Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g90 12/8 tsamba 14-16
  • Kodi Ntchito Yapambuyo Poŵeruka Kusukulu Idzandithandiza Kukula?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ntchito Yapambuyo Poŵeruka Kusukulu Idzandithandiza Kukula?
  • Galamukani!—1990
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kugwira Ntchito—Mapinduwo
  • Kodi Munthu Amaphunziradi Zochuluka Motani?
  • “Kukhupuka Pamsinkhu Wochepa”
  • Kodi Ndiyenera Kupeza Ntchito Yogwira Pambuyo Poŵeruka Kusukulu?
    Galamukani!—1990
  • Kodi Ndiyenera Kugwira Ntchito Pamene Ndidakali Pasukulu?
    Galamukani!—1991
  • Ndingatani Kuti Ndizipeza Ndalama?
    Galamukani!—1998
  • Kodi Ndingakonzekere Motani Kukagwira Ntchito m’Dziko?
    Galamukani!—1992
Onani Zambiri
Galamukani!—1990
g90 12/8 tsamba 14-16

Achichepere Akufunsa Kuti . . .

Kodi Ntchito Yapambuyo Poŵeruka Kusukulu Idzandithandiza Kukula?

AŴIRI mwa atatu—ndimene achichepere tsopano akugwirira ntchito mu United States. Ndipo amathera maola 16 kufika ku 20 pamlungu akuchita motero!a

Kodi nchifukwa ninji achichepere m’ziŵerengero zazikulu akuthamangira ntchito? Brian wazaka 16 zakubadwa akufotokoza kuti: “Ponena za ine ndingoyenera kutero [kugwira ntchito]. Bambo ndi mayi ŵanga anasudzulana, ndipo ndiyenera kuthandiza amayi ŵanga mulimonse mmene ndingathere.” Mofananamo mabanja ambiri amafunikira thandizo landalama. Ndipo ngakhale pamene wachichepere sakuthandizira mwachindunji ku zowonongedwa zapanyumba, ngati angogula zovala zake kapena zinthu zina zaumwini, zimenezi zimapeputsirako makolo mavuto ena azandalama.

Zowonadi, achichepere ambiri amagwira ntchito kotero kuti adzigulire zovala zodula zimene amakhumbira, nsapato, kapena zakudya zamasinaki. Koma kwa achichepere ena, ntchito kwakukulukulu imatanthauza sitepe lalikulu kulinga ku uchikulire. Suzanne wazaka 19 zakubadwa analemba m’magazini a Seventeen kuti: “Ndimagwira ntchito chifukwa chakuti ndimasangalala kukhala wodzidalira. Sindimafunikira kudalira pa makolo anga kundiripirira zinthu. . . . Makolo angapatse ana awo ndalama, koma sangaŵapatse lingaliro lakukhutiritsidwa lochititsidwa ndikupata chinachake.” Ndipo mwinamwake nanunso mumalingalira mofananamo—kuti kukhala ndi ntchito kungakhale chokumana nacho chabwino, kuti kungakuthandizeni kukula mofulumira. Koma kodi kungaterodi?

Kugwira Ntchito—Mapinduwo

Baibulo limatsutsa ulesi. ‘Moyo wa waulesi ukhumba osalandira kanthu,’ ikutero Miyambo 13:4. “Koma moyo wa akhama udzalemera.” Chotero ngati mufunadi chinthu chinachake chogulidwa pamtengo woti makolo anu sangafune, kapena sangakhoze kuulipira, lingaliro lakugwira ntchito mwakhama kotero kuti mudzigulire nokha lingakhale labwino.

Ambiri amatsutsabe nati kugwira ntchito kungathandize kuphunzitsa wachichepere za moyo m’dziko lenileni. Ellen Greenberger ndi Laurence Steinberg achita kufufuza kwakukulu ndikofalitsidwa mwakuya pankhani ya kugwira ntchito kwa achichepere. Iwo anapeza kuti achichepere oterowo “amaphunzira za kuyendetsa malonda, kusamalira ndalama, ndi zamasamu azogula ndi zokugulitsa.” Ntchito ingaphunzitsenso wachichepere osati kuzoloŵera kugwira ntchito ndi achikulire kokha komanso zipsinjo zauchikulire ndi mathayo. Iye angaphunzire mmene angagwirire ntchito ndi kapitao wapantchito “wovuta kukondweretsa” kapena wamtima wapachala, kapena mmene angachitire mokoma mtima ndi makasitoma olunda—ndi antchito anzake. (1 Petro 2:18) “Ndinali mnyamata wochepa paonse pantchitopo,” akukumbukira motero Anthony, “ndipo aliyense ankandivutitsa. Koma ndinaphunzira kuchita ndi anthu.”

Kugwira ntchito kungaphunzitsenso wachichepere maluso ndi zizoloŵezi zantchito, zonga ngati kusunga nthaŵi, kumene kungakhale kothandiza pambuyo pake m’moyo. (Yerekezerani ndi Miyambo 22:29.) “Ndinaphunzira kukhala wathayo,” akutero mnyamata wachichepere wotchedwa Eric. “Kugwira ntchito ndi amalume kunandiphunzitsa kugwira ntchito mwaluso,” akuwonjezera motero Duane. “Iwo anagogomezera ukhondo, ndipo ngati sinachitike bwino, tinabwerezanso kuichita.” Olga, yemwe ankachita ntchito yaulembi pamene anali pasukulu anawonjezera kuti: “Ndinapeza kuzoloŵera kwa kugwira bwino ntchito. Ndipo kulankhula kwambiri patelefoni kunandiphunzitsa kugwiritsira ntchito mawu abwino.”

Kugwira ntchito kungakuphunzitseninso kunyadira zomwe mwakwaniritsa. Mfumu yanzeru Solomo inati: ‘Kodi sichabwino kuti munthu adye namwe, nawonetse moyo wake zabwino m’ntchito zake? Ichinso ndinachizindikira kuti chichokera ku dzanja la Mulungu.’—Mlaliki 2:24.

Kodi Munthu Amaphunziradi Zochuluka Motani?

Komabe, ambiri amakhulupirira kuti ntchito zamakono sizimawathandiza kwenikweni achichepere kukula. M’nthaŵi zakale, achichepere ogwira ntchito anaphunzira ntchito yooti akaigwire kapena maluso ena othandiza. Komabe, lerolino achichepere ambiri (makamaka mu United States) amagwira ntchito m’malesitalanti ogulitsa zakudya zamasinaki kapena m’maindasitale ena otumikira kumene ntchito zimakhala zonga kulongeza mabanzi m’mabokosi kapena kugwira ntchito pamakina ogulitsira zinthu. Ambiri amakaikira phindu lonka patali la ntchito yoteroyo. Greenberger ndi Steinberg anadandaula nati: “Wachichepere amangothera mphindi zochepera pa 10 peresenti ya nthaŵi yake pantchitoyo—pafupifupi mphindi zisanu za ola lirilonse—m’ntchito zonga ngati kuŵerenga, kulemba, ndikuchita masamu. . . . Ntchito zambiri nzatintchito ting’onoting’ono tosiyanasiyana, zochita zimodzimodzi nthaŵi zonse, ndi kubwerezabwereza kosasintha kwa ntchito zosakondweretsa kwenikweni.”

Nkhani ya mu The Wall Street Journal ikuti: ‘Achichepere ambiri ogwira ntchito lerolino sakuphunzira kanthu kalikonse kothandiza kwambiri kuposa kungodziwonetsera. Luso la zopangapanga lawasintha kukhala pafupifupi maroboti. Makina ocholoŵanacholoŵana amawonkhetsa okha ndalama ndikumawauza chenji ya ndalama. Pamalo ophikira masinaki, makina ophika okha achotseratu kuthekera kwakuti wachichepere angaphunzire maluso a kukonza zakudya m’kitchini.’ Ntchito zoterozo mosakaikira zimapereka mautumiki ofunikira ndi aphindu. Komabe, angachite zochepa kukonzekeretsa wachichepere kaamba ka ntchito za achikulire.

Koma bwanji ponena za chokumana nacho chakugwira ntchito ndi achikulire? Greenberger ndi Steinberg akuti: “Malo antchito kumene achichepere amalembedwa ntchito akhala opatulana misinkhu mowonjezereka. Mmalo mogwira ntchito pamodzi ndi akulu, . . . achichepere amakono amakonda kugwirira ntchito pamodzi ndi achichepere anzawo.” The Wall Street Journal imatcha malo antchito oterowo kukhala “mphala za anyamata.”

“Kukhupuka Pamsinkhu Wochepa”

Achichepere ambiri mu United States akupeza ndalama zoposa pa $200 pamwezi pantchito zawo. Kodi kugwira ndalama zimenezi sikuli chokumana nacho chopindulitsa? Taganizirani kufufuza kwa ophunzira pasukulu yasekondale ogwira ntchito a m’sukulu zosiyanasiyana zoposa chikwi chimodzi. Kunapezedwa kuti mbali zitatu mwazinayi za iwo sanathandize chirichonse ku zandalama za banja! Pafupifupi 60 peresenti ya iwo samaika kalikonse ku banki! Pokhala alibe mathayo akulipira lendi, inshuwalansi, ndi zakudya, ambiri a iwo anagwiritsira ntchito ndalama zawo monga zam’thumba—zowononga mmene angafunire.

Jerald G. Bachman wa pa The Institute for Social Research akunena kuti pamene “achichepere ali ndi ndalama zochuluka kwambiri,” iko ndiko “kukhupuka pamsinkhu wochepa,” kapena kukhala nacho chuma chochuluka. Chifukwa ninji choncho? Bachman akulongosola kuti: “Ophunzira ambiri apasukulu zasekondale ali ndi mabajeti a zinthu zosangulutsa zimene mwina sizidzawafikitsa ku zaka zisanu zirinkudza, pamene ndalama zawozo zidzafunikira kugula zinthu zofunikira zonga chakudya ndi lendi.” Inde, mmalo mophunzitsa wachichepere thayo losamalira ndalama, kukhala ndi ndalama zochuluka mopambanitsa kungaphunzitse chosiyanacho. Kungampangitse kulaŵa zosangulutsa zokhala loto chabe ndikupangitsa njira yoloŵera m’dziko lenileni lauchikulire kukhala yovutitsa kwabasi.

Baibulo limasonyezanso kuti kudzitopetsa kaamba kofuna chuma ndiko kulondola chopanda pake. Ilo limati: ‘Usadzitopetse kuti ulemere. . . . Kodi upenyeranji chimene kulibe? Pakuti chuma chimera mapiko, ngati mphungu youluka mumlengalenga.’—Miyambo 23:4, 5.

Kuti ntchito itsimikizire kukhala chokumana nacho chophunzitsa chopindulitsa zidzadalira pa mtundu wa ntchito yophatikizidwamoyo, mtundu wa anthu amene mumagwira nawo ntchito kapena amene mukuwagwirira ntchito, ndimmene mumadziperekera kuntchitoyo. Cholinga chanu chogwirira ntchito ndimmene mumasamalirira unyinji wa ndalama zimene mumapeza kudzasonyezanso mokulira kaya kugwira ntchito kumakuthandizani kapena kukuvulazani.

Koma ngati kukula ndikumene mulidi okondweretsedwa nako, onani zimene Greenberger ndi Steinberg anatsimikizira nazo: ‘Pali zochita zimene ziripo zomwe zingakhale zopindulitsa kuposa kugwira ntchito. Zochitazi zimaphatikizapo kuŵerenga ndi kuphunzira kunja kwa sukulu ndikutenga mathayo antchito zodzifunira zopanda malipiro kapena ntchito zam’mudzi.’ Mwachitsanzo, Nina, amachita ntchito yam’mudzi yaphindu koposa pambuyo poŵeruka kusukulu monga minisitala wanthaŵi zonse wa Mboni za Yehova. Iye akuti: “Ndinalinganiza ndi mlangizi wanga kukhala ndi tsiku limodzi lasukulu lokhala ndi maola ochepa kotero kuti ndidziŵeruka pasukulu dzuŵa lisanafike pamutu. Kuchokera pa Lolemba mpaka Lachitatu ndimapita m’ntchito yolalikira yapoyera. Ndimakonda kuichita. Ndimaikondadi!” Kodi ndandanda yanu ndi mikhalidwe yanu zikakulolani kuchita mofananamo? Kukulitsa “kudzipereka kwaumulungu” mwanjirayi mosakaikira kudzatsimikizira kukhala kopindulitsa kwambiri kuposa kugwira ntchito zina!—1 Timoteo 4:8, NW.

Koma achichepere ena angafune, kapena amayenera, kugwira ntchito kaamba ka zifukwa zandalama. Nkhani zamtsogolo zidzapenda maubwino ndi zoipa zakutero.

[Mawu a M’munsi]

a Chiŵerengero chomakula cha ophunzira omagwira ntchito chatchedwa “chochitika chapadera cha ku Amereka.” (When Teenagers Work, lolembedwa ndi Ellen Greenberger ndi Laurence Steinberg) Achichepere m’maiko ena akukhala ndi mavuto aakulu m’zamaphunziro, ndipo ntchito kaŵirikaŵiri zimasoŵa. Chikhalirechobe, nkhaniyi mosakaikira idzakhala yosangalatsa kwa achichepere ambiri m’maiko mmene mwaŵi wantchito umapezeka. Nkhani yamtsogolo idzachita ndi mkhalidwe wa m’maiko otukuka kumene.

[Chithunzi patsamba 15]

Ntchito ingaphunzitse wachichepere mmene angachitire ndi akulu antchito ndi antchito anzake mwanjira yauchikulire

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena