Kodi Fodya Ngwabwino?
“B.A.T. [British American Tobacco] Uganda 1984 Ltd. siikukhulupirira kuti kusuta ndudu nkovulava thanzi.” Ndemanga imeneyi, yolembedwa m’kalata yopita ku Unduna wa Zaumoyo mu Entebbe, Uganda, yaputa mkwiyo m’Briteni pakati pa otsutsa malonda opanga zokaikitsa ndi miyezo yachinyengo. Chifukwa ninji?
Machenjezo aboma onena za thanzi amalembedwa pamapaketi a fodya m’maiko Akumadzulo kumene chizoloŵezi cha kusuta tsopano chikutsika ndi 1 peresenti pachaka. Komabe, m’maiko otukuka kumene, zofunikira zalamulo zoterozo kaŵirikaŵiri sizimakhalamo, ndipo kumene zimatero, sizimadziŵidwa ngati kuti osuta amagula ndudu zawo imodzi imodzi, mmalo mwa paketi. Malonda m’maiko amenewo akuwonjezeka ndi 2 peresenti pachaka. Koma chimenecho chiri kokha mbali ya vutolo. Fodya wokhala ndi utsi wamphamvu “womwe ngwaupandu kwambiri kwa iwo [maiko a ku Yuropu] kumsuta” amagulitsidwa ku Afirika ndi maiko ena otukuka kumene kuchokera ku Yuropu, akutero Dr. Roberto Masironi, mtsogoleri wa programu ya Fodya kapena Thanzi ya WHO (World Health Organization).
Malonda oipaŵa akupititsanso patsogolo ndudu zatsopano, zamphamvu kwambiri, ndi zotchipa. Mu Zimbabwe, kumene theka la chiŵerengero cha anthu ngapansi pa zaka 16 zakubadwa ndipo kulibe msinkhu woletsedwa kugula fodya, zikuwawopsa kuti ana achichepere adzamwerekera ndi chizoloŵezi chakusuta. Dr. Timothy Stamps, nduna ya zaumoyo m’Zimbabwe, wasonyezanso nkhaŵa ponena za “mauthenga onyengelera olunjikitsidwa kwa akazi achichepere” kuwakola nacho chikoka, chimene chikutchedwa “mankhwala ochangamutsa mofulumira koposa m’maiko Akumadzulo.” Polankhula pamsonkhano wa WHO, ofisala wamkulu wa zamankhwala m’Briteni anati: “Ndikulephera kumvetsetsa mmene aliyense akupititsirabe patsogolo chizoloŵezi chakupha chimenechi.”
Kodi nchifukwa ninji ndawala yowonjezera malondawo siikulephera chinkana kuti pali kutsutsa? Pali zifukwa zazikulu ziŵiri. Choyamba, itatero, ntchito zikwi zambiri mu indasitale ya fodya m’Yuropu zikatha. Chachiŵiri, iwo ndichuma m’maiko amene fodya amagulitsidwako. Mwachitsanzo, Kenya imapeza 5 peresenti kuchokera m’misonkho ndi mapindu pa kugulitsa fodya ya ndalama zonse zopezedwa ndi boma. Ndiponso chothandizira kukula kwa malonda a fodya ndicho ndalama zochirikiza maseŵera zimene makamphani a fodya amazipereka.
Pakali pano, mavuto a thanzi a ku maiko Akumadzulo akukwera m’maiko a mu Afirika. Pamene akupitiriza kulimbana ndi malungo ndi mliri wa matenda ambirimbiri akumaloko, akupeza kuti chuma chawo chikuthera pakulimbana ndi matenda ochititsidwa ndi kusuta.
Asia ali msika wotsatira kumene makampani afodya tsopano akutembenukira. Uku, malonda a fodya mwachiwonekere adzakwera pafupifupi ndi 18 peresenti m’zaka khumi zikudzazo. China ikuyembekezeredwa kuti potsirizira pake idzalandira fodya wa Kumadzulo. Zinadziŵika kale kuti 30 peresenti ya fodya wa padziko lonse akusutidwa ndi anthu a ku China. Katswiri wa kansa wa ku Briteni, Profesa Richard Peto akulosera kuti pa ana a ku China onse okhala ndi moyo lerolino, 50 miliyoni potsirizira pake adzafa ndi matenda ogwirizanitsidwa ndi fodya, ikusimba motero The Sunday Times ya ku London.
Mkhalidwe umodzi pakati pa yomwe imazindikiritsa Mboni za Yehova—zoposa mamiliyoni anayi padziko lonse—ngwakusagwiritsira ntchito fodya. Komabe, zambiri za izo kale ndudu siinkachoka pakamwa. Izo zinaleka pamene zinazindikira kuti kusuta sikumagwirizana ndi chikhulupiriro cha Chikristu. (Mateyu 22:39; 2 Akorinto 7:1) Ngati mufunadi kumasuka ku kumwerekera ndi fodya, funsani thandizo ndi chilangizo kwa mmodzi wa izo. Adzakhala wokondwa kukuthandizani.