazi: kupima osonkha mwaziwo ndikuwupepeta mwaziwo. Kufufuza kwaposachedwapa kwasonyeza kuti mosasamala kanthu za kuyesayesa konse kwa kupima osonkha mwaziwo amene njira yawo ya moyo imawaika pachiswe chachikulu cha kuyambukiridwa ndi AIDS, palidi ena amene amapyola nayo pakupimapo. Iwo amapereka mayankho abodza pa chipepala chamafunsocho nasonkha mwaziwo. Ena mochenjera amangofuna kutsimikizira ngati eniwo ngoyambukiridwa.
Mu 1985 akatswiri a nkhokwe zosungirako mwazi anayamba kupima mwazi kuti atsimikizire ngati mumapezeka zotetezera zimene thupi limatulutsa zokalimbana ndi kachilombo ka AIDS. Vuto la kupimaku nlakuti munthu angakhale atayambukiridwa nako kachirombo ka AIDS kwa nthaŵi yaitali pamene zotetezera thupizi zisanagalamutsidwe zimene kupimaku kumazifunafuna. Mpata wowopsawu umatchedwa nyengo ya kupulukira.
Lingaliro lakuti pali mpata 1 mwa 28,000 wa kuyambukiridwa ndi AIDS m’kuthiridwa mwazi limachokera mkufufuza kofalitsidwa mu The New England Journal of Medicine. Magazinewa anaika avereji ya kuthekera kwa nyengo ya kupulukirayi kukhala ya milungu isanu ndi itatu. Komabe, mu June 1989, miyezi yoŵerengeka izi zisanachitidwe, magazine amodzimodziwa anafalitsa kufufuza kofotokoza kuti nyengo ya kupulukirayi ingakhale yaitali kwambiri—zaka zitatu kapena kuposapo. Kufufuza koyambiriraku kunapereka malingaliro akuti nyengo za kupulukira zazitali zoterozo nzofala kwambiri kuposa mmene kunalingaliridwa kale, ndipo inafotokoza kuti, choipabe nchakuti, anthu ena oyambukiridwa sangatulutse konse zotetezera kachiromboka! Komabe, kufufuza kodzetsa chiyembekezo kwambiri sikunafotokoze zotumbidwazi, iyo inazitcha kukhala “zosazindikiridwa bwino.”
Nkosadabwitsa kuti Dr. Cory SerVass wa Ntchito Yotumidwa ndi Prezidenti Kufufuza AIDS (Presidential Commission on AIDS) anati: “Nkhokwe zosungira mwazi zingapitirizebe kufotokozera anthu kuti mwazi wosungidwawo ngwachisungiko kwenikweni, komatu anthuwo sakuwugulanso chifukwa chakuti akuzindikira kuti ichi sichowona.”
[Mawu a Chithunzi]
CDC, Atlanta, Ga.
[Bokosi patsamba 11]
Mwazi Wothiridwawo ndi Kansa
Asayansi akupeza kuti mwazi wothiridwa ungatsendereze dongosolo lochinjiriza matenda ndikuti dongosolo lochinjiriza matenda lotsenderezedwa moipa limayambukira mlingo wa kupulumuka kwa anthu amene amatumbulidwa chifukwa cha kansa. M’kope lake la February 15, 1987, magazini a Cancer akusimba za kufufuza mawu kochitidwa mu Netherlands. “Mwa odwala kansa ya m’matumbo,” magaziniwo anati, “chiyambukiro choipa cha kuthiridwa mwazi pa opola kwakanthaŵi chinawonekera. M’gulu limeneli munali chiwonjezeko chowirikiza cha zaka 5 kwa odwala opola 48% othiridwa mwazi ndi 74% kwa odwala osathiridwa mwazi.”
Asing’anga pa University ya ku Southern California anapezanso kuti kwa odwala amene anatumbulidwa chifukwa cha kansa ambirimbiri kansayo inabwereranso ngati adathiridwa mwazi. Annals of Otology, Rhinology & Laryngology, ya m’March 1989, inasimba kufufuza kochitidwa ndi asing’angawa pambuyo pa kutumbula odwala zana limodzi motere: “Chiŵerengero cha kubwereranso kwa kansa yonse ya pammero chinali 14% kwa omwe sanalandire mwazi ndi 65% kwa omwe anaulandira. M’kansa ya mkamwa, nkhwiko, ndi mphuno kapena m’mibowo ya mafupa a mphuno, chiŵerengero cha kubwereranso chinali 31% kwa osathiridwa mwazi ndi 71% kwa othiridwa mwazi.”
M’nkhani yake yakuti “Kuthiridwa Mwazi ndi Kutumbula kwa Kansa,” Dr. John S. Spratt anafotokoza motere: “Dokotala wotumbula kansa angafunikire kukhala dokotala wosakonda mwazi.”—The American Journal of Surgery, September 1986.
[Zithunzi patsamba 10]
Kunena kuti mwazi ndiwo mankhwala opulumutsa moyo nkovuta kumvetsetsa koma kuti umapha anthu nkosavuta