Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g91 2/8 tsamba 16-19
  • Dziko Losadziletsa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Dziko Losadziletsa
  • Galamukani!—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Ziyambukiro Zosonkhezera
  • Chida Cholimbanirana ndi Chikhotererocho
  • Kutsatira Zitsanzo Zabwino
  • “Ndikuchifuna Tsopanoli!” Mbadwo Wofuna Kudzisangalatsa Pomwepo
    Galamukani!—1991
  • Kodi Baibulo Limaletsa Kugonana?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • N’chifukwa Chiyani Anthu Masiku Ano Sakumaleza Mtima?
    Galamukani!—2012
  • Dziko Lopanda Upandu Layandikira!
    Galamukani!—1998
Onani Zambiri
Galamukani!—1991
g91 2/8 tsamba 16-19

Dziko Losadziletsa

Kulondola chisangalalo chapanthaŵi yomweyo kwa munthu kosakhazika mtima kwatulukapo kulephera kudziletsa. Talingalirani zitsanzo zoŵerengeka zokha:

Munthu ndi Malo Ake Okhala: Munthu akuwononga malo okhala. Zotulukapo zotsimikizirika kudza mtsogolo, zikulonjeza ngozi; komabe, zotulukapo zamwamsanga, zowononga chuma cha dziko lapansi ndi kuchita zochepa m’kuchepetsa kuipitsa zimatanthauza ndalama ponse paŵiri m’maindasitale ndi boma. Chotero kusakazako kukupitirizabe, mosasamala kanthu za kutsutsa kwa akatswiri ochirikiza malo okhala.

Chuma: Maiko apadziko lonse amabwereka ndalama zowonjezerekawonjezereka, akumaunjika ngongole kaamba kofuna kukwaniritsa pamenepo chuma chosoŵa. Iwo mopusa amatsutsa machenjezo apasadakhale operekedwa ndi akatswiri a zachuma—akuti chiwongola dzanja pangongole zonsezo chingakule pambuyo pake kukhala ngongole yosabwezeka kapena kuti chuma chadziko chozikidwa pa ngongole m’dziko lonse chimakhala cha moyo wamtombozi ndipo chingagwe ngati maiko osauka alephera kulipira ngongole zawo.

Makhalidwe: Ogwiritsira ntchito molakwa mankhwala ogodomalitsa ndi zakumwa zoledzeretsa, otchova njuga, apandu onse, achigololo, adama—kodi ndani angakane kuti onseŵa akuwonjezeka m’machitachita awo m’dziko lonse lerolino? Iwo ali gulu losakhazikika lokhala ndi chonulirapo chofanana: Akuchifuna icho TSOPANOLI! Kaya “icho” chikhale kugonana, ndalama, ulamuliro, kapena kokha kutchuka, ambiri ngofunitsitsa kuthetsa ukwati wawo, banja, chikumbumtima, chisungiko cha ndalama, thanzi, dzina labwino, ngakhale moyo, kaamba ka zisangalalo zofulumira zoterozo.

Sindiko kukuza mawu ndi m’kamwa kunena kuti dziko lamakono nlosadziletsa, lolamuliridwa ndi umbombo waukulu. Ena amalimbikira mowona mtima kutsutsa kusawoneratu zinthu pasadakhale kumene kwafalikira kwambiri m’dziko. Koma zolimba kwambiri ndi zosonkhezera zedi, ndizo magwero ododometsa kuwoneratu zinthu pasadakhale ndi kudziletsa mwa tonsefe.

Ziyambukiro Zosonkhezera

Munthu wamakono, makamaka m’maiko amaindasitale ambiri, wazingidwa mosalekeza ndi kusefukira kwa kusatsa zinthu kowulutsidwa. Kaya pa wailesi yakanema, wailesi, akanema, magazini, kapena manyuzipepala, chisangalalo chapanthaŵi yomweyo chimapititsidwa patsogolo mwaluso.

Kusatsa malonda kowulutsidwa panyuzi kumakukakamizani kuti gulani, gulani, gulani—ndikuti mufunsire makadi angongole kotero kuti mungagule tsopanoli, pomwepa, pomwepa. Zinthu zambiri zimagulitsidwa kokha palamya. ‘Musadere nkhaŵa pakali pano za kulipira!’ kumamveka mochonderera tero kusatsa malondako. Iko kwalinganizidwa kumveka ngati kuti sikwachinyengo chokopa malingaliro anu. Tsegulani tsamba m’magazini, ndipo funde la pefyumu liti guu kwa inu. Tsegulani wailesi, ndipo nyimbo yosatsira idzingolira m’maganizo anu kwamasiku. Tsegulani TV, ndipo zithunzithunzi zake zong’animang’anima zikukopani kukhala dwii pa iyo. M’nyimbo zamtundu wamalimba, zithunzithunzizo zimakometsedwa kwambiri mokhoza kukopa chisamaliro chanu chonse.

Wailesi yakanema imachita zoposa kusatsa malonda okhumba kudzisangalatsa kwapanthaŵi yomweyo. Iyo imakufalitsa. Mutangoitsegula, pomwepo mumachikulitsa chilakolako chofuna kusangalatsidwa. Kaŵirikaŵiri imasangalatsa mwakuwonetsa anthu zinthunzi zokhutiritsa chilakolako chawo. Munthu wandewu amatembenukira kuchiwawa pamene adani ake ‘achifunikira.’ Mwana wopulupudza amachititsa manyazi makolo ake ndi chiphwete chake chopusa. Achilakolako chachisembwere amagonja mosavuta ku chigololo kapena kugonana ukwati usanakhale. TV kaŵirikaŵiri simatsimikizira kusadziletsa kwa anthu oterowo; imawakometsera iwo, ikumawaphimba ndi ulemerero wosangalatsa kapena ndi chisangalalo cha kuseka kokhalapo.

Mofananamo, nkhani yaposachedwapa ya mu The Atlantic Monthly inanena kuti kanema ya Hollywood ya lerolino iri “chiwonetsero chimene chalinganizidwa mosamalitsa kwambiri kusangalatsa anthu m’mphindi iriyonse,” ndi “mafilimu ondondozana akumakupatsani lingaliro mobwerezabwereza lakuti, ‘Mungapenyerere onse!’” Zikuwonekera kuti, palibe chimene chimasangalatsa magulu openyerera lerolino kuposa chiwawa. Nkhaniyo ikunena kuti akanema kale “ankapondereza chikhumbo cha wopenyerera chofuna kudziphatikizamo m’ndewu,” pamene kuli kwakuti “mosiyana, chiwawa cha pakanema lerolino chimagwiritsiridwa ntchito kwakukulukulu kusonkhezera openyerera kuti alaŵe kupha, kumenya, kulemaza.” Kwenikweni, m’makanema mwachuluka kwambiri zochita ndi chiwawa kuposa kukambitsirana mchakuti ziwonetsero za lerolino nzazifupi ndi 25 peresenti m’kulemba kuposa za m’ma 1940, ngakhale kuti akanema enieniwo ngaatali mofanana.

Zipembedzo zadziko ziri m’malo abwino akuthandiza kuwonjola anthu ‘m’chisangalalo cha mphindi yomweyo’ chosokeretsa chimenechi. Komabe, atsogoleri achipembedzo ambiri nawonso akuwonekera kukhala omwerekera m’kufunafuna kwawo chisangalalo chapanthaŵiyo. Kodi timakuŵerenga mobwerezabwereza motani kufunafuna kwawo ulamuliro ndi chisonkhezero m’ndale zadziko, kapena kudzikondweretsa okha ndi nkhosa zawo zosokera mwakululuza miyezo yamakhalidwe abwino, kapena ngakhale kugwiritsira ntchito Baibulo monga chochinga chowalungamitsa chophimba zomwe amachita mwachinyengo mogwirizana ndi zikhumbo zawo? Mmalo movumbula chimene kudzisangalatsa kwapanthaŵi yomweyo kaŵirikaŵiri kumatanthauza—kuti ndi mbali ya msampha wa tchimo—iwo agwirizana ndi ‘atsogoleri ena amakhalidwe’ m’kufeŵetsa lingaliro la tchimo, kulisintha ndi mawu okhazika mtima onga akuti ‘ndimavuto achibadwa’ ndi akuti ‘ndinjira zina za moyo.’—Onani bokosi patsamba 20.

Chida Cholimbanirana ndi Chikhotererocho

Pokhala ndi mkhalidwe woterowo wadziko, kodi tingalimbane nawo motani? Kodi tingapange motani zosankha popanda kusokeretsedwa ndi msampha wa kudzisangulutsa kwapanthaŵi yomweyo? Yankho lingakudabwitseni: Baibulo lingathandize. Mosiyana ndi zimene anthu ambiri angalingalire, Baibulo silimatsutsa kusanguluka. Ilo silimapititsa patsogolo kudzivutitsa kapena kudzimana kopambanitsa. Mmalomwake, Baibulo limatiphunzitsa mmene tingakhalire ndi moyo wachimwemwe, ndi kuika kudzisangulutsa m’malo ake oyenerera.

Baibulo limalongosola Mlengi kukhala “Mulungu wachimwemwe,” amene ‘amakondwera m’ntchito zake.’ (1 Timoteo 1:11, NW; Salmo 104:31) Ponena za anthu, Mlaliki 3:1 amati: ‘Kanthu kalikonse kali ndi nthaŵi yake, ndi chofunika chirichonse cha pansi pa thambo chiri ndi mphindi yake.’ Mogwirizana ndi mavesi otsatira, ichi chimaphatikizapo mphindi yakuseka, mphindi yakulumphalumpha, mphindi yakukupatira, ndi mphindi yakukonda. Miyambo 5:18, 19 imakwezadi kukoma kwa chisangalalo chakugonana pakati pa mwamuna ndi mkazi pamene imauza mwamuna kuti: ‘Ukondwere ndi mkazi wokula naye.’ Chotero, mwachiwonekere, sichisangalalo chirichonse chomwe chiri cholakwika, ndiponso sizisangalalo zonse zimene ziyenera kukanidwa popanda chifukwa chenicheni. Komabe, kaŵirikaŵiri kudziletsa ndiko chipangizo chimene chimasoŵeka.—Agalatiya 5:22, 23.

Kusangalala kwathu tiyenera kukuika mmalo oyenera. Tifunikira kukhala ndi zolondola zoti zichitidwe choyamba. Kukondweretsa Mulungu kuyenera kukala patsogolo pa zisangalalo zathu zonse; kuyenera kukhala chinthu choyamba m’miyoyo yathu. Chotsatira ndicho chikondi chozikidwa pa lamulo lamakhalidwe abwino kaamba ka munthu mnzathu. (Mateyu 6:33; 22:36-40) Ngati timamkondadi Mulungu ndi mnansi wathu, pamenepo tidzakondwa kuika chisangalalo chathu pambuyo pa zofunika zoyambirira ziŵirizi.

Zinthu zoti zichitidwe choyamba zozikidwa pa Baibulo zidzatithandizanso kuchikana kotheratu chisangalalo pamene tifunikira kutero. Tidzatsutsa uchidakwa, chigololo, dama, kutchova njuga, umbombo, kugwiritsira molakwa mankhwala ogodomalitsa, ndi chiwawa. Lirilonse la machimoŵa limapereka chisangalalo chapanthaŵiyo mwanjira yake, koma iwo amakwiyitsa Mulungu ndikuvulaza munthu mnzathu. Malamulo a Mulungu otsutsa machimoŵa ali chizindikiro chotsimikizirika cha chikondi chake kwa ife, popeza kuti m’kupita kwa nthaŵi, tchimo limamlipiritsa koposa wochimwayo. Malipirowo angakhale nthenda, nyumba yosweka, kapena umphaŵi. Icho chingakhale chomalizira chonga imfa kapena changozi monga moyo woluluzika wosaphula kanthu.

Kutsatira Zitsanzo Zabwino

Mulungu amafuna kuti tidzitsogoza miyoyo yachimwemwe ndi yopindulitsa; Mawu ake ngodzaza ndi zitsanzo za amuna ndi akazi amene anatero. M’zochitika zambiri chikhulupiriro chawo ndi chikondi cha Mulungu zinawasonkhezera kuchedwetsa chisangalalo chawo. (Onani Ahebri, mutu 11.) Mose ali chitsanzo chotchuka pamfundoyi. Woleredwa monga mwana wa mwana wamkazi wa Farao mu Igupto wakale, iye anali ndi moyo wokhala ndi chisangalalo chomtsegukira. Ulamuliro, kutchuka, chuma, ndipo mosakaikira ndi mwaŵi wosaneneka wa kugonana zonsezo zikanakhala zake ngati anakhala m’banja la Farao. Mmalomwake, iye anasankha kuvutika ndi onyozeka, mtundu wa Israyeli wokhala muukapolo. Chifukwa ninji?

Ahebri 11:25 akuyankha kuti iye anasankha ‘kuchitidwa zoipa pamodzi ndi anthu a Mulungu, kosati kukhala nazo zokondweretsa za zoipa nthaŵi.’ Mose anawona tanthauzo la chisangalalo chapanthaŵi yomweyo. Chamwamsanga. Chosakhalitsa. Chomatha mofulumira. Chotero mmalo mosumika maganizo pazimene zikanambweretsera chisangalalo chapamphindi yomweyo, iye anasumika maganizo pakupeza chimwemwe chamtsogolo. Monga momwe Ahebri 11:26 amanenera kuti: ‘Anapenyerera chobwera cha mphotho.’ Mphotho imeneyo inali yeniyeni kwa iye, analinso tero Wopereka Mphothoyo. Vesi 27 imati: ‘Anapirira molimbika, monga ngati kuwona Wosawonekayo.’

Ena angaseke chosankha chimene Mose anachipanga. Ena anganene kuti iwo akanasankha chuma, ulamuliro, kutchuka. Koma talingalirani: Ngati Mose akanasankha njira ya kudzisangulutsa kwapanthaŵi yomweyo, kodi tikanadziŵa za iye lerolino? Kodi dzina lake la Chiigupto likanakhalapo lozokotedwa, pa miyala yosweka m’nyumba yosungiramo zinthu zakale, monga mfundo yobisika yodziŵika kokha kwa akatswiri ofukula za m’mabwinja oŵerengeka? Kapena, mwachiwonekere kwambiri, kodi ilo likanakhala lokwiriridwa ndikuiŵalidwa m’fumbi ndi mchenga kwa zaka mazana 34? Ndipo bwanji ponena za mphotho yake? Kodi Mose akanakhala wotsimikiza kukumbukiridwa ndi Yehova akanasankha njira yosavuta yodzikondweretsa yekha?

Dzina la Mose likukhala chisonkhezero kwa anthu mamiliyoni ambiri lerolino. Mtsogolo mwake m’motsimikizirika. Mtsogolo mwanu mungakhalenso motsimikizirika. Nanunso mungakhale magwero a chilimbikitso kwa ena. Pamene mupanga zosankha zanu m’moyo, kuyambira ku chachikulu mpaka ku chaching’ono, musapusitsidwe ndi manenanena adziko akuti muyenera kukhala nacho TSOPANOLI chimene mukuchifuna! Dzifunseni kuti, ‘Kodi chimene ndikuchifuna nchogwirizana ndi chimene Mlengi wanga akundifunira? Kodi kulondola chimene ndikuchifuna tsopanoli kudzatanthauza kukankhira kumbuyo zonulirapo zanga zauzimu? Kodi ndikudodometsa mphotho yanga mnjira iriyonse? Kodi ndikukhazikitsa chitsanzo chotani kwa anzanga ndi banja langa?’

Musasankhe ganizo ladziko lino lakusalingalira zinthu pasadakhale mmalo mwa nzeru ya Mulungu yowona patali. Musasinthanitse chimwemwe chokhalitsa ndi chisangalalo chosakhalitsa, kusinthanitsa chamuyaya ndi chapakanthaŵi. Ndiiko komwe, Mlengi wathu, amatipatsa chisangalalo mnjira yamtengo wosayerekezereka. Salmo 145:16 limatere ponena za iye: ‘Muwoloŵetsa dzanja lanu, nimukwaniritsa zamoyo zonse chokhumba chawo.’ Zina za zisangalalo zimenezi zimadza pomwepo; zina zimafunikira nthaŵi ndi kuleza mtima. Moyo muutumiki wa Yehova ngwodzala ndi chisangalalo—kukongola kwa chilengedwe, ukoma wokhala ndi mabwenzi, chisangalalo cha ntchito yotokosa ndi yopindulitsa, kukondwera kwa kuphunzira mayankho a mafunso a moyo ozizwitsa koposa. Pamwamba pa zonsezo, Mlengi akutipatsa moyo umene udzatisangalatsa kosatha.—Yohane 17:3.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena