Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • dg gawo 11 tsamba 28-32
  • Maziko a Dziko Latsopano Akuyalidwa Tsopano Lino

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Maziko a Dziko Latsopano Akuyalidwa Tsopano Lino
  • Kodi Mulungu Amatisamaliradi?
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Ubale Wowona wa Mitundu Yonse
  • Kudziŵikitsa Anthu a Mulungu
  • Mbali Ina Yodziŵikitsa
  • Kuyankha ku Nkhani Yachiŵiri
  • Kodi Chosankha Chanu N’chiyani?
  • Ubale Wapadziko Lonse Ngwotsimikizirika!
    Galamukani!—1990
  • Mboni za Yehova
    Kukambitsirana za m’Malemba
  • Chifuno cha Mulungu Chidzakwaniritsidwa Posachedwapa
    Kodi Moyo Uli ndi Chifuno?
  • Jehova Mulungu wa Chifuno
    Nsanja ya Olonda—1994
Onani Zambiri
Kodi Mulungu Amatisamaliradi?
dg gawo 11 tsamba 28-32

Chigawo 11

Maziko a Dziko Latsopano Akuyalidwa Tsopano Lino

1, 2. M’kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Baibulo, kodi chikuchitika n’chiyani maso athu ali chipenyere?

CHIMENENSO chili chokondweretsa chili chenicheni chakuti maziko adziko latsopano la Mulungu akuyalidwa tsopano lino, pamene dziko lakale la Satana likunyonyotsoka. Tikuziwona ndi maso athu enieniwa, Mulungu akusonkhanitsa anthu kuchokera kumitundu yonse kuwapanga kukhala maziko a chimangidwe cha dziko lapansi latsopano chimene mwamsanga chidzaloŵa mmalo mwa dziko logaŵanika lamakonoli. M’Baibulo, pa 2 Petro 3:13, chimangidwe chatsopano chimenechi chikutchedwa “dziko lapansi latsopano.”

2 Ulosi wa Baibulo umatinso: “Padzakhala masiku otsiriza [nthaŵi imene tikukhalamo ndi moyo tsopano] . . . , anthu ambiri adzamka, nati, tiyeni tikwere kumka kuphiri la Yehova [kulambira kwake kowona], . . . ndipo iye adzatiphunzitsa za njira zake, ndipo tidzayenda m’mayendedwe ake.”—Yesaya 2:2-3.

3. (a) Kodi ulosi wa Yesaya ukukwaniritsidwa pakati pa ayani? (b) Kodi buku lomalizira la Baibulo limanenapo mawu motani?

3 Ulosi umenewu tsopano ukukwaniritsidwa pakati pa awo amene akugonjera ‘njira za Yehova ndi kuyenda m’mabande ake.’ Buku lomalizira la Baibulo limalankhula za chimangidwe chimenechi cha anthu a mitundu yonse okonda mtendere kukhala ‘khamu lalikulu . . . ochokera mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe,’ ubale weniweni wa padziko lonse wa otumikira Mulungu mogwirizana. Ndipo Baibulo limanenanso kuti: “Iwo ndiwo akutuluka m’chisautso chachikulu.” Ndiko kuti, iwo adzapulumuka mapeto a dongosolo loipa lino la zinthu.—Chivumbulutso 7:9, 14; Mateyu 24:3.

Ubale Wowona wa Mitundu Yonse

4, 5. Kodi n’chifukwa ninji ubale wapadziko lonse wa Mboni za Yehova uli wothekera?

4 Mboni za Yehova mamiliyoni angapo zimayesa kukhala ndi moyo mogwirizana ndi malamulo a Mulungu ndi njira zake. Chiyembekezo chawo cha moyo wosatha chamangika padziko latsopano la Mulungu. Mwakudzisungira miyoyo yawo tsiku ndi tsiku momvera malamulo a Mulungu, iwo amasonyeza kufunitsitsa kwawo kugonjera kunjira zake za kulamulira ponse paŵiri tsopano ndi m’dziko latsopano. Kulikonse, mosasamala kanthu za mtundu wawo, kapena fuko, iwo amamvera miyezo yofananayo monga momwe yalembedwera ndi Mulungu m’Mawu ake. Ndicho chifukwa chake iwo ali ndi ubale wowona wa m’mitundu yonse, chimangidwe cha dziko latsopano la Mulungu.—Yesaya 54:13; Mateyu 22:37, 38; Yohane 15:9, 14.

5 Mboni za Yehova sizimadzipatsa thamo kaamba ka kukhala kwawo ndi ubale wapadera wa padziko lonse. Iwo amadziŵa kuti izi zachititsidwa ndi mzimu wa mphamvu wa Mulungu wogwira ntchito pa anthu amene amagonjera kumalamulo ake. (Machitidwe 5:29, 32; Agalatiya 5:22, 23) Uli wopangidwa ndi Mulungu. Monga momwe Yesu ananenera, “zinthu zosatheka kwa anthu n’zotheka ndi Mulungu.” (Luka 18:27) Chotero Mulungu amene anatheketsa chilengedwe chonse cha chikhalirecho ndiye amenenso akutheketsa chimangidwe cha dziko latsopano chachikhalirecho.

6. Kodi n’chifukwa ninji ubale wa Mboni za Yehova ungatchedwe chozizwitsa cha makono?

6 Chotero, njira ya Yehova ya kulamulira m’dziko latsopano ingathe kuwonedwa kale m’zimene akutulutsa m’maziko adziko latsopano amene tsopano akuyalidwa. Ndipo zimene iye wachita ndi Mboni zake, m’lingaliro lochepa, ndizo chozizwitsa. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti iye wasonkhanitsa Mboni za Yehova kukhala ubale weniweni wapadziko lonse lapansi, umene sungaswedwe ndi zikondwerero zogaŵanitsa zautundu, zaufuko, kapena zachipembedzo. Pamene kuli kwakuti Mboni zili m’chiŵerengelo chokwanira mamiliyoni ndipo zikukhala m’maiko oposa 200, izo n’zomangidwa pamodzi monga ngati m’chomangira chosasweka chimodzi. Ubale wapadziko lonse, wapadera m’mbiri yonse ya anthu umenewu, ulidi chozizwitsa chamakono—chopangidwa ndi Mulungu.—Yesaya 43:10, 11, 21; Machitidwe 10:34, 35; Agalatiya 3:28.

Kudziŵikitsa Anthu a Mulungu

7. Kodi Yesu ananena kuti otsatira ake owona akadziŵika motani?

7 Kodi kungatsimikiziridwenso motani amene ali anthu amene Mulungu akuwagwiritsira ntchito monga maziko a dziko lake latsopano limeneli? Eya, kodi ndani amene amakwaniritsa mawu a Yesu pa Yohane 13:34, 35? Iye anati: “Ndikupatsani inu lamulo latsopano, kuti mukondane wina ndi mnzake; monga ndakonda inu, kuti inunso mukondane wina ndi mnzake. Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.” Mboni za Yehova zimakhulupirira mawu a Yesu ndipo zimawalabadira. Monga momwe mawu a Mulungu amalangizira, iwo ‘ali nacho chikondano chenicheni mwa iwo okha.” (1 Petro 4:8) Iwo ‘amadziveka [iwo eni] ndi chikondi, popeza kuti ndicho chomangira changwiro chachigwirizano.’ (Akolose 3:14) Chotero chikondi cha ubale ndicho “guluwu” imene imawamatiriza pamodzi padziko lonse lapansi.

8. Kodi ndi motani mmene 1 Yohane 3:10-12 amadziŵikitsira mowonjezereka anthu a Mulungu?

8 Ndiponso, 1 Yohane 3:10-12 amati: “Mmenemo awoneka ana a Mulungu, ndi ana a Mdyerekezi: yense wosachita chilungamo sali wochokera kwa Mulungu; ndi iye wosakonda mbale wake. Pakuti uwu ndi uthenga mudawumva kuyambira pachiyambi, kuti tikondane wina ndi mnzake: osati monga Kaini anali wochokera kwa woipayo, namupha mbale wake.” Chotero, anthu a Mulungu ali ndi ubale wopanda chiŵawa, wapadziko lonse.

Mbali Ina Yodziŵikitsa

9, 10. (a) Kodi atumiki a Mulungu akadziŵika ndi ntchito yotani m’masiku otsiriza? (b) Kodi ndi motani mmene Mboni za Yehova zakwaniritsira Mateyu 24:14?

9 Pali njira yina yodziŵira atumiki a Mulungu. Muulosi wake wonena za mapeto adziko, Yesu anasimba zinthu zambiri zimene zikasonyeza nyengo ino kukhala masiku otsiriza. (Wonani chigawo 9.) Mbali yaikulu ya ulosi umenewu ikutchulidwa m’mawu ake pa Mateyu 24:14 (NW): “Ndipo mbiri yabwino imeneyi ya ufumu idzalalikidwa m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni kumitundu yonse; ndipo pomwepo mapeto adzafika.”

10 Kodi tawona ulosi umenewu ukukwaniritsidwa? Inde, chifukwa chakuti chiyambire masiku otsirizawo mu 1914 Mboni za Yehova zalalikira mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu padziko lonse lapansi mwanjira imene Yesu analamula, ndiko kuti, kunyumba za anthu. (Mateyu 10:7, 12; Machitidwe 20:20) Mboni mamiliyoni angapo zikufika kwa anthu mumtundu uliwonse kukalankhula nawo za dziko latsopano. Izi zachititsa kuti inu mulandire brosha lino, popeza kuti ntchito ya Mboni za Yehova imaphatikizapo kusindikiza ndi kugaŵira mabuku mabiliyoni ambiri ofotokoza Ufumu wa Mulungu. Kodi inu mumadziŵa munthu wina aliyense amene amalalikira za Ufumu wa Mulungu kunyumba ndi nyumba padziko lonse lapansi? Ndipo Marko 13:10 amasonyeza kuti ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa imeneyi iyenera “choyamba,” kuchitidwa mapetowo asanadze.

Kuyankha ku Nkhani Yachiŵiri

11. Kodi n’chiyaninso chimene Mboni za Yehova zimakwaniritsa mwa kugonjera ku ulamuliro wa Mulungu?

11 Mwakugonjera kumalamulo a Mulungu ndi malamulo a makhalidwe abwino, Mboni za Yehova zimachitanso kanthu kena: Zimasonyeza kuti Satana anali wabodza pamene ananena kuti anthu sakakhoza kukhala okhulupirika kwa Mulungu poyesedwa motero kuyankha kunkhani yaikulu yachiŵiriyo, imene imakhudza umphumphu wa munthu. (Yobu 2:1-5) Popeza iwo ali chimangidwe cha anthu mamiliyoni ochokera kumitundu yonse, Mboni za Yehova zimasonyeza, monga bungwe limodzi, kukhulupirika kuulamuliro wa Mulungu. Ngakhale iwowa ali anthu opanda ungwiro, iwo amachirikiza mbali ya Mulungu ya nkhani ya ulamuliro wachilengedwe chonse mosasamala kanthu za chitsenderezo cha Satana.

12. Mwachikhulupiriro chawo, kodi Mbonizo zimatsanzira yani?

12 Lerolino, Mboni za Yehova mamiliyoni angapo zimenezi zimawonjezera umboni wawo ku uja wamzera wautali wamboni zina m’nthaŵi zakale zimene zinasonyeza kukhulupirika kwa Yehova Mulungu. Zina za zimenezi zinali Abele, Nowa, Yobu, Abrahamu, Sara, Isake, Yakobo, Debora, Rute, Davide, ndi Danieli, kungotchulapo oŵerengeka chabe. (Ahebri, chaputala 11) Izo zili, monga momwe Baibulo limanenera, ‘khamu lalikulu la mboni zokhulupirika.’ (Ahebri 12:1) Amenewa ndi ena kuphatikizapo ophunzira a Yesu anasunga umphumphu kwa Mulungu. Ndipo Yesu mwiniyo anapereka chitsanzo chachikulu koposa mwa kusunga umphumphu mwangwiro.

13. Kodi ndi mawu ati a Yesu onena za Satana amene atsimikizira kukhala owona?

13 Izi zimasonyeza kuti zimene Yesu adanena ponena za Satana kwa atsogoleri achipembedzo n’zowona kuti: “Tsopano mufuna kundipha ine, ndine munthu amene ndinalankhula ndi inu chowonadi chimene ndinamva kwa Mulungu. . . . Muli ochokera kwa atate wanu Mdyerekezi, ndipo zolakalaka zake za atate wanu mufuna kuchita. Iyeyu anali wambanda kuyambira pachiyambi, ndipo sanaima m’chowonadi, pakuti mwa iye mulibe chowonadi. Pamene alankhula bodza, alankhula za mwiniwake; pakuti ali wabodza, ndi atate wake wabodza.—Yohane 8:40, 44.

Kodi Chosankha Chanu N’chiyani?

14. Kodi n’chiyani chikuchitika patsopano lino kumaziko a dziko latsopano?

14 Maziko adziko latsopano amene akuyalidwa tsopano ndi Mulungu mumpangidwe wa chimangidwe cha mitundu yonse cha Mboni za Yehova akufikira kukhala olimba mowonjezerekawonjezereka. Chaka chilichonse zikwi mazana ambiri za anthu zikugwiritsira ntchito ufulu wawo wa kusankha wozikidwa pachidziŵitso cholongosoka, kuvomereza ulamuliro wa Mulungu. Iwo amakhala mbali yachimangidwe cha dziko latsopano, chomachirikiza mbali ya Mulungu ya nkhani yauchifumu wa chilengedwe chonse, ndi kutsimikizira Satana kukhala wabodza.

15. Kodi ndi ntchito yolekanitsa yotani imene ikuchitika m’tsiku lathu?

15 Mwakusankha ulamuliro wa Mulungu iwo adzayeneretsedwa kuikidwa ku “dzanja lamanja” la Kristu pamene akulekanitsa “nkhosa” ndi “mbuzi.” Muulosi wake wonena za masiku otsiriza Yesu ananeneratu kuti: “Adzasonkhanidwa pamaso pake anthu a mitundu yonse; ndipo iye adzalekanitsa iwo wina ndi mnzake, monga mbusa alekanitsa nkhosa ndi mbuzi; nadzakhalitsa nkhosa kudzanja lake lamanja, koma mbuzi kudzanja lamanzere.” Nkhosa ndiwo anthu odzichepetsa amene amasonkhana ndi kuchirikiza abale a Kristu, ogonjera kuulamuliro wa Mulungu. Mbuzi ndizo anthu aliuma amene amakana abale a Kristu ndipo samachita chilichonse kuchirikiza ulamuliro wa Mulungu. N’chotulukapo chotani? Yesu anati: “Amenewa [mbuzizo] adzachoka kumka ku chilango cha nthaŵi zonse, koma olungama [nkhosazo] kumoyo wanthaŵi zonse.”—Mateyu 25:31-46.

16. Kodi muyenera kuchitanji ngati mufuna kukhala ndi moyo m’Paradaiso alinkudza?

16 Ndithudi, Mulungu amatisamalira! Posachedwa adzapereka paradaiso wadziko lapansi wokondweretsa. Kodi inu mufuna kukhala ndi moyo m’Paradaiso ameneyo? Ngati mutero, sonyezani kuyamikira kwanu makonzedwe a Yehova mwa kuphunzira za Iye ndi kuchitapo kanthu pa zimene mukuphunzira. “Funani Yehova popezeka iye, itanani iye pamene ali pafupi; Woipa asiye njira yake, ndi munthu wosalungama asiye maganizo ake nabwere kwa Yehova; ndipo Yehova adzam’chitira chifundo.”—Yesaya 55:6, 7.

17. Kodi n’chifukwa ninji simuyenera kuzengeleza posankha amene mudzamtumikira?

17 Musazengeleze. Mapeto a dongosolo lakaleli la zinthu ayandikira kwambiri. Mawu a Mulungu amalangiza kuti: “Musakonde dziko lapansi, kapena za m’dziko lapansi. Ngati wina akonda dziko lapansi, chikondi cha atate sichiri mwa iye . . . Dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake; koma iye wakuchita chifuniro cha Mulungu akhala kunthaŵi yonse.”—1 Yohane 2:15-17.

18. Kodi ndi njira iti imene idzakukhozetsani kuyembekezera mwachidaliro kukhala ndi moyo m’dziko latsopano lokongola la Mulungu?

18 Anthu a Mulungu tsopano akuphunzitsidwa kaamba ka moyo wosatha m’dziko latsopano. Iwo akuphunzira maluso auzimu ndi maluso ena ofunika podzalima paradaiso. Tikulimbikitsani kusankha Mulungu monga wolamulira ndi kuchirikiza ntchito yopulumutsa moyo imene akuichititsa padziko lonse lapansi lerolino. Phunzirani Baibulo ndi Mboni za Yehova, ndipo fikani pakudziŵa Mulungu amene amasamaladi za inu ndi amene adzathetsa kuvutika. Mwanjira iyi inunso mungakhale mbali ya maziko adziko latsopano. Pamenepo mungathe mwachidaliro kuyembekezera kupeza chiyanjo cha Mulungu ndi kukhala ndi moyo kosatha m’dziko latsopano lokongola limenelo.

[Chithunzi patsamba 31]

Mboni za Yehova zili ndi ubale wowona wa m’mitundu yonse

[Chithunzi patsamba 32]

Maziko adziko latsopano la Mulungu akuyalidwa patsopano lino

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena