Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g90 12/8 tsamba 8-10
  • Ubale Wapadziko Lonse Ngwotsimikizirika!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ubale Wapadziko Lonse Ngwotsimikizirika!
  • Galamukani!—1990
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mboni za Yehova Nzosiyana
  • Mmene Umodzi Umafikiridwira
  • Maulosi Abaibulo Akukwaniritsidwa
  • Pamene Mafuko Onse Adzakhala Pamodzi Pamtendere
    Galamukani!—1993
  • Maziko a Dziko Latsopano Akuyalidwa Tsopano Lino
    Kodi Mulungu Amatisamaliradi?
  • Kusankhana Mitundu
    Galamukani!—2014
  • Kupeza Chigwirizano Chaufuko mu South Africa Yovutitsidwa
    Nsanja ya Olonda—1989
Onani Zambiri
Galamukani!—1990
g90 12/8 tsamba 8-10

Ubale Wapadziko Lonse Ngwotsimikizirika!

M’MISHONALE anali asanakhalitse Kumadzulo kwa Afirika pamene anakapezeka pamsonkhano wachipembedzo kudera lakumidzi. Pamene anafikira banja la kumaloko, mnyamata wa zaka ziŵiri anayamba kulira, osadziŵa chifukwa chake.

M’mishonaleyu anayesa kutonthoza mwanayu, koma kulira kwa mnyamatayu kunasanduka kufuula. “Kodi chalakwika nchiyani?” m’mishonaleyo anawafunsa tero amake. Iwo anayankha mochititsidwa manyazi naati: “Ndiganiza ndinuyo. Akuwopa mtundu wa khungu lanu. Sanawonepo mzungu ndi kalelonse.”

Kusiyana kwakuthupi kwa anthu timakudziŵa kuchokera paubwana. Kunyada kumadzakulitsidwa pambuyo pake. Malingaliro a ana amasinthidwa pamene awona mmene anthu achikulire akuchitira ndi kukhalira, monga ngati makolo awo. Kusukulu amasonkhezeredwanso ndi aphunzitsi, mabwenzi, ndi anzawo amkalasi.

Mogwirizana ndi kufufuza kwanthaŵi yaitali mu United States, panthaŵi imene ana amafika zaka 12 zakubadwa, iwo amakhala atakulitsa kale malingaliro ndi mikhalidwe yoipayi ponena za magulu amwambo, aufuko, ndi achipembedzo owazinga. Pamene akula malingalirowa amakhala atakhazikika mwakuya.

Mboni za Yehova Nzosiyana

M’dziko mmene kunyada kukuchuluka, Mboni za Yehova zimakhala zosiyana kwambiri. Iwo amadziŵika m’mitundu yonse chifukwa cha kugwirizana kwawo mwaufuko. Uku kumaonedwa kaŵirikaŵiri ndi openyerera misonkhano yawo ya chaka ndi chaka.

Mwachitsanzo, nyuzipepala yakuti States-Item inasimba izi ponena za msonkhano waukulu wa Mboni wochitikira kum’mwera kwa United States: “Kulingalira kwaubale kunadzaza Louisiana Superdome pamene Mboni za Yehova zachichepere ndi zachikulire, zakuda ndi zoyera zinakhazikika kuyamba . . . kuphunzira ndi kukhalamo ndi phande m’zokumana nazo. . . . Kupatulana mafuko . . . sikuli vuto kwa mboni.”

Pamsonkhano wa Mboni, mu South Africa, mkazi wachinenero cha Xhosa anati: “Nkozizwitsa kuti m’South Africa muno anthu a mafuko onse angakhale ogwirizana motero. Nchosiyana kwambiri ndi chimene ndazoloŵerana nacho m’matchalitchi.”

Pamene alendo ochokera Kumpoto ndi Kum’mwera kwa Amereka limodzinso ndi Ulaya anapezeka pamisonkhano yaikulu ya Mboni mu Far East ndi ku South Pacific, mogwirizana ndi lipoti lina, “panalibe kudziŵa nkudziŵa komwe kuti kodi uyu ngwafuko liti kwa iwo, kapena kwa oŵalandirawo.”

Chotero, chomwe chiri chosiyana kwambiri kwa Mboni za Yehova mamiliyoni ambiri padziko lonse lapansi ndicho umodzi wawo weniweni ndi kugwirizana kwamafuko. Iwo ngogwirizanitsidwa pamodzi ndi chikondi chenicheni Chachikristu. Mongadi mmene Yesu ananenera kuti: ‘Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.’—Yohane 13:35.

Chotero Mboni za Yehova ziri kale ndi ubale weniweni, wokhalirira wa mitundu yonse! Izo zimakumbukira cimene Yesu ananena pa Mateyu 23:8 kuti: “Inu nonse muli abale.” Ndipo ichi chikuchitika panthaŵi imene mipatuko yamafuko ndi miyambo ndi chidani zikupikisanitsa mitundu.—Onaninso 1 Akorinto 1:10; 1 Yohane 3:10-12; 4:20, 21; 5:2, 3.

Mmene Umodzi Umafikiridwira

Chachikulu paumodzi umenewu ndicho malangizo ozikidwa pa Baibulo amene Mboni za Yehova zimaŵalandira pa Nyumba zawo Zaufumu ndi kuphunzira kwawo kwaumwini kwa Baibulo. Iwo ngofanana ndi Akristu a ku Tesalonika, za amene mtumwi Paulo anati: ‘Pakulandira mawu a uthenga wa Mulungu, simunawalandira monga mawu a anthu, komatu monga momwe ali ndithu, mawu a Mulungu, amenenso achita mwa inu okhulupirira.’—1 Atesalonika 2:13.

Chotero, Mboni zimakhulupirira zimene Baibulo limanena, ndipo zimayesetsa mowona mtima kutsanzira njira za Mulungu za kuganizira zinthu. Izo zimakumbukira chimene mtumwi Wachikristu Petro ananena mouziridwa kuti: ‘Zowona ndizindikira kuti Mulungu alibe tsankhu; koma m’mitundu yonse, wakumuopa iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.’—Machitidwe 10:34, 35.

Mogwirizana ndi ichi, Yesu analangiza atsatiri ake kupanga ophunzira mwa anthu “a mitundu yonse.” (Mateyu 28:19) Mofananamo, Mboni za Yehova mokangalika zimafunafuna okonda chilungamo m’magulu onse amafuko ndi miyambo, popanda kusankha. Ndipo pamene anthu a ziyambi zosiyanawo ndi mafuko agwirizana m’kulambira, kugwira ntchito, ndipo ayanjanira pamodzi, kulingalira koipa kuja kumalakidwa. Iwo amaphunzira kumulingalira munthu wina kukhala wofunika, ndikukondana.

Zowona, munthu amene wakhala akupatula fuko kwanthaŵi yaitali sangasinthe malingaliro ake panthaŵi yomweyo. Koma atakhala Mboni, iye amayamba “kuvala umunthu watsopano” wa Mkristu weniweni, ndipo amagwira ntchito zolimba kulaka malingaliro ake a poyambapo. (Aefeso 4:22-24, NW) Iye samayesa kulungamitsa kunyada kwake mwakuti, ‘Umu ndimo mmene ndinaleredwera.’ Ayi, iye amakalamira kusintha malingaliro ake ndi ‘kukonda abale.’—1 Petro 2:17.

Maulosi Abaibulo Akukwaniritsidwa

Chomwe chikuchitikira Mboni za Yehova lerolino nchapadera kwenikweni. Ndithudi, chinaloseredwa m’Baibulo.

Onani chimene Yesaya 2:2-4 (NW) ananeneratu kuti chikachitika “m’masiku a kumapeto,” ‘m’masiku otsiriza’ ano a dongosolo loipa ili la zinthu. (2 Timoteo 3:1-5, 13) Ulosi wa Yesaya umenewo unadziŵitsa kuti kulambira kowona kwa Yehova kukakhazikitsidwa mumbadwo uno, ndikuti ‘mitundu yonse idzasonkhana kumeneko. Ndipo anthu ambiri adzanka, nati, Tiyeni tikwere kunka ku phiri la Yehova, ndipo iye adzatiphunzitsa za njira zake, ndipo tidzayenda m’mayendedwe ake.’

Ulosi wa Yesaya unadziŵitsanso chotulukapo chachilendo ichi, chimene chawonedwa m’mitundu yonse pakati pa Mboni za Yehova m’zaka za zana lonse lino: “Ndipo iwo adzasula malupanga ao akhale zolimira, ndi nthungo zao zikhale anangwape; mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo.”

Ndiponso, bukhu la Baibulo la Chibvumbulutso, ponena za nthaŵi yathu, linaneneratu kuti khamu la anthu ambiri ‘ochokera mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe’ akasonkhana pamodzi muubale weniweni kutumikira Mulungu mogwirizana.—Chibvumbulutso 7:9, 15.

Awa simalingaliro ongoyerekeza. Khamu lalikulu lochokera m’mitundu yonse, m’magulu a mafuko ndi miyambo, layamba kale kupangidwa. Ubale weniweni wokhalirira ukuchitidwa tsopano lino! Uwo ndimaziko a chitaganya chatsopano kotheratu, cha anthu achimwemwe ogwirizana pachiunda chonse, chomwe chidzalowa mmalo chitaganya chamakonochi choipa chomwe chidzawonongedwa posachedwapa ndi Mulungu. Monga mmene Yesu ananenera, chitaganya chogwirizanachi, ‘chidzalandira dziko lapansi,’ ndikukhalabe ndi moyo pa ilo kosatha pansi pa kulamulira kwa Ufumu wa Mulungu.—Mateyu 5:5; 6:9, 10; Salmo 37:10, 11, 28, 29, 37, 38.

Kodi bwanji osadziwonera nokha? Inu mukuitanidwa kukacheza ku Nyumba Yaufumu iriyonse ya Mboni za Yehova ndikuwona kugwirizana kwawo kwamafuko. Kapena nthaŵi yotsatira imene Mboni zidzakufikirani, aitanireni m’nyumba ndikuwapempha kukusonyezani kuchokera m’Baibulo chimene chiri maziko a kugwirizana kwawo kwamafuko. Aloleni akusonyezeni chiyembekezo chawo cha m’Baibulo cha dziko latsopano kumene ubale weniweni udzakhalako padziko lonse lapansi.

Mulungu Wamphamvuyonse, Yehova, akupereka chitsimikizo chake kuti chifuniro chake cha kukhazikitsa ubale wa anthu onse chidzakwaniritsidwa. Iye akuti: ‘Momwemo adzakhala mawu anga amene atuluka m’kamwa mwanga, sadzabwerera kwa ine chabe, koma adzachita chimene ndifuna, ndipo adzakula mmene ndinawatumizira.’—Yesaya 55:11.

Tikukuitanani kusanthula umboni wochokera m’maulosi a Baibulo ndikuchokera m’kukwaniritsidwa kwa maulosi amenewo. Mutatero, mudzawona kuti kugwirizana kwamafuko nkosathekera chabe koma nkosapewekadi!

[Mawu Otsindika patsamba 9]

Zomwe zikuchitika pakati pa Mboni za Yehova lerolino zinaloseredwa m’Baibulo

[Chithunzi patsamba 10]

Mboni za Yehova nzapadera m’kukhala ndikugwirizana kwenikweni kwamafuko pakati pawo

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena