Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g91 2/8 tsamba 15-16
  • “Ndikuchifuna Tsopanoli!” Mbadwo Wofuna Kudzisangalatsa Pomwepo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Ndikuchifuna Tsopanoli!” Mbadwo Wofuna Kudzisangalatsa Pomwepo
  • Galamukani!—1991
  • Nkhani Yofanana
  • Dziko Losadziletsa
    Galamukani!—1991
  • “Simlandu Wanga!”—Mbadwo wa Kudzikhululukira
    Galamukani!—1991
  • N’chifukwa Chiyani Anthu Masiku Ano Sakumaleza Mtima?
    Galamukani!—2012
  • Ukamaudyerera Ubwana Wako
    Galamukani!—2003
Onani Zambiri
Galamukani!—1991
g91 2/8 tsamba 15-16

“Ndikuchifuna Tsopanoli!” Mbadwo Wofuna Kudzisangalatsa Pomwepo

Johnny wachichepere akuwoneka ngati wavutika kwambiri, koma inu kwakuvutani kuti mugwire pakamwa osaseka. Wakhwinyata, walobodoka mawondo, ndipo akuyenda modzikhwekhweretsa. Nkhope yake njachisoni—atachita tsinya pamphumi, napenya ndi diso lanjala, ndipo waŵisula mlomo wake. Iye akufuna chinthu chimodzi chokha: chakudya chotsekemera.

“Koma Amayi,” iye akunyonyola motero. Atonthola osawonjezera mawu ena. Amake amzazira, mbale ndi supuni ziri m’manja. “Usamavuta Johnny, ndati IYAYI!” iwo akutero mwaukali. “Ukadya chakudya chotsekemera tsopano, sudzachikonda chakudya chamadzulo. Ndipo kwangotsala mphindi 15 kuti tidye!”

“Koma ndikuifuna TSOPANOLI!” iye akulira. Amake akuleka kutakasa namtuzulira maso mwana wawo. Atatero mwanayo amadziŵa chomwe chidzatsatira; abwerera mochenjera, nakakhumata ali yekha m’chipinda chotsatira. Mosataya nthaŵi, acheutsidwa ndi zinthu zina naiŵaliratu za kudya pofika nthaŵi imene chakudya chakonzeka.

Ana nthaŵi zina amawoneka kukhala muukapolo m’kamphindi. Pamene akufuna chinthu chinachake, iwo amachifuna tsopanoli. Lingaliro lakuyembekezera mphotho yabwinopo, kapena kudzimana chisangalalo chifukwa chakuti chingawavulaze pambuyo pake, nlovuta kwambiri kwa iwo kulimvetsetsa. Komabe, ndilingaliro limene iwo—ndi tonsefe kwakukulukulu—tiyenera kuliphunzira.

Kufufuza kwaposachedwapa kochitidwa ndi asayansi pa Yunivesiti ya Columbia mu United States kunasanthula mphamvu ya ana aang’ono yakudzimana chisangalalo kaamba ka mphotho yokhumbiridwa. Anawo anapemphedwa kusankhapo pa mphatso ziŵiri, imodzi yokhumbirika kwambiri kuposa inayo—tinene kuti, apa bisiketi imodzi paja aŵiri. Iwo akalandira mphatso yabwinopo ngati akayembekezera kufikira pamene mphunzitsi atabwerako. Komabe, iwo akathetsa kuyembekezako panthaŵi iriyonse mwakuliza belu, komano akapatsidwa mphatso yocheperapo ndikumanidwa yaikuluyo. Asayansiwo analemba kachitidwe kawo ndikufufuza makulidwe a ana ameneŵa zaka khumi pambuyo pake.

Magazini a Science akusimba kuti ana amene anachedwetsa chisangalalo anachita bwinopo pa misinkhu yaunyamata. Iwo anali achipambano mokulira m’mayanjano ndi m’maphunziro ndipo anali okhoza bwino kupirira ndi chipsinjo ndi kugwiritsidwa mwala. Mwachiwonekere, mphamvu za kuchedwetsa chisangalalo—kudzimana chimene tikuchifuna—ndiluso lofunika kwambiri m’moyo. Ndipo limapindulitsa ngakhale akulu omwe.

Tonsefe timapanikizidwa tsiku lirilonse kusankha pakati pa chisangalalo cha panthaŵi yomweyo ndi chochedwetsedwa. Zosankha zina zingawonekere kukhala zazing’ono: ‘Kodi ndidye keke ija kapena ndichepetse macalorie anga?’ ‘Kodi ndipenyerere TV, kapena kodi pali chinachake chopindulitsa kwenikweni chimene ndiyenera kuchita tsopano lino?’ ‘Kodi ndiwayankhe mozaza kapena ndigwire lirime langa?’ M’chochitika chirichonse, tiyenera kupenda msampha wa kufuna chisangalalo cha panthaŵi yomweyo ndi ziyambukiro zofika patali. Nzowona kuti, izi sizingakhale nkhani zazikulu kwambiri.

Zazikulu kwambiri ndizo zosankha zamakhalidwe zimene anthu amayang’anizana nazo: ‘Kodi ndiname kuti ndipulumuke mkhalidwewu, kapena kodi ndipeze njira yochenjera yowona mtima?’ ‘Kodi ndikopedwe ndi kuthyatsiraku ndikuwona chimene chidzachitika, kapena kodi ndisamalire ukwati wanga?’ ‘Kodi ndigwirizane ndi gulu ndikusuta mbanje, kapena kodi ndimvere lamulo ndikutetezera thupi langa?’ Mosakaikira monga momwe mwawonera, njira yofuna chisangalalo chapanthaŵi yomweyo ingawononge moyo wa munthu mofulumira kwambiri.

Monga momwe magazini a Science akunenera: “Kuti agwire ntchito bwino, anthu ayenera kuimitsa modzifunira kudzisangalatsa kwapomwepo ndikumamatira pamkhalidwe wotsogozedwa ndi chonulirapo kaamba ka zotulukapo zamtsogolo.” Chotero mwinamwake tidzalephera kukhala ndi moyo wabwino ngati tidzafuna kukhutiritsa chikhumbo chathu chirichonse pompo.

Ngakhale kuli choncho, tikukhala m’dziko lokonda chisangalalo chapanthaŵi yomweyo, dziko lowonekera kukhala lotsogozedwa ndi mazana osaŵerengeka a anthu aakulu okhala ndi nzeru zofanana ndi za Johnny wachichepere, okhoterera pakufuna kupeza chimene akuchifuna tsopanoli, osalingalira zotulukapo. Mkhalidwe wawo ndiwo waumba dziko lathu lamakonoli, ndipo osati mwaubwino.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena