Achichepere Akufunsa Kuti . . .
Kodi Ndiyenera Kupeza Ntchito Yogwira Pambuyo Poŵeruka Kusukulu?
“Galamukani!”: Kodi chinakuchititsa kupeza ntchito yogwira pambuyo poweruka kusukulu nchiyani?
Eric: Ndinkakhala panyumba, ndipo ndinafuna kuthandiza makolo anga ndi ndalama.
Olga: Kudziimira pandekha. Ndinafuna kukhala ndi ndalama zangazanga.
Michelé: Ndidayamba kale kupatsidwa alawansi, koma ndinafuna kupeza kuzoloŵera ntchito.
Duane: Sindinagwirire ntchito kukundika ndalama. Ndinagwirira ntchito kuthandiza amalume wanga, omwe anali ndi malonda opaka utoto, osula miyala, ndi zina zotero.
Anthony: Ndinkagwira ntchito chifukwa chakuti ndinafuna kukhala wokhoza kugula zovala.
“Galamukani!”: Kodi amako sankakugulira zovala?
Anthony: Sankagula zovala za mtundu womwe ndinkaufuna.
KODI mukulingalira zopeza ntchito yogwira pambuyo poweruka kusukulu? Mwinamwake mungangofuna kukhala ndi ndalama zamthumba zapang’ono, ndipo kupeza ntchito kukuwoneka kukhala njira yofulumira yozipezera.
Ntchito ingakhale ndi maubwino ake.a Iyo ingamphunzitse wachichepere kukhala wathayo. Ingampatsenso kuzoloŵera kopindulitsa ndi maluso. Komabe, simbali zonse zantchito zimene ziri ndi maubwino, ndipo musanalowe ntchito, inuyo muyenera kupenda zowonongedwa mosamalitsa.—Yerekezerani ndi Luka 14:28; 1 Akorinto 10:23.
Kodi Ndidzachita Nazonji Ndalamazo?
Achichepere ambiri amagwirira ntchito kotero kuti athandize makolo awo ndi ndalama. Komabe, David L. Manning mphunzitsi wa sukulu ya sekondale akudziŵitsa kuti “cholinga choyambirira cha kugwirira ntchito yaganyu chimawonekera kukhala kudzisangalatsa kwa munthu mwini komwerekera.” Ndithudi, ndalama zambiri zimene achichepere amapeza zimawonongedwera, osati ku zotaika zabanja kapena kusungidwa, koma kuzinthu zosangulutsa, kuyambira pamawailesi a stereo ndi kugula matikiti olowera m’makonsati kufikira kugula nsapato zansalu zodula kwenikweni. M’kupita kwanthaŵi, ndalama zopezedwa kaŵirikaŵiri zimawonongedwa zonsezo.
“Kodi ndinachita nazonji ndalama zanga?” ndilo linali yankho la Michelé wachichepere pamene mtola nkhani wa Galamukani! anafunsa gulu la achichepere chimene anachita nazo ndalama zimene analandira pantchito zawo. “Sindikudziŵa,” ndimmene anavomerezera. “Sindinasungepo tiki ndiimodzi yomwe. Ndiganiza kuti ndinaziwononga m’kuyendayenda. Makanema—uku ndimapitako kumapeto a mlungu uliwonse. Ndi nsapato. Changa chomwe ndinagula ndinsapato. Ndinalipira ndalama zokwanira $250 kuzigula.” Olga wachichepere anayankha mofananamo naati: “Ndiganiza ndinawononga ndalama zanga zonse. Utapanga ndalama zambiri, umawononganso zambiri. Koma sindikukumbukira mpang’ono pomwe chomwe ndinachita nazo.”
Solomo anafunsa kuti, ‘Kodi ntchito zake zonse munthu asauka nazo zimpindulira chiyani?’ (Mlaliki 1:3) Ndipo popanda chifukwa chenicheni chogwirira ntchito, popanda makonzedwe enieni a mmene muzigwiritsira ntchito—kapena kuzisunga—ndalama zimene mupeza, ntchito yanu yamphamvuyo mofananamo ingakhale yosaphula kanthu, yachabechabe.b Inu mungafunse kuti, ‘Kodi choipapo nchiyani kuziwonongera pa zinthu zimene ndimakonda?’
Kugwirira ntchito zosowa zenizeni ndiko chinthu china. Koma kudzikhaulitsa mwamphamvu ndi ntchito kaamba ka zofuna zopanda pake ndiko msampha. Iko kungakupangireni chilakolako choipa cha chuma chakuthupi. (Yerekezerani ndi 1 Timoteo 6:8, 9.) Iko kungayambitse mzimu wodzigangira, wa ine poyamba womwe umasemphana ndi mzimu Wachikristu wa kupatsa. (Machitidwe 20:35) Chotero musanalowe ntchito, kodi sichikakhala bwino kuwona ngati palidi kusoŵa kwenikweni kwa kuchitira tero?
Sukulu ndi Ntchito
Chinthu china choyenera kuchilingalira ndicho chiyambukiro chimene kugwira ntchito kungabweretse pa kuphunzira kwanu. “Palibe munthu angathe kukhala kapolo wa Ambuye awiri,” anatero Yesu. (Mateyu 6:24) Lamulo lamakhalidwe abwino ili limagwira ntchito kwa ophunzira ambiri omwe amadzipeza opanikizidwa pakati pa sukulu ndi ntchito.
Kufufuza kwasonyeza kuti kumakhala kwachidziŵikire kwenikweni kwa achichepere omwe amagwira ntchito kulova kusukulu kuposa osagwira ntchito. Ndipo iwo atapezekako, kaŵirikaŵiri samatchera khutu. “Ndinkaweruka kusukulu masana ndipo ndinkagwira ntchito yaukalaliki kuchokera pa wanu koloko kufikira pafaifi,” akulongosola tero Olga wachichepere. Kodi chotulukapo chinali chiyani? “Ndinkatopa zedi. Sukulu ndi ntchito zimatopetsadi.” Pamenepo, nkosadabwitsa kuti magiredi a ophunzira ambiri amatsika atayamba kugwira ntchito. Ena amalepheradi mayeso.
“Ndidafunikira kupezeka kusukulu yochitidwa m’nthaŵi yatchuthi chamasukulu,” ndimmene akukumbukirira Anthony, yemwe analephera pamene ankagwira ntchito pantchito ya pafakitale pambuyo poweruka kusukulu. Komabe, Anthony anapitirizabe kugwira ntchito m’nyengo yatchuthi. Kodi chotulukapo chinali chiyani? “Ndinalepheranso mayeso kusukulu yochitidwa m’nthaŵi yatchutiyi ndipo ndinafunikira kubwereza kalasilo.” Zowona, ophunzira aluntha ena amakhala okhoza kusungabe magiredi awo abwino. Michelé akukumbukira motere: “Ndidangotchera khutu kwa mphunzitsi wanga, kumvetsetsa chimene ankanena, ndikupambana mayeso. Sindinaŵerengepo.” Komabe, pali kusiyana kwakukulukulu pakati pa kungotchera khutu m’sukulu ndikumwerekeramo kwenikweni m’kuphunzira.—Yerekezerani ndi 1 Timoteo 4:15.
Chotero ngati mukulingalira za ntchito, dzifunseni kuti: ‘Kodi homuweki yanga ndidzailabadira bwino? Kodi ndidzakhoza kupuma bwino ndikugona?’ (Mlaliki 4:6) Zambiri zidzadalira pamtundu wantchitoyo ndi ndandanda yake. Koma ngati ntchito idodometsa kuphunzira kwanu, kodi njabwinodi?
Ntchito ndi Banja Lanu
Chodetsanso nkhaŵa ndicho chiyambukiro chimene kugwira ntchito kungakhale nacho paunansi wanu ndi ziŵalo zabanja. “Kufufuza kwathu kwasonyeza . . . kuti achichepere omwe amagwira ntchito amathadi kuwononga nthaŵi yochepa pantchito zabanja kuposa achichepere osagwira ntchito,” atero ofufuza Laurence Steinberg ndi Ellen Greenberger. Mwachitsanzo, “achichepere ambiri ogwira ntchito amasimba kuti samadya kaŵirikaŵiri chakudya chamadzulo ndi banja lawo (chotero amaphonya imodzi ya nthaŵi zochepa patsiku pamene makolo ndi ana ‘amagwirizana’ m’machitachitawo).”
Nthaŵi zakudya zinali mbali zofunika kwambiri za moyo wabanja m’nthaŵi za Baibulo ndipo zimapitirizabe kukhala tero kwa anthu a Mulungu lerolino. (Yerekezerani ndi Miyambo 15:17.) Kwa Mboni za Yehova, mabanja ambiri amagwiritsira ntchito chakudya cham’mawa kapena chamadzulo kukambirana nkhani zauzimu. Kodi ntchito yogwira pambuyo poweruka kusukulu imakuletsani kukhalamo ndi phande?
Achichepere ogwira ntchito angayambenso kudzimva odziimira pawokha kwa makolo awo. Ena amalingaliradi kuti popeza kuti ali ndi ndalama zawo, iwo sayenera kugonjera kuulamuliro wa makolo awo. Komabe, malipiro omwe mumalandira samakuwonjolani kuthayo lanu la m’Malemba la ‘kumvera mwambo wa atate’ kapena kulabadira ‘chilangizo cha amako.’ (Miyambo 1:8) Machitsanzo, makolo anu ali ndi kuyenerera kulikonse kwa kutsimikizira unyinji wa ndalama zanu zomwe mwalandira umene uyenera kuthandizira zowonongedwa za banja. Ndiiko nkomwe, pafupifupi ndalama zawo zonse zimatero.
Ngati musankhapo kugwira ntchito, bwanji osasonyeza uchikulire ndi chikondwerero chanu muubwino wabanja mwa kupempha makolo anu kuti akuuzeni unyinji wa ndalama zimene mungathandizire ku ndalama zabanja?
Ntchito Yanu ndi Uzimu Wanu
Kulingalira kofunika kwenikweni kuposa zonse ndiko chiyambukiro chimene kugwira ntchito kungakhale nako pauzimu wanu. Steinberg ndi Greenberger akusimba kuti kudziunikira ku malo antchito kaŵirikaŵiri kwatulukapo ‘mkhalidwe wopanduka,’ monga ngati kuba pantchito kapena kunama m’sukulu. Achichepere ena amagonjeradi ku kutsendereza kwa ausinkhu wofanana nachotsera ndalama—kapena kubera—mabwenzi. Kutsendereza kwa ntchito (ndikukhala ndi ndalama m’manja) kumasonkhezera achichepere ambiri kumwa zoledzeretsa ndi kugwiritsira molakwa mankhwala.
Zowona, mutakhala ndi malamulo amakhalidwe abwino Achikristu, simungaganizirepo kuchita zinthu zoterozo. Komabe, kulowa ntchito kungautsire wachichepere ku “mayanjano oipa” kwambiri. (1 Akorinto 15:33) Kodi ndinu wokonzekera kusamalira kutsendereza koteroko? Pamene muli kusukulu, kodi ‘mwachita mwanzeru ndi akunja’ mwa kupewa kuyanjana koipa? (Akolose 4:5) Ngati mwasonyeza zifooko m’nkhaniyi, kodi mulidi wokonzekera kuyang’anizana ndi zitsenderezo zazikulu pamalo antchito?
Ndandanda yotopetsa yantchito ingachipangitsenso kukhala chovuta kwa inu kutsatira njira Zachikristu za misonkhano, phunziro laumwini la Baibulo, ndi kukhalamo ndi phande muuminisitala Wachikristu. “Ndinaphonyapo misonkhano chifukwa chakuti ndinali wotopa pambuyo pasukulu ndi ntchito,” watero Michelé.
Chosankha cha kupeza ntchito ya pambuyo poweruka kusukulu nchofunikira kusamala kwenikweni. Kulingalira kosamalitsa kuyenera kuperekedwa ku zochititsa zonse. Zifotokozeni nkhanizo ndi makolo anu kapena Mkristu wachikulire. Ngati ntchito yalingaliridwa kukhala yofunikira, yesani zolimba kukhala wachikatikati. Pangani ndandanda imene ingakuloleni kupereka chisamaliro chokwanira ku maphunziro ndi kukula kwanu kwauzimu. Ngati ichi nchosatheka, lingalirani njira zina zopezera ndalama. Mwinamwake pali ntchito zazikulu zapabanja zimene makolo anu ali ofunitsitsa kukulipirani kuti muzichite. Achichepere ena amayamba malonda aang’ono, monga ngati kutchetcha udzu kapena kulera ana, zimene zimawalola kupeza ndalama panthaŵi yawo yabwino.
Koma bwanji ponena za achichepere m’maiko osauka kwambiri omwe alibe chomwe angasankhe koma kungogwira ntchito? Nkhani yamtsogolo idzafotokoza mkhalidwe wawo.
[Mawu a M’munsi]
a Onani nkhani yakuti “Kodi Ntchito Yapambuyo Poweruka Kusukulu Idzandithandiza Kukula?” m’kope lathu lino.
b Onani makope a Galamukani a January 8, 1989, ndi February 8, 1989 kaamba ka malingaliro onena za kusamalira ndalama.
[Mawu Otsindika patsamba 19]
“Cholinga choyambirira cha ntchito yaganyu chimawonekera kukhala kumwerekera m’kudzisangalatsa”
[Chithunzi patsamba 18]
Kodi mukugwirira ntchito kulipirira zotaika zenizeni kapena kukhutiritsa chikondi cha zinthu zakuthupi?